1Mauwo adati, “Munthu iwe, imirira ndilankhule nawe.”
2Pamene ankalankhula, Mzimu wa Mulungu udaloŵa mwa ine nundiimiritsa, ndipo ndidamva Mulungu akulankhula.
3Adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, ndikukutuma kwa Israele, mtundu wa anthu aupandu amene andipandukira. Iwowo ndi makolo ao akhala akundichimwira mpaka lero lino.
4Anthu ake ndi okanika ndiponso achipongwe. Ndikukutuma kuti ukanene zimene Ine Ambuye Chauta ndikuŵauza.
5Ndiye popeza kuti iwowo ngaupandu, kaya akamvera kaya akakana, (pakuti ndi anthu opanduka) koma adzadziŵa ndithu kuti mneneri wafikadi pakati pao.
6Tsono iwe mwana wa munthu, usachite nawo mantha ndipo usaope zimene azikanena. Usachite mantha ngakhale minga ndi mkandankhuku zikuzinge ndipo ukukhala pakati pa zinkhanira. Komabe usaope mau ao ndipo usade nkhaŵa ndi mapenyedwe ao, chifukwa anthuwo ngaupandu.
7Popeza kuti iwowo ngaupandu, kaya akamvera kaya akakana, udzaŵauze ndithu mau anga.
8“Koma tsono iwe mwana wa munthu, umvere bwino zimene ndikukuuza. Usakhale waupandu ngati iwowo. Tsopano yasama, udye chimene ndikupatse.”
9Chiv. 5.1 Ine poyang'ana, ndidaona dzanja litaloza ine, litagwira mpukutu wolembedwa.
10Adaufunyulula nandiwonetsa. Mpukutu wonsewo unali wolembedwa kuseli nkuseri. Mau amene adaalembedwa m'menemo anali a za madandaulo, za maliro ndi za matemberero.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.