1Ndikulira mopemba kwa Mulungu,
ndi mau okweza ndikufuula kwa Mulungu kuti andimve.
2Pa tsiku lamavuto ndimafunafuna Ambuye.
Usiku wonse ndimakweza manja anga
ndi kupemphera kosalekeza.
Mtima wanga umakana kuusangalatsa.
3Ndikamalingalira za Mulungu,
ndimangobuula mumtima.
Ndikamasinkhasinkha za Iye,
ndimataya mtima.
4Mumagwira zikope zanga kuti ndisagone tulo.
Ndikuvutika kwambiri
kotero kuti sindingathe kulankhula.
5Ndimalingalira za masiku akale,
ndimakumbukira zaka zamakedzana.
6Ndimasinkhasinkha mumtima mwanga usiku.
Ndimadzifunsa ndi kufufuzafufuza mumtima mwanga.
7Ndimati,
“Kodi Ambuye adzandikana mpaka liti?
Kodi sadzandikomeranso mtima?
8Kodi chikondi chao chosasinthika chija chatheratu?
Kodi malonjezo ao aja atha mpaka muyaya?
9Kodi Mulungu waiŵala kukoma mtima kwake kuja?
Kodi wakwiya ndi kuleka chifundo chake chija?”
10“Chondiŵaŵa ndi chakuti,
Mulungu Wopambanazonse wasintha mchitidwe wake.”
11Komabe ndidzakumbukira ntchito zanu, Inu Chauta,
inde, ndidzakumbukira zodabwitsa zanu zakalekale.
12Ndidzasinkhasinkha za zonse zimene mwachita,
ndidzalingalira za ntchito zanu zamphamvuzo.
13Njira zanu, Inu Mulungu, nzoyera.
Kodi alipo mulungu winanso wamkulu ngati Mulungu wathu?
14Inu ndinu Mulungu amene mumachita zodabwitsa,
amene mwaonetsa mphamvu zanu pakati pa mitundu ya anthu.
15Mudaombola anthu anu ndi mkono wanu wamphamvu,
ndiye kuti ana a Yakobe ndi Yosefe.
16Pamene madzi adakuwonani, Inu Mulungu,
pamene madzi adakuwonani, adachita mantha,
inde, nyanja yakuya idanjenjemera.
17Mitambo idachucha madzi,
mumlengalenga mudachita bingu.
Zing'aning'ani mbali ndi mbali.
18Phokoso la bingu lanu lidamveka konsekonse,
mphezi zanu zidaŵalitsa dziko lonse,
dziko lapansi lidanjenjemera ndi kugwedezeka.
19Inu mudadzera pa nyanja,
njira yanu idadzera pa madzi akuya,
komabe mapazi anu sadaoneke.
20Mudatsogolera anthu anu ngati nkhosa
kudzera mwa Mose ndi Aroni.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.