Ahe. 5 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Mkulu wa ansembe aliyense amasankhidwa pakati pa anthu, namuika kuti aziŵaimirira pamaso pa Mulungu. Ntchito yake nkupereka mphatso ndi nsembe chifukwa cha machimo.

2Popeza kuti iye yemweyo ali ndi zofooka zambiri, ndiye kuti angathe kuŵalezera mtima amene ali opanda nzeru ndi osokera.

3Lev. 9.7 Nchifukwa chake aumirizidwa kumapereka nsembe chifukwa cha machimo a iye yemwe, ndiponso machimo a anthu ena.

4Eks. 28.1 Palibe munthu amadzitengera yekha ulemu wokhala mkulu wa ansembe onse, koma amachita kuitanidwa ndi Mulungu, monga momwe adaaitanidwira Aroni.

5 Mas. 2.7 Momwemonso Khristu sadadzikweze yekha ku ulemu wokhala mkulu wa ansembe onse, koma Mulungu ndiye adachita kumuuza kuti,

“Iwe ndiwe Mwana wanga,

Ine lero ndakubala.”

6 Mas. 110.4 Penanso Mulungu adati,

“Ndiwe wansembe mpaka muyaya,

unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.”

7 Mt. 26.36-46; Mk. 14.32-42; Lk. 22.39-46 Yesu, pa nthaŵi imene anali munthu pansi pano, mofuula ndi molira misozi, adapereka mapemphero ndi madandaulo kwa Mulungu, amene anali nazo mphamvu zompulumutsa ku imfa. Ndiye popeza kuti Yesu adaadzipereka modzichepetsa, Mulungu adamvera mapemphero ake.

8Motero Yesu, ngakhale anali Mwana wa Mulungu, adaphunzira kumvera pakumva zoŵaŵa.

9Atasanduka wangwiro kotheratu, adakhala gwero la chipulumutso chosatha kwa onse omvera Iye,

10ndipo Mulungu adamtchula mkulu wa ansembe onse, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.

Aŵachenjeza kuti asataye chikhulupiriro chao

11Tili ndi zambiri zoti nkunena pa zimenezi, koma nzovuta kufotokoza kwake, popeza kuti mwasanduka ouma mitu.

121Ako. 3.2Lija nkale mukadayenera kukhala ophunzitsa anzanu, komabe nkofunika kuti wina akuphunzitseninso maphunziro oyamba enieni a mau a Mulungu. Nkofunikanso kukumwetsani mkaka, m'malo mwa kukupatsani chakudya cholimba.

13Ngati wina aliyense angomwa mkaka, ndiye kuti akali mwana wakhanda, sangathe kutsata chiphunzitso chofotokoza za chilungamo.

14Koma chakudya cholimba ndi cha anthu okhwima. Pakugwiritsa ntchito nzeru zao, iwoŵa adadzizoloŵeza kusiyanitsa pakati pa zabwino ndi zoipa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help