1Chauta adandiwuza kuti, “Tenga cholemberapo chachikulu ndipo ulembepo ndi malembo odziŵika bwino kuti ‘KUSAKAZA-KWAMSANGA-KUFUNKHA-KOFULUMIRA.’ ”
2Tsono ndidapeza mboni zokhulupirika, wansembe Uriya ndiponso Zekariya mwana wa Yeberekiya, kuti andichitire umboni.
3Patapita nthaŵi mkazi wanga adaima, nabala mwana wamwamuna. Pamenepo Chauta adandiwuza kuti, “Umutche dzina lakuti KUSAKAZA-KWAMSANGA-KUFUNKHA-KOFULUMIRA.
4Pakuti mwanayo asanayambe kuitana kuti ‘Ababa’ kapena kuti ‘Amama’, chuma cha Damasiko ndi zofunkha za Samariya zidzatengedwa ndi mfumu ya ku Asiriya.”
Mfumu ya ku Asiriya ikubwera5Chauta adandiwuzanso kuti,
6“Anthu a dziko ili akana madzi anga a ku Siloamu oyenda mwachifatse, ndipo amakondwerera Rezini ndi mwana wa Remaliya.
7Nchifukwa chake Ine Ambuye ndidzaŵadzetsera mfumu ya ku Asiriya ndi ankhondo ake kuti adzathire nkhondo Yuda. Adzabwera ngati chigumula cha madzi a mtsinje wa Yufurate osefukira pa magombe ake onse.
8Adzaloŵa mwamphamvu m'dziko la Yuda, ndipo adzasefukira nadzapitirira mpaka kumayesa m'khosi. Adzachita ngati kutambasula mapiko ake ndi kuphimba dziko lako lonse, iwe Imanuele!”
9Sonkhanani mwamantha, inu mitundu ina ya anthu,
ndipo munjenjemere.
Mvetsetsani, inu maiko onse akutali.
Valani zankhondo, komabe mudzaonongedwa.
Inde, valanidi zankhondo, komabe mudzatha.
10Chitani upo, koma upowo sudzaphula kanthu.
Mupangane zochita, koma zidzalephereka,
pakuti Mulungu ali nafe.
Chauta achenjeza mneneri11Chauta adandilangiza mwamphamvu, ndipo adandichenjeza kuti ndisamayenda m'njira ya anthuŵa. Adati,
121Pet. 3.14, 15 “Usamachita nao zimene anthu ameneŵa amachita, ndipo usamaopa zimene iwowo amaopa, usachite nazo mantha.
13Chauta Wamphamvuzonse ndiye amene uyenera kumuwona kuti ndi woyera, ndiye amene uyenera kumuwopa, ndiye amene uyenera kuchita naye mantha,
141Pet. 2.8 ndiye adzakhala ngati malo opatulika. Koma kwa anthu a ku Yuda ndi a ku Israele adzakhala ngati mwala wokhumudwitsa, ndiponso ngati thanthwe logwetsetsa. Kwa anthu a mu Yerusalemu, adzakhala ngati msampha ndi khwekhwe.
15Ndipo anthu ambiri adzakhumudwapo. Adzagwa nadzathyokathyoka. Adzakodwa mu msampha ndi kugwidwa.”
Achenjeza opempha nzeru kwa mizimu16Manga bwino umboniwu ndipo umatepo chimatiro pa mau ameneŵa, pamaso pa ophunzira anga.
17Ahe. 2.13 Ndidzayembekeza Chauta amene akubisira fuko la Yakobe nkhope yake, ndipo ndidzaika chikhulupiriro changa mwa Iye.
18 Ahe. 2.13 Onani, ine ndi ana amene Chauta wandipatsa, ndife zizindikiro ndi zidziŵitso kwa Aisraele zofuma kwa Chauta Wamphamvuzonse amene amakhala pa phiri la Ziyoni.
19Tsono anthu akakuuzani kuti, “Kafunseni kwa olankhula ndi mizimu ndi kwa olosa amene amatulutsa liwu loti psepsepse ndi kumang'ung'udza.” Kodi anthu sayenera kupempha nzeru kwa milungu yao? Kodi sungapite kwa anthu akufa kukapemphera nzeru anthu amoyo,
20kuti akalandireko mau enieni ndi malangizo? Iyai, amene amalankhula motero, mwa iwo mulibe konse kuŵala.
Nthaŵi ya mavuto21Anthu adzayendayenda m'dziko movutika kwambiri ali ndi njala. Chifukwa cha njalayo, adzakalipa, ndipo adzayang'ana kumwamba ndi kutemberera mfumu yao ndi Mulungu wao.
22Koma akadzayang'ana pa dziko, adzangoona mavuto okhaokha ndi mdima woopsa ndi wodetsa nkhaŵa. Adzaponyedwa mu mdima wandiweyani.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.