1Ombani m'manja inu anthu a mitundu yonse.
Fuulani kwa Mulungu poimba nyimbo zachimwemwe.
2Paja Chauta Wopambanazonse, ndi woopsa,
ndiye mfumu yaikulu pa dziko lonse lapansi.
3Iye adatigonjetsera anthu ambirimbiri,
mitundu ina ya anthu adaiika pansi pa ulamuliro wathu.
4Adatisankhulira dzikoli kuti likhale choloĊµa chathu,
adatipatsa ife anthu a Yakobe dziko lokomali
pakuti amatikonda.
5Mulungu wakwera, anthu akumfuulira,
Chauta wakwera, akumuimbira lipenga.
6Imbani nyimbo zotamanda Mulungu,
imbani nyimbo zotamanda.
Imbani nyimbo zotamanda mfumu yathu,
imbani nyimbo zotamanda.
7Mulungu ndiye Mfumu ya dziko lonse lapansi.
Imbani mwaluso nyimbo zotamanda.
8Mulungu amalamulira mitundu ya anthu.
Mulungu amakhala pa mpando wake woyera waufumu.
9Atsogoleri a anthu a mitundu ina yonse amasonkhana
pamodzi ndi anthu a Mulungu wa Abrahamu,
pakuti mafumu onse a pansi pano ndi ake a Mulungu,
Iyeyo ndiye wamkulu kopambana.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.