Mphu. 47 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Natani

1 2Sam. 7.2, 3; 12.1 Atafa Samuele, padabwera Natani,

kuti akhale mneneri pa nthaŵi ya Davide.

Davide

2 1Sam. 17.34—18.7; 2Sam. 5.7; 8.1; 12.13 Monga momwe amapatulira mafuta pakati pa

zopereka za nsembe ya chiyanjano,

momwemonso Davide Ambuye adamsankhula pakati

pa Aisraele onse.

3Ankaseŵera ndi mikango ngati anaambuzi,

ndiponso ndi zimbalangondo ngati anaankhosa.

4Suja akali mnyamata adapha chiphona,

nachotsa manyazi a anthu ake,

pamene adaponya mwala ndi khwenengwe

nkugwetsa Goliyati wodzikuza uja.

5Ndiye kuti adapempha Ambuye Opambanazonse,

ndipo Iwo adalimbitsa dzanja lake lamanja

kuti aphe wankhondo wamphamvu uja,

ndi kutsimikiza mphamvu za anthu ake.

6Motero anthu adamtamanda ngati wogonjetsa

anthu 10,000.

Adamuyamika chifukwa cha madalitso amene

Ambuye adampatsa,

kenaka adamuveka chisoti chaufumu.

7Iye adagonjetsa adani ake onse ku mbali zonse,

naonongeratu mphamvu za Afilisti,

ndipo mpaka lero lino adaniwo alibenso mphamvu.

8Pa zonse zimene ankachita,

ankathokoza Woyera uja, Wopambanazonse uja.

Ankachita zimenezi ndi mau oyamika.

Ankaimba nyimbo ndi mtima wake wonse,

chifukwa ankakonda Mlengi wake.

9Adasankhula anthu oimba nyimbo ku guwa,

kuti aziimba nyimbo zokoma ndi zeze.

10Adakometsa masiku achikondwerero

nakhazikitsa mwambo wake pa nyengo ndi nyengo,

kotero kuti anthu ankatamanda dzina loyera la Ambuye.

Ndipo m'Nyumba ya Mulungu munkamveka mau oyamika

kuyambira m'maŵa mpaka madzulo.

11Ambuye adamkhululukira machimo ake,

ndipo adampatsa mphamvu zazikulu mpaka muyaya.

Adachita naye chipangano chaufumu

nampatsa mpando waufumu m'dziko la Israele.

Solomoni

12Pambuyo pa Davide, mwana wake wanzeru

adaloŵa ufumu.

Adakhazikika popanda zovuta, chifukwa cha

bambo wakeyo.

13 1Maf. 4.21-32 Solomoni adakhala mfumu pa nthaŵi ya mtendere,

ndipo Mulungu adapereka mtendere ponse pozungulira,

kuti athe kumanga Nyumba yolemekezeramo Mulungu,

malo opembedzeramo mpaka muyaya.

14Iwe Solomoni, unali wanzeru kwambiri pa nthaŵi

ya unyamata wako,

nzeru zako zinali zodzaza ngati mtsinje.

15Mbiri yako idadziŵika pa dziko lonse lapansi

ndipo udalidzaza ndi miyambi ndi mikuluŵiko.

16Dzina lako lidamveka mpaka ku zilumba zakutali,

ndipo anthu adakukonda chifukwa cha mtendere

wa pa ufumu wako.

17Nyimbo zako, malangizo ako, mafanizo ako,

ndiponso mau ako ofotokozera zobisika,

zonsezi anthu zinkaŵachititsa chidwi.

18 1Maf. 10.21, 27 M'dzina la Ambuye Mulungu,

Iye amene amatchedwa Mulungu wa Aisraele,

udakundika golide ngati chitini,

ndipo siliva udamsandutsa chinthu wamba ngati mtovu.

19 1Maf. 11.1 Koma udadzipereka wathunthu kwa akazi,

ndipo udasanduka kapolo wa zilakolako zako.

20Udaononga mbiri yako,

udaipitsa mtundu wako.

Udadzetsa tsoka pa ana ako

mwakuti adavutika chifukwa cha uchitsiru wako.

21 1Maf. 12.15-20 Ufumu udagaŵikana,

choncho ufumu wa Efuremu udapanduka.

22 2Sam. 7.15 Koma Ambuye sadaleke kukhala achifundo,

sadaononge zimene Iwo adapanga.

Sadaononge ana a wosankhidwa wao,

sadaononge zidzukulu za munthu amene ankamukonda.

Tsono adasunga otsala a Yakobe,

nasiyira Davide chiphukira chofumira mwa iye.

Rehobowamu ndi Yerobowamu

23 1Maf. 11.43; 12.10-30; 2Maf. 17.6, 18 Solomoni adakapumula ndi makolo ake,

nasiya mmodzi mwa ana ake kuti aloŵe

m'malo mwake.

Iyeyo anali Rehobowamu, munthu wopanda nzeru,

chipukupuku cha munthu,

amene anthu ake adampandukira chifukwa cha

mkhalidwe wake.

Panalinso Yerobowamu, mwana wa Nebati,

amene adachimwitsa Aisraele,

ndi kutsogoza Aefuremu pa njira yoipa.

24Machimo ao adachuluka kopitirira,

kotero kuti adaŵatulutsa m'dziko mwao.

25Chifukwa ankachitadi zoipa zamitundumitundu,

mpaka chilango chidaŵagwera.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help