Ezek. 38 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mlandu wa mfumu Gogi

1Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,

2Chiv. 20.8 “Iwe mwana wa munthu, udzudzule Gogi, wa ku dziko la Magogi, kalonga wamkulu wa mzinda wa Meseki ndi wa Tubala, ndipo umuimbe mlandu.

3Umuuze kuti Ine Ambuye Chauta, ndikuti, Ndikudana nawe, iwe Gogi, kalonga wamkulu wa ku Meseki ndi ku Tubala.

4Ndidzakuzunguza, ndidzakukola ndi mbedza m'kamwa mwako. Ndidzakutulutsira poyera, iweyo pamodzi ndi gulu lako lonse lankhondo, akavalo ndi okwerapo ake. Onsewo adzakhala atanyamula zishango ndi malihawo, malupanga ao ali osololasolola.

5Pamodzi ndi iwowo palinso asilikali a ku Persiya, ku Etiopiya ndi ku Puti. Onsewo ali ndi zishango ndi zisoti zankhondo.

6Palinso Gomeri ndi magulu ake onse ankhondo, banja la Togarima ndi gulu lake lankhondo lochokera kutali kumpoto. Palidi mitundu ya anthu ambiri imene ili nawe.

7“Konzekani, mukhale okonzeka ndithu, iweyo pamodzi ndi gulu lonse lankhondo limene lasonkhana mokuzungulira. Ndiwe amene udzaŵatsogolere pokamenya nkhondo.

8Ndidzakuitana patapita masiku ambiri. Zaka zikubwerazi, ndidzakuloŵetsa m'dziko lopulumuka ku nkhondo. Udzaŵapeza anthu atasonkhana kuchokera ku mitundu yambiri ya anthu, atakhazikika ku mapiri a Aisraele amene adaasiyidwa nthaŵi yaitali. Aisraelewo adaŵatulutsa pakati pa mitundu ya anthu, ndipo onsewo ali pa mtendere tsopano.

9Tsono iweyo ndi magulu ako ankhondo ndi mitundu yambiri ya anthu imene ili nawe, mudzabwera ngati mphepo yamkuntho. Mudzaphimba dziko lonse ngati mtambo.

10“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Pa tsiku limenelo mumtima mwako mudzaloŵa maganizo ofuna kukonzekera kuchita zoipa.

11Ndipo udzanena kuti, ‘Ndikukathira nkhondo dziko la midzi yopanda malinga. Ndipita kwa anthu amene amakhala mwamtendere, amene satchinjirizidwa ndi malinga kapena zitseko kapena mipiringidzo.

12Ndikukaŵalanda chuma chao ndi kufunkha zinthu zao. Ndikukathira nkhondo anthu okhala m'mizinda imene kale inali mabwinja. Ndidzalimbananso ndi anthu amene adasonkhana kuchokera ku maiko ambiri. Anthuwo ali ndi zoŵeta ndi katundu wochuluka, ndiponso amakhala pakatikati pa dziko lapansi.’

13Anthu a ku Sheba ndi ku Dedani, ndiponso amalonda a ku Tarisisi ndi midzi yake yonse, adzafunsa kuti, ‘Kodi kutereku, ukudzafunkha? Kodi wasonkhanitsa gulu lako lankhondo kudzanyamula zofunkha, kudzatenga siliva ndi golide, kudzalanda ziŵeto ndi katundu, kuti zikhale zofunkha zochuluka?’

14“Nchifukwa chake, iwe mwana wa munthu, ulalike ndipo uuze Gogi kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Pa nthaŵi imene anthu anga Aisraele adzakhale mwamtendere, udzanyamuka.

15Udzachokera kwanu ku mbali zakutali kumpoto, pamodzi ndi mitundu yambiri ya anthu, onsewo okwera pa akavalo, gulu lankhondo lalikulu ndi lamphamvu.

16Udzabwera kudzalimbana ndi anthu anga Aisraele, ngati namondwe woononga dziko lapansi. Masiku amenewo iwe Gogi ndidzakuyambanitsa ndi dziko langa kuti anthu a mitundu yonse adzandidziŵe, pamene ndidzaonetse kuyera kwanga pa zimene ndidzakuchite iweyo Gogi.

Mulungu adzalanga Gogi

17“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Kodi iwe si ndiwe amene ndidalankhula za iwe masiku amakedzana, kudzera mwa atumiki anga aneneri a ku Israele? Pa zaka zambiri iwo ankalengeza kuti ndidzautsa iwe kuti udzalimbane ndi Aisraele.

18Pa nthaŵi imeneyo, pamene Gogi adzabwera kudzalimbana ndi dziko la Israele, mkwiyo wanga udzayaka zedi. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.

19Chifukwa cha mkwiyo ndi ukali wanga woyakawo, ndikulumbira kuti kudzachita chivomezi chachikulu m'dziko lonse la Israele.

20Nsomba za m'nyanja ndi mbalame zamumlengalenga, nyama zakuthengo ndi zokwaŵa zonse, pamodzi ndi anthu onse okhala pa dziko lapansi, zonsezo zidzanjenjemera ndi mantha. Mapiri adzaphwanyika, magomo adzanyenyeka, ndipo makoma onse adzagwa pansi.

21Gogi ndidzamuutsira nkhondo kuchokera ku mapiri anga onse. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Anthu a Gogiyo adzaphana okhaokha ndi malupanga.

22Ndidzamulanga ndi mliri ndi imfa. Ndidzagwetsa mvula yoopsa ndi matalala ndiponso sulufure ndi miyala yamoto pa iye, pa magulu ake ankhondo ndiponso pa mitundu yonse ya anthu omperekeza.

23Umu ndimo m'mene ndidzaonetsere kuti ndine wamphamvu ndi woyera. Choncho ndidzadziŵika kwa anthu a mitundu yonse. Tsono adzadziŵadi kuti Ine ndine Chauta.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help