1Estere, atapemphera choncho masiku atatu, adaavula zovala zake zimene ankavala popembedza zija, nkuvala zina zokongola kwambiri.
2Atavala zokongola kwambiri choncho, adayambanso kupempha chithandizo kwa Mulungu ndi Mpulumutsi wake amene amaona zonse.
3Tsono adanyamuka pamodzi ndi adzakazi aŵiri, wina atamgwirira pa dzanja,
4wina akutsata pambuyo atagwirira zovala zake.
5Estere ankaoneka woŵala ndi wokongola kwambiri. Kunjaku ankaoneka wosangalala ngati wokondedwa, koma mumtima mwake anali ndi mantha oopsa.
6Adabzola zitseko zonse, nakaloŵa ku chipinda cha mfumu, nkukaima pamaso pake. Mfumu inali itakhala pa mpando wake waufumu, itavala zovala zake zonse zaufumu, golide ndi miyala yamtengowapatali zili kholophethe. Analidi wochititsa mantha kumpenya.
7Nkhope ya mfumu inali yaulemerero. Tsono mfumu idaŵeramuka nkuyang'ana Estere ndi maso aukali zedi. Pamenepo Estere m'nkhongono zii, nkhope nkudzati mbee, iye nkukomoka. Adayedzamitsa mutu wake pa mdzakazi wake womtsogolera uja.
8Koma Mulungu adafeŵetsa mtima wa mfumu. Idadzambatuka pa mpando wake, nkufungatira Estere m'manja mwake, mpaka pamene adatsitsimuka. Tsono idamlimbitsa mtima ndi mau ofatsa, nimufunsa kuti,
9“Kwagwanji, iwe Estere? Ndine mbale wako, usachite mantha.
10Iwe sungafe ai, lamulo lathu likukhalira anthu wamba okha.
11Sendera apa pafupi.”
12Pamenepo mfumu idagwira ndodo yake yaufumu ndi kuiika pa khosi la Estere, ndipo idamumpsompsona nimuuza kuti, “Tandiwuza zimene ukufuna.”
13Apo Estere adayankha kuti, “Poona inu, Mbuye wanga, ndinachita ngati ndikuwona mngelo wa Mulungu, ndipo mtima unachita kuti phwi chifukwa cha ulemerero wanu.
14Ndithu ndinu ochititsa chidwi kwambiri, mbuye wanga, ndipo maonekedwe anu ngokoma kwabasi.”
15Koma Estere akulankhula choncho, adakomokanso.
16Pamenepo mfumu idavutika kwambiri, ndipo atumiki ake onse nawonso adayesa kumlimbitsa mtima Estere.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.