Chiv. 9 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Pamenepo mngelo wachisanu adaliza lipenga lake. Atatero ndidaona nyenyezi itagwa pansi kuchokera ku thambo. Idapatsidwa kiyi ya dzenje lopita ku Chiphompho chakuya.

2Gen. 19.28; 2Es. 7.36Nyenyeziyo idatsekula padzenjepo, ndipo padatuluka utsi wonga wam'ching'anjo. Dzuŵa ndi thambo zidada chifukwa cha utsi wotuluka m'dzenjewo.

3Eks. 10.12-15; Lun. 16.9Muutsimo mudatuluka dzombe kukaloŵa m'dziko lapansi, ndipo dzombelo lidapatsidwa mphamvu zoluma zonga za zinkhanira za pa dziko lapansi.

4Ezek. 9.4Dzombelo lidalamulidwa kuti lisaononge udzu wa pa dziko lapansi, kapena chomera chilichonse, kapena mtengo uliwonse. Lidaloledwa kungoononga anthu opanda chizindikiro cha Mulungu chija pamphumi pao.

5Silidaloledwe kuŵapha, koma kungoŵazunza pa miyezi isanu. Kuŵaŵa kwake kwa mazunzowo kunkalingana ndi ululu wa chinkhanira chikaluma munthu.

6Yob. 3.21; Yer. 8.3Masiku amenewo anthuwo adzafunafuna imfa, koma osaipeza. Adzafunitsitsa kufa, koma imfa izidzaŵathaŵa.

7 Yow. 2.4 Dzombelo linkaoneka ngati akavalo okonzekera nkhondo. Pamitu pake panali ngati zisoti zaufumu zagolide, nkhope zake ngati za anthu.

8Yow. 1.6Tsitsi lake linali litalilitali ngati la azimai, mano ake ngati a mkango.

9Yow. 2.5Pachifuwa pake panali mamba onga ngati malaya achitsulo apachifuwa. Kulira kwa mapiko ake kunali ngati kwa magareta ankhondo ambiri okokedwa ndi akavalo othamangira ku nkhondo.

10Dzombelo lili ndi michira ngati zinkhanira, ndipo lili ndi mbola. Mphamvu yake ija yopwetekera anthu pa miyezi isanu inali kumichira kwake.

11Mfumu yake inali mngelo wolamulira Chiphompho chija. Pa Chiyuda dzina lake ndi Abadoni, pa Chigriki ndi Apoliyoni (tanthauzo lake ndiye kuti, “Woononga uja”.)

12Tsoka loyamba lija lapita. Atsalabe masoka enanso aŵiri oyenera kubwera.

13 Eks. 30.1-3 Mngelo wachisanu ndi chimodzi adaliza lipenga lake. Atatero ndidamva liwu lochokera ku ngodya zinai za guwa lagolide lija lokhala pamaso pa Mulungu.

14Liwulo lidauza mngelo wachisanu ndi chimodzi wokhala ndi lipenga uja, kunena kuti, “Amasule angelo anai aja amene ali omangidwa pa mtsinje waukulu wa Yufurate.”

15Adaŵamasuladi angelowo kuti akaphe chimodzi mwa zigawo zitatu za anthu onse. Angelowo Mulungu anali ataŵakonzera ora lake, tsiku lake, mwezi wake ndi chaka chake.

16Ndidamva chiŵerengero cha ankhondo a pa akavalo aja, kuti chinali mamiliyoni 200.

17Lun. 11.17, 18M'masomphenya momwemo, akavalowo ndidaŵaona motere: okwerapo ake adaavala malaya achitsulo apachifuwa a maonekedwe ofiira ngati moto, obiriŵira ngati utsi, ndi achikasu ngati miyala ya sulufure. Mitu ya akavalowo inali ngati ya mikango, ndipo m'kamwa mwao munkatuluka moto, utsi ndi sulufure.

18Chimodzi mwa zigawo zitatu za anthu onse chidaphedwa ndi miliri itatu iyi: wa moto, wa utsi ndi wa sulufure, zimene zinkatuluka m'kamwa mwa akavalo aja.

19Akavalowo mphamvu zao zinali m'kamwa ndi ku michira. Michira yaoyo inali ngati njoka, yokhala ndi mitu yopwetekera anthu.

20 Mas. 115.4-7; 135.15-17; Dan. 5.23 Anthu ena onse otsala, amene sadaphedwe ndi miliri ija, sadatembenuke mtima kuti asiye ntchito za manja ao. Sadaleke kupembedza mizimu yoipa, ndi mafano agolide, asiliva, amkuŵa, ndi amtengo, amene sangathe kupenya, kapena kumva, kapena kuyenda.

21Anthuwo sadatembenukenso kuti aleke kupha anzao, ufiti, dama ndi kuba.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help