Eks. 5 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mose ndi Aroni akumana ndi Farao

1Pambuyo pake Mose ndi Aroni adapita kwa Farao nakamuuza kuti, “Naŵa mau a Chauta, Mulungu wa Aisraele, akunena kuti, ‘Uŵalole anthu anga apite ku chipululu, kuti akachite mwambo wachipembedzo wondilemekeza Ine.’ ”

2Farao adayankha kuti, “Kodi Chautayo ndani kuti ine nkumvera zimenezo ndi kuŵalola Aisraele kuti apite? Chautayo sindimdziŵa, ndipo sindidzalola konse kuti Aisraele apite.”

3Koma iwo adamuuza kuti, “Mulungu wa Ahebri adalankhula nafe. Chonde tiloleni kuti tipite ku chipululu ulendo wa masiku atatu, kuti tikapereke nsembe kwa Chauta, Mulungu wathu. Tikapanda kupita adzatipha ndi matenda kapena nkhondo.”

4Koma mfumu ya ku Ejipito ija idafunsa Mose ndi Aroni kuti, “Chifukwa chiyani mukuŵasiyitsa ntchito yao Aisraele? Chokani apa, bwererani ku ntchito yanu.”

5Farao adapitirira kuŵauza kuti, “Anthu ameneŵa akuchulukana kwambiri tsopano. Bwanji inu mufuna kuŵaletsa kugwira ntchito yao?”

6Motero pa tsiku limenelo Farao adalamula akuluakulu a thangata, pamodzi ndi akapitao achiisraele kuti,

7“Musaŵapatsenso udzu wa njerwa anthu ameneŵa, monga muja munkachitiramu. Alekeni azikamweta okha udzuwo.

8Koma chiŵerengero cha njerwa chikhale chonchija, monga momwe ankaumbira kale. Musaŵachepetsere ndi pang'ono pomwe, ngaulesi ameneŵa. Nchifukwa chake akulira nkumati, ‘Tiyeni tikapereke nsembe kwa Mulungu wathu.’

9Muŵagwiritse ntchito yakalavulagaga anthu ameneŵa, kuti azitanganidwa ndi ntchito m'malo momangomvera zabodza.”

10Akuluakulu a thangata ndi akapitao Achiisraele adapita kukaŵauza anthu kuti, “Farao wanena kuti, ‘Sindidzakupatsaninso udzu.

11Muzidzimwetera nokha kulikonse komwe mungaupeze. Koma chiŵerengero cha njerwa ndi chonchija.’ ”

12Motero anthu aja adamwazikira m'dziko lonse la Ejipito kukafunafuna udzuwo.

13Akulu a Farao aja ogwiritsa ntchito, adafulumizitsa Aisraele naŵauza kuti, “Muziwumba chiŵerengero chonchija cha njerwa pa tsiku, monga munkachitira pamene ankakupatsani udzu.”

14Akuluakulu a thangata a Farao aja ankamenyanso akapitao Achiisraele amene adaŵaika kuti akhale omayang'anira ntchito, namaŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani lero simudaumbe chiŵerengero chonchija cha njerwa monga munkachitira kale?”

15Tsono akapitao achiisraele aja adapita kwa Farao kukadandaula kuti, “Pepani amfumu, kaya chifukwa chiyani mwatichita zotere ife atumiki anu?

16Udzu satipatsanso ife, bwana, komabe akutilamula kuti, ‘Kaziwumbani njerwa!’ Ndiponso akungotimenya. Anthu anu akulakwa.”

17Farao adaŵayankha anthuwo kuti, “Ndinu alesi inu, alesi zedi, nchifukwa chake mukuti, ‘Tiyeni tipite tikapereke nsembe kwa Chauta.’

18Chokani apa, bwererani ku ntchito yanu. Udzu asakupatseni, koma chiŵerengero cha njerwa ndi chonchija ndithu basi.”

19Akapitao achiisraele aja adaona kuti alidi pa mavuto, ataŵauza kuti, “Muziwumba chiŵerengero chonchija cha njerwa tsiku ndi tsiku.”

20Tsono atachoka kwa Farao kuja, adakumana ndi Mose ndi Aroni amene ankaŵadikira,

21ndipo adaŵauza kuti, “Chauta aone mwachitazi, ndipo akuweruzeni inu poti Farao ndi nduna zake mwaŵasandutsa adani athu. Inuyo ndinu amene mwaika lupanga m'manja mwao kuti atiphe ife.”

Mose adandaula kwa Chauta

22Choncho Mose adapemphera kwa Chauta nati, “Inu Chauta, chifukwa chiyani mukuzunza anthu anu? Nanga ine mudanditumiranji?

23Chipitire changa chija kwa Farao kukamuuza mau anu aja, wakhala akuzunzabe anthu anu. Ndipo Inu simudachitepo kanthu konse kuti muŵaombole anthu anu.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help