1Nthaŵi ina kudzakhala mfumu ina
yolamulira mwaungwiro,
ndiponso nduna zina zoweruza mwachilungamo.
2Aliyense mwa iwo adzakhala ngati
pothaŵirapo mphepo ndi malo obisalirapo namondwe.
Adzakhala ngati mitsinje yoyenda m'dziko louma,
ndipo ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu m'chipululu.
3Maso a anthu openya sadzakhalanso otseka,
ndipo makutu a anthu akumva adzakhala otchera.
4Anthu a mtima waphamphu
adzadziŵa kuchita zinthu moganiza bwino,
ndipo anthu achibwibwi
adzalankhula mosadodoma ndi momveka.
5Chitsiru sichidzalandira ulemu,
ndipo munthu woipa sadzalemekezeka.
6Munthu wopusa amalankhula zauchitsilu,
ndipo amaganiza kuchita zoipa.
Amachita zoipira Mulungu,
amalankhula zonyoza Mulungu.
Anjala saŵapatsa chakudya,
aludzu saŵapatsa chakumwa.
7Munthu wachabechabe njira zake nzoipa.
Amalingalira zaupandu kuti aŵachite chiwembu
anthu osauka pakuŵanamizira,
ngakhale pamene osaukawo ali osalakwa konse.
8Koma munthu wa mtima wabwino
amalingalira zabwino,
ndipo amalimbikira kuchita zabwino.
Chenjezo kwa akazi osasamala9Tatiyeni, inu akazi aulesi, mumve mau anga.
Inu akazi odzitama, imvani zimene ndikulankhula.
10Pakapita chaka ndi masiku pang'ono,
mudzanjenjemera inu akazi amatama,
chifukwa mitengo ya mphesa idzakanika,
zipatsonso sizidzaoneka.
11Dederani inu akazi aulesi,
njenjemerani, inu odzikhulupirira udyo.
Vulani zovala, ndipo muvale nsanza m'chiwuno.
12Dzimenyeni pa chifuŵa mwachisoni,
chifukwa minda yachonde ndi yamphesa yaonongeka,
13ndipo minga ndi mkandankhuku
zikumera pa dziko la anthu anga.
Ndithu, mulire nyumba zonse
zimene ankakhalamo mosangalala,
ndiponso mzinda umene udaali ndi chimwemwe.
14Nyumba yaufumu idzasiyidwa,
ndipo mzinda wonse udzakhala wopanda anthu.
Malinga ake ndi nsanja yomwe
zidzasanduka mapanga mpaka muyaya.
Abulu akuthengo adzasangalala kumeneko,
ndipo ziŵeto zidzapeza busa komweko.
15Koma Mulungu adzatitumizira mzimu wake,
kuchokera kumwamba,
ndipo dziko lachipululu lidzasanduka lachonde,
minda yonse idzabereka dzinthu dzambiri.
16Pamenepo m'dziko lonse mudzakhala chilungamo,
kuyambira ku chipululu mpaka ku minda yachonde.
17Chifukwa anthu onse akamachita zachilungamo,
m'dziko mudzakhala mtendere ndi bata mpaka muyaya.
18Anthu a Mulungu adzakhala m'midzi yamtendere,
m'nyumba zokhulupirika, ndiponso m'malo ousira abata.
19Komabe nkhalango idzaonongedwa ndi matalala,
ndipo mzinda udzagwetsedwa mpaka pansi.
20Anthu adzakondwa kwambiri
chifukwa adzakhala ndi madzi ambiri,
ndipo abulu ndi ng'ombe zao azidzadya paliponse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.