1Mose ankaŵeta ziŵeto za mpongozi wake Yetero, wansembe uja wa ku Midiyani. Tsiku lina adatenga ziŵetozo, nayenda nazo cha kuzambwe kwa chipululu, mpaka kukafika ku phiri la Mulungu dzina lake Horebu.
2 Aisraelewo ukaŵauze kuti, NDILIPO wandituma kwa inu.”
15Ndipo Mulungu adamuuzanso Mose kuti, “Aisraele ukaŵauze kuti, Chauta, Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, Mulungu wa Yakobe, ndiye amene wandituma kwa inu. Tsono limeneli ndilo dzina langa mpaka muyaya. Limeneli ndilo dzina limene idzanditchula mibadwo yonse yam'tsogolo.
16Pita ukaŵasonkhanitse atsogoleri onse a Aisraele, ukaŵauze kuti, Chauta, Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Yakobe, adandiwonekera; adandilamula kuti ndikuuzeni kuti wabwera kwa inu, ndipo zonse zimene akukuchitani Aejipito, waziwona.
17Mulungu watsimikiza kuti adzakutulutsani ku Ejipito kuno kumene mukuzunzika, ndipo adzakuloŵetsani m'dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi. Dzikolo ndi lamwanaalirenji.”
18Mulungu adapitirira kunena kuti, “Zimene ukaŵauzezo, adzamva. Ndiye mukapite kwa mfumu ya ku Ejipito, iwe ndi atsogoleri a Aisraelewo, ndipo mfumuyo mukaiwuze kuti, ‘Chauta, Mulungu wa Ahebri, adakumana nafe. Tsono tikukupemphani, mutilole kuti tipite ulendo wa masiku atatu ku chipululu, kuti tikapereke nsembe kwa Chauta, Mulungu wathu.’
19Kudziŵa ndikudziŵa kuti mfumu ya ku Ejipitoyo sidzakulolani kuti mupite, mpaka nditaikakamiza kutero.
20Tsono Ine ndidzagwiritsa ntchito mphamvu zanga ndipo ndidzalanga Ejipito ndi zozizwitsa zomwe ndidzachite kumeneko. Zikadzachitika zimenezo, adzakulolani.
21Eks. 12.35, 36
Lun. 10.17Aejipito ndidzaŵafeŵetsa mtima pa anthu anga, kotero kuti pamene muzidzachoka, simudzapita chimanjamanja.22Mkazi aliyense adzapempha Mwejipito woyandikana naye ndiponso amene amakhala naye m'nyumba, kuti ampatse zinthu zodzikongoletsera zasiliva ndi zagolide, ndiponso zovala. Zimenezi mudzaveka ana anu aamuna ndi aakazi, motero mudzaŵalanda zonse Aejipitowo.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.