Ahe. 10 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Malamulo a Mose ndi chithunzi chabe cha madalitso amene alikudza, osati madalitso enieniwo. Ngakhale nsembe zimodzimodzi zimaperekedwa kosalekeza chaka ndi chaka, Malamulowo sangathe konse mwa nsembezo kuŵasandutsa angwiro anthu oyandikira pamenepo.

2Anthu opembedza Mulungu aja akadayeretsedwa kwathunthu, sibwenzi mtima wao ukuŵatsutsabe, ndipo akadaleka kumapereka nsembe.

3Koma monga zilirimu, nsembezo zimakumbutsa anthu za machimo ao chaka ndi chaka.

4Magazi a ng'ombe zamphongo ndi a atonde sangathe konse kuchotsa machimo.

5 Mas. 40.6-8 Nchifukwa chake pamene Khristu adadza pansi pano, adati,

“Inu Mulungu simudafune nsembe kapena zopereka,

koma thupi mudandikonzera.

6Nsembe zoocha kwathunthu

ndi nsembe zoperekera machimo,

simudakondwere nazo.

7Tsono ine ndidati,

‘Inu Mulungu, ndabweratu

kuti ndichite zimene mukufuna,

paja zidalembedwa choncho

ponena za Ine m'buku la Malamulo.’ ”

8Motero poyamba adati, “Nsembe kapena zopereka, nsembe zopsereza kwathunthu kapenanso nsembe zoperekera machimo, simudazifune ndipo simudakondwere nazo.” Zimenezi nzimene Malamulo adaanena kuti ziperekedwe.

9Koma pambuyo pake adati, “Ndabweratu, kuti ndichite zimene mukufuna.” Motero Khristu adathetsa mphamvu za nsembe za mtundu woyamba zija, kuti m'malo mwake akhazikitse nsembe ya mtundu wachiŵiriyo.

10Chifukwa chakuti Yesu Khristu adachita zimene Mulungu adaafuna kuti achite, ife tidayeretsedwa ndi nsembe ya thupi lake, limene Iye adapereka kamodzi kokhako.

11 Eks. 29.38 Wansembe aliyense amaimirira tsiku ndi tsiku nkumatumikira, ndipo amapereka nsembe imodzimodzi mobwerezabwereza. Komabe nsembe zimenezi sizingathe konse kuchotsa machimo.

12Mas. 110.1 Koma Khristu adapereka nsembe imodzi yokha yochotsera machimo onse. Ndipo ataipereka, adakakhala ku dzanja lamanja la Mulungu.

13Kumeneko akudikira tsono kuti Mulungu asandutse adani ake kukhala ngati chopondapo mapazi ake.

14Mwa nsembe imodzi yomweyo wasandutsa angwiro kwamuyaya onse amene Iye akuŵayeretsa.

15Mzimu Woyera nayenso amatitsimikizira zimenezi. Poyamba Iye akuti,

16 Yer. 31.33 “Nachi chipangano chimene ndidzachita nawo

atapita masiku amenewo, akutero Ambuye:

ndidzaika Malamulo anga m'mitima mwao,

ndidzachita kuŵalemba m'maganizo ao.”

17 Yer. 31.34 Pambuyo pake akutinso, “Sindidzaŵakumbukiranso konse machimo ao ndi zolakwa zao.”

18Pamene Mulungu wakhululukira zonsezi, sipafunikanso nsembe yoperekera machimo.

Tiyandikire kwa Mulungu ndi kulimbika m'chikhulupiriro

19Motero tsono, abale, timayembekeza mosakayika konse kuloŵa m'Malo Opatulika Kopambana chifukwa cha imfa ya Yesu.

20Iye adatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo yobzola chochinga, chimene chili thupi lake.

21Ndiponso tili ndi Wansembe wamkulu woyang'anira nyumba ya Mulungu.

22Lev. 8.30; Ezek. 36.25Nchifukwa chake tsono, tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona, tili ndi chitsimikizo cha chikhulupiriro. Timuyandikire ndi mitima yoyeretsedwa, yopanda kalikonse koitsutsa, ndiponso ndi matupi osambitsidwa ndi madzi oyera.

23Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.

24Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino.

25Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.

26Pakuti tikamachimwirachimwira mwadala, kwina tikudziŵa choona, palibenso nsembe ina iliyonse ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo.

27Yes. 26.11 Pamenepo chotitsalira si china ai, koma kumangodikira ndi mantha chiweruzo, ndiponso moto woopsa umene udzaononga otsutsana ndi Mulungu.

28Deut. 17.6; 19.15 Munthu wophwanya Malamulo a Mose amaphedwa popanda nchifundo chomwe, malinga pakakhala mboni ziŵiri kapena zitatu.

29Eks. 24.8 Nanji tsono munthu wonyoza Mwana wa Mulungu, munthu woyesa chinthu chachabe magazi achipangano amene adamuyeretsa, munthu wonyoza Mzimu wotipatsa madalitso a Mulungu! Chilango cha munthu wotere chidzakhala choopsa kopambana.

30Deut. 32.35; Deut. 32.36 Paja tikumdziŵa kale amene adati, “Kulipsira nkwanga, ndidzakhaulitsa ndine.” Adatinso, “Ambuye adzaweruza anthu ake.”

31Kugwa m'manja mwa Mulungu wamoyo ndi chinthu choopsa.

32Kumbukirani masiku akale aja mutangolandira kuŵala chatsopano. Pa nthaŵi imene ija mudaalimbana ndi mazunzo ambiri.

33Mwina ankakunyozani ndi kukuchitani chipongwe, anthu akuwonerera. Mwinanso munkamva nawo zoŵaŵa amene ankasautsidwa motero.

34Munkasaukira limodzi ndi amene adaaponyedwa m'ndende, ndipo mudalola mokondwa kuti alande chuma chanu, mutadziŵa kuti muli ndi chuma choposa ndi chosatha.

35Tsono musataye kulimba mtima kwanu, pakuti kumabweretsa mphotho yaikulu.

36Pafunikadi kupirira, kuti muchite zimene Mulungu akufuna, kuti motero mukalandire zimene adalonjeza.

37Hab. 2.3, 4 Paja Malembo akuti,

“Pangotsala kanthaŵi pang'ono chabe

kuti Iye amene alikudza, afike.

Sachedwa ai.

38Wolungama wanga adzakhala ndi moyo pakukhulupirira.

Koma akamachita mantha nkubwerera m'mbuyo,

Ine sindikondwera naye.”

39Ifetu sindife anthu oti nkumabwerera m'mbuyo ndi kutayika ai, ndife anthu okhulupirira, kuti tipulumuke.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help