1Pa mwezi wa Nisani, chaka cha 20 cha ufumu wa Arita-kisereksesi, pamene adabwera ndi vinyo pamaso pa mfumuyo, ndidatenga vinyoyo ndi kumpereka kwa mfumu. Tsono nkale lonse sindidakhalepo ndi nkhope yachisoni pamaso pake.
2Apo mfumu idandifunsa kuti, “Kodi bwanji nkhope yako ili yakugwa, pamene sukudwala? Chimenechi si china, koma ndi chisoni chamumtima.” Pamenepo ndidaopa kwambiri.
32Maf. 25.8-10; 2Mbi. 36.19; Yer. 52.12-14 Ndidauza mfumu kuti, “Amfumu akhale ndi moyo mpakampaka. Ilekerenji nkhope yanga kukhala yakugwa, pamene mzinda kumene kuli manda a makolo anga, adani adausandutsa bwinja, ndipo zipata zake adazitentha ndi moto?”
4Tsono mfumu idandifunsa kuti, “Tsono umati undipemphe chiyani?” Pamenepo ndidapemphera kwa Mulungu Wakumwamba.
5Ndipo ndidaiwuza mfumuyo kuti, “Ngati chingakukondweretseni amfumu, ndipo ngati mungandikomere mtima mtumiki wanune, munditume ku Yuda, kumzinda kumene kuli manda a makolo anga, kuti ndikaumangenso mzindawo.”
6Apo mfumu, mkazi wake ali pambali pake, idandifunsa kuti, “Kodi kumeneko ukakhalako nthaŵi yaitali bwanji, ndipo udzabwerako liti?” Ndidaiwuza nthaŵi yake, ndipo idandilola kuti ndipite.
7Tsono ndidauza mfumu kuti, “Ngati chingakukondweretseni amfumu, mundipatse makalata oti ndikapereke kwa abwanamkubwa a chigawo cha Patsidya pa Yufurate, kuti akandilole kudzera m'chigawocho mpaka ndikafike ku Yuda.
8Mundipatsenso kalata ina yolembera Asafu, kapitao woyang'anira nkhalango ya mfumu, kuti akandipatse mitengo yokamangira mitanda ya zipata za linga loteteza Nyumba ya Mulungu, ya makoma a mzinda, ndiponso ya nyumba yokakhalamo ine.” Mfumu idandipatsa zimene ndidaapemphazo, popeza kuti Mulungu wanga wokoma mtima anali nane.
9Choncho ndidanyamuka ulendo nkukafika kwa abwanamkubwa a chigawo cha Patsidya pa Yufurate, ndipo ndidaŵapatsa makalata a mfumu aja. Monsemo nkuti mfumu itatumiza akulu ankhondo ndiponso anthu okwera pa akavalo, kuti atsakane nane.
10Koma atamva zimenezi, akuluakulu aŵa, Sanibalati wa ku Horoni ndi Tobiya, mkulu wina wa chigawo cha Amoni, adaipidwa kwambiri poona kuti wina wabwera kudzachitira Aisraele zabwino.
11Choncho ndidafika ku Yerusalemu ndipo ndidakhala kumeneko masiku atatu.
12Sindidauze ndi mmodzi yemwe zimene Mulungu wanga adaaika mumtima mwanga, zoti ndichitire Yerusalemu. Tsono ndidadzuka usiku pamodzi ndi anthu ena oŵerengeka. Ndinalibe bulu wina kupatula yekhayo amene ndidaakwerapo.
13Ndidatuluka usiku podzera ku Chipata cha ku Chigwa, nkuyenda cha ku Chitsime cha Chilombo Cham'madzi ndi ku Chipata cha Zinyalala. Ndipo ndidayang'ana makoma a Yerusalemu amene adaagamukagamuka ndiponso zipata zake zimene zidaaonongeka ndi moto.
14Pambuyo pake ndidapitirira mpaka kukafika ku Chipata cha Kasupe ndi ku Dziŵe la Mfumu. Koma panalibe malo oti bulu amene ndidaakwerapoyo adzerepo.
15Choncho ndidayenda ndi usiku kudzera ku chigwa, kunka ndikuliyang'ana khomalo. Ndipo ndidapotoloka nkudzaloŵa mu mzinda kudzera pa Chipata cha ku Chigwa chija.
16Akuluakulu aja sadadziŵe kumene ndidaapita kapenanso zimene ndinkachita. Ndinali ndisanaŵauze Ayuda, ansembe, atsogoleri, akuluakulu aja kapenanso ena onse amene ankayenera kudzagwira ntchitoyo.
17Tsono ndidaŵauza kuti, “Mukuwona mavuto amene tili nawo. Yerusalemu wasanduka bwinja ndipo zipata zake azitentha. Tiyeni timange makoma a Yerusalemu, kuti tisamachitenso manyazi.”
18Motero ndidaŵasimbira za m'mene Mulungu wanga adandithandizira ndiponso mau amene mfumu idandiwuza. Apo anthuwo adati, “Tiyeni tiyambepo kumanga.” Choncho adalimbitsana mtima kuti akaiyambe ntchito yabwinoyo.
19Koma pamene akuluakulu aja Sanibalati ndi Tobiya ndiponso Gesemu Mwarabu adamva zimenezi, adayamba kutiseka ndi kutinyoza. Adati, “Kodi chimene mukuchitachi nchiyani? Mukuti muukire mfumu kodi?”
20Ine ndidaŵayankha kuti, “Mulungu Wakumwamba adzatithandiza kuti zinthu zitiyendere bwino, ndipo ife atumiki ake tiyambapo kumanga. Koma inuyo mulibe chanu muno, mulibe mphamvu yolandirira malo muno, ndipo mulibenso chilichonse chokumbutsa za inu mu Yerusalemu.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.