Mas. 10 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero lopempha chiweruzo cholungama

1Chifukwa chiyani mumaima kutali nafe, Inu Chauta?

Chifukwa chiyani mumabisala

pamene tili pa mavuto?

2Anthu oipa amazunza anthu osauka modzikuza.

Akodwe m'misampha yotcha iwo omwe.

3Paja munthu woipa amanyadira

zokhumba za mtima wake,

wokonda chuma amanyoza ndi kukana Chauta.

4Munthu woipa sasamala Mulungu

chifukwa cha kunyada kwake.

Mumtima mwake amati, “Kulibe Mulungu.”

5Zinthu zimamuyendera bwino nthaŵi zonse.

Chiweruzo chanu chili naye kutali,

ndipo salabadako konse.

Kunena za adani ake, iye amangoŵanyodola.

6Mumtima mwake amaganiza kuti,

“Sindidzagwedezeka, sindidzaona konse mavuto.”

7 Aro. 3.14 Pakamwa pake pamangolankhula

zotemberera, zonyenga ndi zoopseza.

M'kamwa mwake mumatuluka zovutitsa ena

ndiponso zoipa zokhazokha.

8Amalalira m'midzi,

amapha anthu osalakwa m'malo obisalira.

Amazondazonda kuti apeze opanda mwai.

9Amabisalira osauka ngati mkango m'ngaka yake,

amabisalira osauka kuti aŵagwire.

Osaukawo amaŵagwiradi akaŵakokera mu ukonde wake.

10Amambwandira ndi kupsitiriza anthu osoŵa mwai,

ndipo nyonga zake zimaŵagwetsa pansi.

11Mumtima mwake amaganiza kuti,

“Mulungu sasamalako,

waphimba maso ake,

sadzaziwona zimenezi.”

12Dzambatukani, Inu Chauta.

Onetsani mphamvu zanu, Inu Mulungu.

Musaiŵale ozunzika.

13Chifukwa chiyani munthu woipa amanyoza Mulungu?

Chifukwa chiyani mumtima mwake amati,

“Sadzandilanga?”

14Inutu mumaonadi,

mumazindikira zovuta ndi zosautsa,

kuti muchitepo kanthu.

Wopanda mwai amadzipereka kwa Inu.

Nayenso wamasiye mumamthandiza.

15Thetsani mphamvu za munthu woipa ndi wochimwa.

Fufuzani kuipa kwake,

ndipo mumlange kuti asadzabwerezenso.

16Chauta ndiye Mfumu mpaka muyaya.

Mitundu ya anthu akunja idzatheratu m'dziko lake.

17Chauta, mumamva zimene odzichepetsa amapempha.

Mudzalimbitsa mitima yao,

mudzaŵatchera khutu.

18Potero mudzaŵateteza amasiye ndi opsinjidwa,

kuti anthu amene ali a pansi pano,

asadzathe kuwopsezanso.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help