1 Eks. 12.1-27 Kudangotsala masiku aŵiri kuti chifike chikondwerero cha Paska ndi chikondwerero cha masiku odya buledi wosafufumitsa. Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo ankafunafuna njira yoti amgwirire Yesu mochenjera, nkumupha.
2Koma ankati, “Zimenezi tisadzachite pa nthaŵi ya chikondwerero ai, pangadzachitike chipolowe pakati pa anthu.”
Mai wina adzoza Yesu ku Betaniya(Mt. 26.6-13; Yoh. 12.1-8)3 Lk. 7.37, 38 Tsiku lina Yesu anali ku Betaniya, m'nyumba ya Simoni wotchedwa Wakhate. Pamene ankadya, kudafika mai wina atatenga nsupa yagalasi ya mafuta enieni onunkhira, amtengowapatali, a mtundu wa narido. Maiyo adaphwanya nsupa ija, nayamba kuthira mafutawo pamutu pa Yesu.
4Anthu ena pamenepo adaipidwa nazo nanena kuti, “Chifukwa chiyani kuŵasakaza chotere mafuta onunkhiraŵa?
5Ndithu mafuta ameneŵa akadatha kuŵagulitsa, pa mtengo wopitirira ndalama zasiliva mazana atatu, kenaka ndalamazo nkukapatsa anthu osauka?” Choncho anthuwo adamupsera mtima mai uja.
6Koma Yesu adati, “Mlekeni maiyu, mukumuvutiranji kodi? Zimenetu wandichitira iyeyuzi nzabwino kwambiri.
7Deut. 15.11Anthu osauka muli nawo nthaŵi zonse, kotero kuti pamene mufuna kuŵachitira zachifundo, mungathe kuŵachitira. Koma Ine simudzakhala nane nthaŵi zonse.
8Iyeyu wachita zimene akadatha kuchita. Wadzozeratu thupi langa ndi mafuta onunkhira, kuti alikonzeretu lisanaikidwe m'manda.
9Ndithu ndikunenetsa kuti kulikonse kumene anthu azikalalika Uthenga Wabwino pa dziko lonse lapansi, azidzafotokozanso zimene maiyu wachita, kuti anthu azidzamkumbukira.”
Yudasi apangana ndi akulu a Ayuda za kupereka Yesu(Mt. 26.14-16; Lk. 22.3-6)10Pambuyo pake Yudasi Iskariote, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja, adapita kwa akulu a ansembe kuti akapereke Yesu kwa iwo.
11Pamene iwo adamva zimenezi adakondwa, ndipo adamlonjeza kuti adzampatsa ndalama. Iyeyo tsono adayamba kufunafuna mpata womuperekera kwa iwo.
Yesu achita phwando la Paska ndi ophunzira ake(Mt. 26.17-25; Lk. 22.7-14; Yoh. 13.21-30)12Pa tsiku loyamba la masiku a buledi wosafufumitsa, tsiku lomwe anthu ankapha mwanawankhosa wochitira phwando la Paska, ophunzira a Yesu adamufunsa kuti, “Kodi tikakukonzereni kuti malo okadyerako phwando la Paska?”
13Yesu adatuma aŵiri mwa ophunzira ake, naŵauza kuti, “Pitani m'mudzimu. Mukumana ndi munthu wamwamuna atasenza mtsuko wa madzi. Mukamtsatire.
14Kunyumba kumene ati akaloŵe, mukauze mwini nyumbayo kuti, ‘Aphunzitsi akufunsa kuti, kodi nchiti chipinda cha alendo choti Iwowo adzadyeremo phwando la Paska ndi ophunzira ao?’
15Iyeyo akakuwonetsani chipinda chachikulu cham'mwamba, momwe akonzamo zonse zofunikira. M'menemo mukatikonzere chakudya.”
16Ophunzira aja adanyamuka naloŵa mumzindamo. Adachipezadi monga momwe Yesu adaaŵauzira, ndipo adakonza za phwando la Paska.
17Kutada, Yesu adabwera ndi ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja.
18Mas. 41.9Onse atakhala pansi nkumadya, Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti wina mwa inu, mnzanga wodya nane, andipereka kwa adani anga.”
19Ophunzirawo adamva chisoni, nayamba mmodzimmodzi kumufunsa kuti, “Monga nkukhala ine?”
20Yesu adaŵayankha kuti, “Ndi wina ndithu mwa khumi ndi aŵirinu, yemwe akusunsa mkate m'mbalemu pamodzi ndi ine.
21Mwana wa Munthu akukaphedwadi, monga momwe Malembo akunenera za Iye. Komabe ali ndi tsoka munthu amene akukapereka Mwana wa Munthuyo. Kukadakhala bwino koposa kwa munthu ameneyo, akadapanda kubadwa.”
Za mgonero wa Ambuye(Mt. 26.26-30; Lk. 22.15-20; 1 Ako. 11.23-25)22Iwo alikudya choncho, Yesu adatenga mkate, nathokoza Mulungu, nkuunyemanyema, nagaŵira ophunzira aja, ndipo adati, “Kwayani, ili ndi thupi langa.”
23Kenaka adatenga chikho, nathokoza Mulungu, nkuchipereka kwa ophunzirawo, naamwa onse.
24Eks. 24.8; Yer. 31.31-34 Ndipo adaŵauza kuti, “Aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka.
25Kunena zoona, sindidzamwanso chakumwa cha mtengo wamphesachi, mpaka tsiku limene ndidzamwe chatsopano mu Ufumu wa Mulungu.”
26Tsono ataimba nyimbo yotamanda Mulungu, onse adatuluka nkumapita ku Phiri la Olivi.
Yesu aneneratu kuti Petro adzamkana(Mt. 26.31-35; Lk. 22.31-34; Yoh. 13.36-38)27 Zek. 13.7 Pambuyo pake Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Nonsenu mukhumudwa nane nkundisiya. Paja Malembo akuti, ‘Ndidzapha mbusa, ndipo nkhosa zidzangoti balala.’
28Mt. 28.16Koma ndikadzauka kwa akufa, ndidzatsogola ndine kupita ku Galileya.”
29Petro adati, “Ngakhale onse akhumudwe nkukusiyani, ine ndekha ai.”
30Yesu adamuuza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti lero lomwe lino usiku womwe uno, tambala asanalire kachiŵiri, ukhala utandikana katatu kuti Ine sundidziŵa.”
31Apo Petro adanenetsanso kuti, “Ngakhale atati andiphere nanu kumodzi, ine sindingakukaneni konse kuti sindikudziŵani.” Ophunzira ena onse aja nawonso adanena chimodzimodzi.
Pemphero la Yesu ku Getsemani(Mt. 26.36-46; Lk. 22.39-46)32Yesu adapita ndi ophunzira ake aja ku malo ena, otchedwa Getsemani. Tsono adauza ophunzirawo kuti, “Inu bakhalani pano, Ine ndikukapemphera.”
33Adatengako Petro, Yakobe ndi Yohane. Yesu adayamba kugwidwa ndi chisoni ndi kuvutika mu mtima.
34Adaŵauza kuti, “Mumtima mwanga muli chisoni chachikulu chofa nacho. Inu khalani pompano, koma mukhale masotu.”
35Adapita patsogolo pang'ono, nadzigwetsa pansi, nkuyamba kupemphera. Adati, “Ngati nkotheka nthaŵi yoopsa ino indipitirire.”
36Adanenanso kuti, “Abba, Atate, mungathe kuchita chilichonse. Mundichotsere chikho cha masautsochi. Komabe chitani zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.”
37Atatero adabwerera kwa ophunzira aja, naŵapeza ali m'tulo. Tsono adafunsa Petro kuti, “Simoni, uli m'tulo kodi iwe? Mongadi walephera kukhala maso ndi kanthaŵi kochepa komwe?
38Khalani maso inu ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani. Mtima ndiye ukufunitsitsadi, koma langokhala lofooka ndi thupi.”
39Adachokanso nakapemphera ndi mau omwe aja.
40Pamene adabwerakonso, adaŵapeza ali m'tulo, chifukwa zikope zao zinkalemera ndi tulo. Choncho iwowo adasoŵa choyankha.
41Pamene adabwerako kachitatu, adati, “Kodi monga mukugonabe ndi kupumula? Basi tsopano. Nthaŵi ija yafika, Mwana wa Munthu akuperekedwa kwa anthu ochimwa.
42Dzukani, tiyeni tizipita. Suuyu wodzandipereka uja, wafika.”
Yesu agwidwa(Mt. 26.47-56; Lk. 22.47-53; Yoh. 18.2-12)43Yesu akulankhula choncho, nthaŵi yomweyo wafika Yudasi, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja. Adaabwera ndi khamu la anthu atatenga malupanga ndi zibonga. Anthuwo adaaŵatuma ndi akulu a ansembe, aphunzitsi a Malamulo ndi akulu a Ayuda.
44Wodzampereka uja anali ataŵauza chizindikiro kuti, “Yemwe ndikamumpsompsoneyo, ndi ameneyo. Mukamgwire nkupita naye, osamtaya.”
45Pamene Yudasi adabwera, adadzangofikira pa Yesu, nkunena kuti, “Aphunzitsi!” Atatero adamumpsompsona.
46Apo anthu aja adamugwira Yesu.
47Koma wina mwa ophunzira amene anali naye pamenepo, adasolola lupanga lake, natema wantchito wa mkulu wa ansembe onse, mpaka kumusenga khutu.
48Tsono Yesu adaŵafunsa anthu aja kuti, “Bwanji mwachita kunditengera malupanga ndi zibonga, ngati kuti ndine chigaŵenga?
49Lk. 19.47; 21.37Tsiku ndi tsiku ndidaali nanu m'Nyumba ya Mulungu ndikuphunzitsa, inuyo osandigwira. Koma izi zatere kuti zipherezere zomwe Malembo adanena.”
50Pamenepo ophunzira ake onse aja adathaŵa, kumsiya yekha.
51Mnyamata wina ankatsatira Yesu, atangofundira nsalu yokha, opanda chovala china. Anthu aja adaati amgwire,
52koma iye adaikolopola nsalu ija, nkuthaŵa ali maliseche.
Yesu ku Bwalo Lalikulu la akulu a Ayuda(Mt. 26.57-68; Lk. 22.54-55, 63-71; Yoh. 18.13-14, 19-24)53Tsono anthu aja adapita naye Yesu kwa mkulu wa ansembe onse. Kumeneko kudaasonkhana onse akulu a ansembe, akulu a Ayuda, ndi aphunzitsi a Malamulo.
54Petro ankamutsatira Yesu chapatali, mpaka ku bwalo la nyumba ya mkulu wa ansembe uja. Adakhala pansi pamodzi ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu, nkumaotha nao moto.
55Akulu a ansembe aja ndi onse a m'Bwalo Lalikulu la Ayuda ankafunafuna umboni woneneza Yesu kuti amuphe, koma osaupeza.
56Ambiritu ankamuneneza zabodza, koma umboni wao sunkagwirizana.
57Ena adaimirira nayamba kumneneza zabodza.
58Yoh. 2.19Adati, “Munthu uyu ife tidamumva akunena kuti, ‘Ine ndidzapasula Nyumba ya Mulunguyi, yomangidwa ndi anthu chabe, ndipo patapita masiku atatu ndidzamanga ina yosamangidwa ndi anthu.’ ”
59Koma ngakhale aponso zokamba zaozo sizinali zogwirizana.
60Tsono mkulu wa ansembe onse adaimirira pamaso pao, nafunsa Yesu kuti, “Kodi ulibe poyankha? Nzotani zimene anthuŵa akukunenezazi?”
61Yesu adangokhala chete, osayankha kanthu. Pamenepo mkulu wa ansembe uja adafunsanso kuti, “Kodi ndiwedi Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu Wolemekezeka?”
62Dan. 7.13Yesu adayankha kuti, “Inde, ndinedi. Ndipo mudzaona Mwana wa Munthu atakhala ku dzanja lamanja la Mulungu wamphamvuzonse. Mudzamuwona akubwera pa mitambo.”
63Apo mkulu wa ansembe uja adang'amba zovala zake, nati, “Kodi pamenepa tikusoŵanso mboni zina?
64Lev. 24.16 Mwadzimvera nokha kunyoza Mulungu koopsaku. Tsono mukuganiza bwanji?” Onse adagamula kuti ayenera kuphedwa.
65Ena adayamba kumthira malovu, namuphimba m'maso nkumamuwomba makofi, namanena kuti, “Lotatu, wakumenya ndani?” Alonda aja nawonso adayamba kummenya.
Petro akana Yesu(Mt. 26.69-75; Lk. 22.56-62; Yoh. 18.15-18, 25-27)66Petro anali kunsi pa bwalo. Mtsikana wina, wantchito wa mkulu wa ansembe onse, adafika pomwepo.
67Ataona Petro akuwotha moto, adamuyang'anitsitsa, nati, “Inunsotu munali ndi Yesu wa ku Nazareteyu.”
68Koma Petro adakana, adati, “Zimenezo ine sindikuzidziŵa, sindikuzimvetsa konse.” Ndipo adatuluka kumapita cha ku chipata. Pamenepo tambala adalira.
69Koma mtsikana uja adamuwona, nayambanso kuuza amene anali pamenepo kuti, “Akulu ameneŵa anali m'gulu lomweli.”
70Koma Petro adakananso. Patangopita kanthaŵi, anthu amene adaali pamenepo adamuuza Petro kuti, “Ndithu nawenso ndiwe wa gulu lomweli. Kodi kwanu si ku Galileya iwe?”
71Koma Petro adayamba kudzitemberera nkumalumbira kuti, “Mtheradi, munthu amene mukunenayu ine sindimdziŵa.”
72Nthaŵi yomweyo tambala adalira kachiŵiri. Tsono Petro adakumbukira mau aja a Yesu akuti, “Tambala asanalire kaŵiri, ukhala utakana katatu kuti sundidziŵa.” Pomwepo Petro adayamba kulira misozi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.