1Ndidaonanso zinthu m'masomphenya: ndidaona munthu atatenga chingwe choyesera m'manja mwake.
2Ndidamufunsa kuti, “Kodi mukupita kuti?” Iye adandiyankha kuti, “Ndikukayesa mzinda wa Yerusalemu kuti ndidziŵe kutalika kwa muufupi mwake ndi m'litali mwake.”
3Apo mngelo uja ankalankhula naneyu adasendera, mngelo winanso adadzakumana naye.
4Woyamba uja adauza mnzakeyo kuti, “Thamangira mnyamata wachingweyo, ukamuuze kuti mu Yerusalemu mudzakhala anthu ambiri ndiponso zoŵeta zochuluka, kotero kuti mzindawo udzakhala wopanda malinga.
5Chauta akuti Iye yemwe ndiye adzakhale linga lamoto loteteza mzindawo, ndipo adzaonetsa ulemerero wake m'kati mwake.”
6Chauta akunena kuti, “Tiyeni, tiyeni, thaŵaniko ku dziko lakumpoto. Paja ndidakumwazirani ku mphepo zinai za mlengalenga.
7Tiyeni, thaŵirani ku Ziyoni, inu amene mudatengedwa ukapolo kupita ku Babiloni.
8Aliyense wokantha inu, wakantha chinthu cha mtengo wapatali zedi kwa Ine.” Tsono Chauta Wamphamvuzonse adandituma kwa mitundu imene idaagwira anthu ake kukaiwuza uthenga wake wakuti,
9“Ine Chauta ndidzaŵamenya anthuwo ndi dzanja langa, ndipo amene anali akapolo ao, ndiwo amene adzaŵalande chuma chao.” Pamenepo mudzadziŵa kuti Chauta Wamphamvuzonse ndiye wandituma.
10“Inu anthu a ku Ziyoni, imbani mokondwa, chifukwa ndikubwera, ndikudzakhala pakati panu,” akutero Chauta.
11Nthaŵi imeneyo anthu a mitundu yambiri adzabwera kwa Chauta, adzasanduka anthu ake, ndipo Iye adzakhala pakati panu. Apo mudzadziŵa kuti Chauta Wamphamvuzonse ndiye wandituma kwa inu.
12Iyeyo adzamtenganso Yuda kuti akhale chuma chake m'dziko lopatulika, ndipo Yerusalemu adzakhala mzinda wake wapamtima.
13Anthu nonsenu, ingokhalani chete pamaso pa Chauta, chifukwa wadzambatuka ndi kutuluka ku malo ake oyera.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.