Yob. 12 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Yobe adayankha kuti,

2“Inunso ndinu anthu,

ndipo mukafa, nzeru zanu zidzafera nanu pamodzi.

3Koma inenso ndili nazo nzeru ngati inu nomwe.

Inu simundipambana, ai.

Aliyense amadziŵa zonse mwanenazi.

4Ine ndine chinthu choseketsa kwa abwenzi anga.

Ine amene ndinkapemphera kwa Mulungu, Iye nkundiyankha,

ine munthu wolungama ndi wopanda mlandu,

tsopano ndine chinthu chochiseka.

5Munthu amene ali pabwino

amanyoza mnzake amene ali pa tsoka.

Tsokalo limagwa pa amene wayamba kale kugwa.

6Achifwamba ndiwo amakhala pa mtendere,

amene amaputa Mulungu ndiwo amakhala pabwino.

Anthuwo amadalira nyonga zao ngati ndiye Mulungu wao.

7“Koma ufunse kwa nyama zakuthengo, zidzakuphunzitsa.

Ufunse mbalame zamumlengalenga, zidzakuuza.

8Upemphe nzeru kwa zolengedwa za dziko lapansi,

zidzakuphunzitsa, ngakhale nsomba zam'nyanja

zidzakufotokozera.

9Kodi mwa zonsezo nchiti chimene

sichidziŵa kuti zonsezi adachita ndi Chauta?

10M'manja mwake ndimo muli zamoyo zonse,

mulinso moyo wa anthu a mitundu yonse.

11Kodi suja khutu ndiye limamva mau,

monga m'mene lilime ndiye limalaŵa chakudya?

12Inde anthu okalamba ali ndi nzeru,

anthu amvulazakale ndi omvetsa zinthu.

13“Koma Mulungu ali ndi nzeru ndi mphamvu zopambana.

Ali ndi uphungu wabwino, ndi kumvetsa zinthu zonse.

14Akapasula, palibe woti nkumanganso.

Akatsekera munthu m'ndende, palibe woti nkumtsekulira.

15Akamanga mvula, dziko limauma,

Akaimasula, madzi amasefukira pa dziko lonse.

16Iye ali ndi mphamvu, ndiponso ali ndi nzeru zonse.

Anthu opusitsidwa, ndiponso opusitsa anzao,

onsewo ali mu ulamuliro wake.

17Iye amalanda aphungu nzeru zao,

ndipo amapusitsa aweruzi.

18Amamasula am'ndende a mafumu,

ndipo amaŵamanga mafumuwo.

19Amasokeza ansembe ataŵalanda nzeru zao,

ndipo amatsitsa atsogoleri amphamvu.

20Amakhalitsa chete aphungu okhulupirika,

ndipo akuluakulu amaŵalanda luntha.

21Amanyoza anthu otchuka,

ndipo anthu anyonga amaŵatha mphamvu.

22Amavundukula zamumdima,

ndipo mdimawo amausandutsa kuŵala.

23Amakuza mitundu ina ya anthu,

koma inanso amaiwononga.

Amachulukitsa mafuko, nkuŵamwazanso.

24Amasandutsa atsogoleri kuti akhale zitsiru,

ndi kumaŵayendetsa m'thengo mopanda njira.

25Iwowo amanka nafufuza njira mumdima mopanda kuŵala,

nkumayenda ali dzandidzandi ngati oledzera.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help