Mas. 41 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero la munthu wodwalaKwa Woimbitsa Nyimbo. Salmo la Davide.

1Ngwodala munthu amene amaganizirako za amphaŵi,

popeza kuti Chauta adzapulumutsa munthu wotere

pa tsiku lamavuto.

2Chauta adzamteteza ndi kumsunga ndi moyo.

Adzatchedwa wodala pa dziko.

Chauta sadzampereka kwa adani ake,

kuti amchite zimene iwo akufuna.

3Chauta adzamthandiza munthuyo akamadwala.

Adzamchiritsa matenda ake onse.

4Tsono ndidati, “Inu Chauta, ndakuchimwirani,

mundikomere mtima, muchiritse moyo wanga.”

5Koma adani anga ondifunira zoipa, amati,

“Kodi munthu ameneyu adzafa liti, kuti aiŵalike?”

6Amene amabwera kudzandiwona,

ndi wosakhulupirika,

mumtima mwake amaganiza zoipa za ine,

ndipo akatuluka, amakaziwanditsa.

7Onse odana nane amanong'onezana za ine,

amayesa kuti zoipa zandigwera

chifukwa cha kuipa kwanga.

8Amati, “Yamgwera nthenda yofa nayo,

sadzukanso pamene wagonapo.”

9 Mt. 26.23; Mk. 14.18; Lk. 22.21; Yoh. 13.18 Ngakhalenso bwenzi langa lapamtima

amene ndinkamkhulupirira,

amene ankadya nane pamodzi,

wandiwukira.

10Koma Inu Chauta, mundikomere mtima,

mundichiritse kuti ndiŵalange anthuwo.

11Mukatero ndidzadziŵa kuti mumakondwera nane,

chifukwa mdani wanga sadandipambane.

12Inu mwandichirikiza

chifukwa cha kukhulupirika kwanga,

mwandikhazika pamaso panu mpaka muyaya.

13 Mas. 106.48 Atamandike Chauta, Mulungu wa Israele,

kuyambira muyaya mpaka muyaya.

Inde momwemo. Inde momwemo.

BUKU LACHIŴIRI(Mas. 42—72)
Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help