1Pambuyo pake Yosefe adalamula wantchito wamkulu woyang'anira nyumba yake kuti, “Dzaza matumba a anthuŵa ndi chakudya chambiri momwe angathe kusenzera. Ndipo ndalama za aliyense uziike pakamwa pa thumba.
2Tsono pakamwa pa thumba la wamng'onoyo uikepo chikho changa chasiliva chija, pamodzi ndi ndalama zake zimene amati agulire tirigu.” Wantchitoyo adachita monga momwe adaamuuzira.
3M'maŵa kutacha, anthu aja adaloledwa kupita pamodzi ndi abulu ao.
4Atangoyenda pang'ono kuchoka mumzindamo, Yosefe adauza wantchito wake wamkulu uja kuti, “Nyamuka, uthamangire anthu aja. Ukaŵapeza, uŵafunse kuti, ‘Bwanji mwabwezera zoipa kwa zabwino?
5Mwaberanji chikho chimene mbuyanga amamwera? Amati akafuna kudziŵa zam'tsogolo, amagwiritsa ntchito chikho chimenechi. Ndithu zimene mwachitazi nzoipa kwambiri.’ ”
6Wantchito uja ataŵapeza, adanena mau omwe adaamuuza aja.
7Iwo aja adamuyankha kuti, “Kodi mukulankhulazi nzotani bwana? Ife sitikadatha mpang'ono pomwe kuganiza kuti tichite zimene mukunenazi.
8Inu nomwe mudaona kuti ife pochoka ku Kanani, tidabwera ndi ndalama zimene tidaazipeza m'matumba mwathu. Nanga tingaberenji siliva kapena golide m'nyumba mwa bwana wanu?
9Tsono bwana, wina mwa ife akapezeka ndi chikho chimenechi, ndithu aphedwe, ndipo tonsefe tidzakhala akapolo anu, bwana!”
10Apo wantchitoyo adati, “Chabwino. Komatu wina pakati panupa akapezeka ndi chikhocho, ameneyo akhala kapolo wanga, ena nonsenu muzipita mwaufulu.”
11Motero onsewo adatsitsa msanga matumba ao, aliyense nkumasula thumba lake.
12Wantchito wa Yosefe uja adafunafuna mosamala kwambiri kuyambira pa wamkulu mpaka pa wamng'ono, ndipo chikhocho adachipeza m'thumba la Benjamini.
13Apo onsewo adang'amba zovala zao ndi chisoni. Adasenzetsanso abulu katundu wao uja, nabwerera kumzinda konkuja.
14Yuda ndi abale ake atafika kunyumba kwa Yosefe, adampeza akadali momwemo ndipo onsewo adaŵerama pamaso pake.
15Yosefe adati, “Mwachita chiyani? Kodi simukudziŵa kuti munthu monga ine ndingathe kudziŵa zakutsogolo?”
16Apo Yuda adati, “Kodi ife tinganene chiyani kwa inu, bwana? Tilinso ndi mau ngati? Tingathe kudziyeretsa bwanji? Mulungu waulula cholakwa chathu, bwana. Tonsefe bwana, ndife akapolo anu, osati mmodzi yekha amene wapezeka ndi chikhoyu ai.”
17Koma Yosefe adati, “Iyai! Ine sindingathe kuchita zotero. Yekhayo amene wapezeka ndi chikho, ndiye adzakhala kapolo wanga. Enanu mungathe kumabwerera kwanu kwa bambo wanu.”
Yuda apepesera Benjamini18Pamenepo Yuda adasendera kwa Yosefe, nati “Pepani bwana, loleni ine mtumiki wanu kuti ndilankhule nanu. Musati mukwiye nane bwana, inu muli ngati Farao yemwe.
19Bwana, paja mudaatifunsa kuti, ‘Kodi muli naye bambo wanu kapena mbale wanu?’
20Ndipo ife tidaakuyankhani kuti, ‘Tili naye bambo wathu wokalamba ndi mbale wathu wina wamng'ono amene adabadwa bambo wathuyo atakalamba kale. Mkulu wake wa mnyamata ameneyo adamwalira kale. Choncho m'mimba mwa mai wake, yekhayu ndiye amene ali moyo, ndipo bambo wake amamkonda kwabasi.’
21Bwana, paja inu mudaatiwuza kuti, ‘Mudzabwere naye, kuti ndidzamuwone.’
22Ife tidaakuyankhani kuti, ‘Mnyamatayo sangachoke kwa bambo wake, popeza kuti akatero, bambo wakeyo kufa kudzakhala komweko.’
23Tsono paja mudaanena kuti simudzatilola kufikanso pamaso panu tikadzapanda kubwera naye mng'ono wathuyo.
24Titabwerera kwathu kwa bambo wathu mtumiki wanu, tidamuuza mau anu onse aja.
25Iye atatiwuza kuti, ‘Bwererani mukatigulireko chakudya pang'ono,’
26ife tidamuuza bambo wathu kuti, ‘Sitingathe kupita popeza kuti munthu uja sakatilola kufika pamaso pake, tikapanda kupita ndi mng'ono wathuyu.’
27Koma bambo wathu adati, ‘Mukudziŵa kuti mkazi wanga adandibalira ana aŵiri.
28Wina mwa iwowo adandisiya kale. Ndiye kuti adajiwa ndi zilombo chifukwa sindidamuwonenso.
29Tsopano mukanditengeranso uyu, nakaphedwa, ndiye kuti ine ndidzafa ndi chisoni.’ ”
30Yuda adapitiriza kulankhula nati, “Nchifukwa chake tsopano ndikabwerera kwathu kwa bambo wanga, mtumiki wanu, opanda mnyamata ameneyu, amene moyo wa bambo wanga uli pa iye,
31akakangoona kuti iyeyu palibe, basitu akafa. Ndiye kuti ifeyo ndi amene tidzachititse bambo wathu chisoni chofa nacho mu ukalamba wake.
32Ndiponsotu bwana, ine ndidapereka moyo wanga kwa bambo wanga chifukwa cha mnyamata ameneyu. Ndidamuuza kuti ngati mnyamatayu sindidzabwerera naye, ndidzakhala wolakwa pamaso pa bambo wanga moyo wanga onse.
33Ndiye tsopano bwana, ineyo nditsalira kuno kuti ndikhale kapolo wanu m'malo mwa mnyamatayu. Muloleni iyeyu apite ndi abale akeŵa.
34Ine ndingathe bwanji kupita kwa bambo wanga popanda mnyamatayu kupita nane? Ine ndekha sindingathe kupirira kuti ndiwone tsoka lotere likugwera bambo wanga.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.