1 Mbi. 29 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Zopereka zaufulu zomangira Nyumba ya Chauta

1

3Komanso kuwonjezera pa zonse zimene ndidaperekera Nyumba yoyerayo, ndili nachonso chuma changa cha golide ndi siliva. Ndipo chifukwa cha kudzipereka kwanga pa Nyumba ya Chauta wanga, ndikuchiperekanso chumacho kwa Mulungu wanga.

4Ndikupereka matani a golide 100, golide wake wabwino kwambiri wa ku Ofiri, ndi matani a siliva wosalala 240. Zonsezo zidzakhala zokutira makoma a Nyumba,

5ndiponso zogwiritsira ntchito zonse zochitika ndi anthu aluso, golide wopangira zinthu zagolide ndiponso siliva wopangira zinthu zasiliva. Tsono pakati pa inuyonso ndani amene atapeko mwaufulu zinthu zake ndi kuzipereka kwa Chauta?”

6Pomwepo atsogoleri a mabanja a makolo adapereka zopereka zao mwaufulu, monga momwe adachitiranso atsogoleri a mafuko, atsogoleri a magulu a anthu zikwi, atsogoleri a magulu a anthu mazana ndiponso akapitao a ntchito za mfumu.

7Zimene adapereka ku ntchito ya Nyumba ya Chauta ndi izi: matani 170 a golide, makilogramu 84 a ndalama zagolide za mtundu wina, matani 340 a siliva, matani pafupifupi 620 a mkuŵa, ndipo matani oposa 3,400 a chitsulo.

8Aliyense amene anali nayo miyala ya mtengo wapatali, ankaipereka ku nyumba zosungiramo chuma cha Chauta. Amene ankasamala zimenezo anali Yehiyele Mgeresoni.

9Tsono anthu adakondwa chifukwa chakuti akulu aowo ankapereka mwaufulu ndiponso ndi mtima wao wonse. Nayenso mfumu Davide adakondwa kwambiri.

Davide atamanda Mulungu

10Nchifukwa chake Davide adatamanda Chauta pamaso pa msonkhano wonse. Adati, “Mutamandike mpaka muyaya Inu Chauta, Mulungu wa Israele, kholo lathu.

11Mt. 6.13 Inu Ambuye, ndinu aakulu, amphamvu, aulemerero, opambana pa nkhondo ndiponso oposa pa ulemu, pakuti zonse zakumwamba ndi za pansi pano nzanu. Mfumu ndinu nokha, Inu Chauta, ndipo wolamulira zonse ndinu.

12Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu ndipo mumalamulira zonse, chifukwa muli ndi mphamvu zonse. Inu nokha mutha kukweza munthu ndi kumpatsa mphamvu.

13Tsopano tikukuthokozani, Inu Mulungu wathu, ndi kutamanda dzina lanu laulemerero.

14“Koma ine ndine yani, ndipo anthu anga ndi ayani kuti tingathe kupereka mwaufulu motere? Paja zinthu zonse zimachokera kwa Inu ndipo zimene tikupereka kwa Inu nzanu zomwe.

15Inu Chauta, mukudziŵa kuti ife ndife alendo chabe pansi pano. Tili ngati anthu ongokhala nao chabe, monga momwe analiri makolo athu. Masiku athu okhala pa dziko lapansi ali ngati chithunzithunzi chabe ndipo palibe poti tingakhulupirire.

16Inu Chauta, Mulungu wathu, inde tapereka mphatso zimenezi kuti akumangireni nyumba, koma zonsezi zikuchokera m'manja mwanu ndipo nzanu zomwe.

17Mulungu wanga, ndikudziŵa kuti Inu mumapenyetsetsa mtima, ndipo mumakondwera ndi anthu achilungamo. Ndapereka mwaufulu zinthu zonse ndi mtima wolungama, ndipo tsopano ndaŵaona anthu anu amene ali panoŵa nawonso akupereka mwaufulu ndi mokondwa kwa Inu.

18Inu Chauta, Mulungu wa makolo athu aja, Abrahamu, Isaki ndi Israele, limbitsani nthaŵi zonse maganizo ndi makhalidwe ameneŵa mwa anthu anu, ndipo akhale ndi mtima wokhulupirika mpaka kwa Inu muyaya.

19Mwana wanga Solomoni mumpatse mtima wangwiro, kuti azisunga malamulo ndi malangizo anu ndi kuŵatsata bwino ndithu, ndiponso kuti amange nyumba imene ine ndaipezera zofunika zonsezi.”

20Tsono Davide adauza msonkhano wonse kuti, “Tamandani Chauta, Mulungu wanu.” Apo anthu onsewo adatamanda Chauta, Mulungu wa makolo ao. Adaŵeramitsa mitu yao napembedza Chauta, ndipo adalambira mfumu.

21M'maŵa mwake anthuwo adapereka kwa Chauta, nsembe zopsereza izi: ng'ombe 1,000, nkhosa zamphongo 1,000, ndiponso anaankhosa 1,000, pamodzi ndi chopereka cha chakumwa, kudzanso nsembe zina zochuluka zoperekera Aisraele onse.

22Tsiku limenelo adadya ndi kumwa mosangalala kwambiri pamaso pa Chauta.

Pambuyo pake Solomoni, mwana wa Davide, anthu adamlonga ufumu kachiŵiri. Adamdzoza pamaso pa Chauta kuti akhale mfumu, ndipo Zadokinso kuti akhale wansembe.

231Maf. 2.12 Tsono Solomoni adakhala pa mpando waufumu wa Chauta nakhala mfumu m'malo mwa Davide atate ake. Zinthu zinkamuyendera bwino, ndipo Aisraele onse ankamumvera.

24Atsogoleri onse, ankhondo ndi ana a mfumu Davide omwe, onsewo adadzipereka kwa mfumu Solomoni.

25Aisraele onse adaona m'mene Chauta adakwezera Solomoni. Adampatsadi ukulu wa ufumu wakuti mfumu ina iliyonse sidaulandirepo m'dziko la Israele, iyeyo asanaloŵe.

Imfa ya Davide

26Umu ndimo m'mene Davide, mwana wa Yese, adalamulira Aisraele onse.

272Sam. 5.4, 5; 1Mbi. 3.4 Nthaŵi imene Davide adalamulira Aisraele idakwanira zaka 40. Adalamulira zaka zisanu ndi ziŵiri ku Hebroni, ndipo ku Yerusalemu adalamulirako zaka 33.

28Tsono adamwalira atafika pokalamba zedi. Masiku ake adachuluka, pamodzi ndi chuma ndi ulemerero wake. Ndipo Solomoni, mwana wake, adaloŵa ufumu m'malo mwake.

29Tsono ntchito za mfumu Davide kuyambira pa chiyambi mpaka potsiriza pake, zidalembedwa m'buku la mbiri ya mneneri Samuele, m'buku la mbiri ya mneneri Natani, ndi m'buku la mbiri ya mneneri Gadi.

30M'menemo adasimba za kulamulira kwake, za mphamvu zake ndiponso za zonse zimene zidamuwonekera iyeyo, mpakanso zimene zidaonekera fuko la Israele ndiponso zimene zidaonekera maiko ena ozungulira.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help