Akol. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Ndikufuna kuti mudziŵe kuti ndikukuvutikirani kwambiri, inuyo ndi anzanu a ku Laodikea, ndi ena onse amene sitidaonane nawo maso ndi maso chikhalire.

2Ndikufuna kuti zimenezi ziŵalimbitse mtima, ndipo azilunzana pamodzi m'chikondi, azikhala odzaza ndi nzeru zomvetsa zinthu. Motero adzatha kudziŵa mozama chinsinsi cha Mulungu chonena za Khristu.

3Mwa Iyeyu mudzapeza chuma chonse chobisika, ndiye kuti nzeru ndi luntha.

4Ndikunenatu zimenezi, kuwopa kuti wina aliyense angakukopeni ndi mau onyenga.

5Pakuti ngakhale sindili nanu m'thupi, komabe mumtimamu ndili nanu pamodzi. Ndipo ndakondwa kuwona kuti mukulongosola bwino zonse, ndi kuti chikhulupiriro chanu mwa Khristu nchosagwedezeka konse.

Za moyo weniweni pakukhala mwa Khristu

6Tsono popeza kuti mudavomereza kuti Khristu Yesu ndi Mbuye wanu, moyo wanu wonse ukhale wolunzana naye.

7Mukhale ozika mizu mwa Iye. Mupitirire kumanga moyo wanu pa Iye. Mulimbike kukhulupirira monga momwe mudaphunzirira, ndipo muzikhala oyamika kwambiri.

8Chenjerani kuti wina aliyense angakusokonezeni ndi mau olongosola nzeru zapatali. Ameneŵa ndi mau onyenga chabe. Paja nzeru zimenezi zimangochokera ku miyambo ya anthu, ndi ku maganizo ao okhudza zapansipano, osati kwa Khristu ai.

9Pakuti m'thupi la Khristu umulungu wonse umakhalamo wathunthu.

10Ndipo mwa Iye inu mudapatsidwa moyo wonse wathunthu. Iye ndiye mutu wolamulira maulamuliro onse ndi mphamvu zonse zosaoneka.

11Mwa Iye mudachita ngati kuumbalidwa, osatitu kuumbala kwa anthuku ai, koma kuvula khalidwe lanu lokonda zoipa; kuumbala kumene amachita Khristu nkumeneku.

12Aro. 6.4Pamene mudabatizidwa, mudachita ngati kuikidwa m'manda pamodzi ndi Khristu. Ndipo ndi ubatizowo mudaukitsidwanso pamodzi naye, pakukhulupirira mphamvu za Mulungu amene adamuukitsa kwa akufa.

13Aef. 2.1-5Inu kale munali akufa chifukwa cha machimo anu, ndiponso chifukwa munali osaumbalidwa mu mtima. Koma tsopano Mulungu wakupatsani moyo pamodzi ndi Khristu. Adatikhululukira machimo athu zonse.

14Aef. 2.15Adafafaniza kalata ya ngongole yathu, yonena za Malamulo a Mose. Kalatayo inali yotizenga mlandu, koma Iye adaichotsa pakuikhomera pa mtanda.

15Motero mwa Khristu Mulungu adaŵalanda zida maufumu ndi maulamuliro onse, ndipo pamaso pa onse, adaŵayendetsa ngati akaidi pa mdipiti wokondwerera kupambana kwake.

16 Aro. 14.1-6 Wina aliyense asakuzengeni mlandu pa nkhani yokhudza zakudya kapena zakumwa, kapena pa zokhudza masiku a chikondwerero, kapena a mwezi wokhala chatsopano, kapena pa zokhudza tsiku la Sabata.

17Zonsezi ndi chithunzithunzi chabe cha zinthu zenizeni zimene zilikudza, koma zenizenizo ndi Khristu amene.

18Wina aliyense asakuletseni kupata mphothoyo. Iwo aja amakonda kudziwonetsa ngati odzichepetsa, popembedza amatamanda angelo. Amaika mtima pa zimene akuti adaziwona m'masomphenya. Amadzitukumula popanda chifukwa, popeza kuti amangotsata nzeru za anthu,

19Aef. 4.16osakangamira Khristu amene ali mutu wa Mpingo. Komatu mwa Khristu thupi lonse limalandira mphamvu, ndi kulumikizika pamodzi mwa mfundo zake ndi mitsempha yake. Motero thupi limakula monga momwe Mulungu afuna kuti likulire.

Za kufa ndi kuuka pamodzi ndi Khristu

20Mudafa pamodzi ndi Khristu, ndiye kuti simulamulidwanso ndi miyambo ya dziko lapansi. Tsono bwanji mukuchita ngati kuti moyo wanu ukudalirabe zapansipano? Bwanji mukuŵamvera malamulo onga aŵa akuti,

21“Usagwire chakuti”, “Usakhudze chakuti”?

22Malamulo ameneŵa ndi zophunzitsa zimenezi ndi za anthu chabe, ndipo zimangokhudza zinthu zimene zimatha, anthu akamazigwiritsa ntchito.

23Kwinaku mauwo amaoneka ngati anzeru, pakuti amalamula anthu zambiri pa za kupembedza, za kudzichepetsa ndi za kuzunza thupi lao. Komabe malamulowo alibe phindu, ndipo sathandiza konse kugonjetsa khalidwe longosangalatsa thupi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help