1
16Apo Samuele adamuuza kuti, “Basi, musapitirize! Imani ndikukambireni zimene Chauta wandiwuza usiku.” Tsono Saulo adati, “Nenani.”
17Samuele adati, “Ngakhale kale munali wamng'ono pamaso pa anthu, tsopano mwasanduka mtsogoleri wa mafuko onse a Aisraele. Chauta adakudzozani kuti mukhale mfumu yomalamulira Aisraele.
18Ndipo Chauta adakutumani kuti, ‘Pita, ukaononge kwathunthu Aamaleke, anthu oipa mtima aja, ndipo uchite nawo nkhondo mpaka kuŵatheratu onsewo.’
19Chifukwa chiyani nanga simudamvere mau a Chauta? Chifukwa chiyani mudathamangira zofunkha ndi kuchita zoipira Chauta?”
20Saulo adayankha kuti, “Iyai, inetu mau a Chauta ndidatsata, ndipo ndidapitadi kukachita zimene Chauta adandituma. Ndidagwira Agagi mfumu ya Aamaleke, ndipo ndidapha Aamaleke onse.
21Koma pa zofunkha anthu adatengako nkhosa ndi ng'ombe, ndi zina zabwino kwambiri, zimene zinkayenera kuwonongedwa, kuti akazipereke nsembe kwa Chauta, Mulungu wanu, ku Giligala.”
22Koma Samuele adati,
“Kodi Chauta amakondwa ndi chiti:
nsembe zopsereza ndi nsembe zina,
kapena kumvera mau ake?
Ndithu, ndi kumvera ndi kupereka nsembe
kwabwino kwambiri nkumvera.
Ndi kutchera khutu ndi kupereka mafuta ankhosa
kwabwino kwambiri nkutchera khutu.
23Kugalukira kuli ngati tchimo loombeza,
kukhala wokanika kuli ngati tchimo lopembedza mafano.
Popeza kuti mwakana mau a Chauta,
Iyenso wakukanani kuti musakhalenso mfumu.”
24Pamenepo Saulo adauza Samuele kuti, “Ndachimwa, ndalakwira lamulo la Chauta ndiponso malangizo anu, chifukwa chakuti ndinkaopa anthu ndipo ndinkamvera mau ao.
25Nchifukwa chake tsono pepani, ndagwira mwendo, mundikhululukire tchimo langa, ndipo mubwerere nane pamodzi, kuti ndikampembedze Chauta.”
26Koma Samuele adayankha kuti, “Sindibwerera nanu, popeza kuti mwakana mau a Chauta, Iyenso wakukanani kuti musakhalenso mfumu yolamulira Aisraele.”
271Sam. 28.17; 1Maf. 11.30, 31 Pamene Samuele ankatembenuka kuti azipita, Saulo adagwira mpendero wa mkanjo wake, ndipo mkanjowo udang'ambika.
28Apo Samuele adamuuza kuti, “Chauta wachita ngati kung'amba ufumu wa Israele kuchoka kwa inu lero, ndipo waupereka kwa mnzanu wabwino koposa inuyo.
29Mulungu Waulemerero wa Aisraele sanama kapena kusintha maganizo. Pakuti Iye si munthu, kuti athe kusintha maganizo.”
30Tsono Saulo adati, “Inde ndachimwa, komabe chonde mundilemekeze pakati pa atsogoleri a anthu anga ndi pamaso pa Aisraele onse, ndipo mubwerere nane pamodzi, kuti ndikapembedze Chauta, Mulungu wanu.”
31Choncho Samuele adabwereradi, natsagana ndi Saulo. Ndipo Sauloyo adapembedza Chauta.
32Pambuyo pake Samuele adauza Saulo kuti, “Bwera nayeni kuno Agagi uja, mfumu ya Aamaleke.” Ndipo Agagiyo adafika kwa Samuele mokondwa, chifukwa adati, “Ndithudi, zoŵaŵa za imfa zapita!”
33Koma Samuele adati,
“Monga momwe lupanga lako lasandutsira akazi
kuti akhale opanda ana,
momwemonso mai wako adzakhala wopanda
mwana pakati pa akazi ena.”
Ndipo Samuele adapha Agagiyo namduladula patsogolo pa guwa la Chauta ku Giligala.
34Tsono Samuele adapita ku Rama, koma Saulo adapita ku nyumba yake ku Gibea wa Saulo.
35Samuele sadamuwonenso Saulo moyo wake wonse, koma ankamulira ndithu, popeza kuti Chauta adaamuchotsa Sauloyo kukhala mfumu yolamulira Aisraele.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.