1 2Maf. 24.1; 2Mbi. 36.5-7; Dan. 1.1, 2 Naŵa mau amene adadza kwa Yeremiya, onena za anthu onse a ku Yuda. Mauŵa adafika chaka chachinai cha ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya ku Yuda, ndiye kuti chaka choyamba cha ufumu wa Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni.
2Mneneri Yeremiya adauza anthu onse a ku Yuda ndi onse okhala ku Yerusalemu kuti,
3“Pa zaka 23, kuyambira chaka cha 13 cha ufumu wa Yosiya mwana wa Amoni mfumu ya ku Yuda, mpaka lero lino, ndakhala ndikulandira mau a Chauta ndi kumavutika nkukuuzani, koma inu simudamvere.
4Inu simudamvere kapena kutchera khutu, ngakhale kuti Chauta sadaleke kukutumirani aneneri, atumiki ake.
5Aneneriwo ankati, ‘Aliyense mwa inu akaleka makhalidwe ake oipa ndi ntchito zake zoipa, ndiye kuti mudzakhala m'dziko limene Chauta adakupatsani inu ndi makolo anu mpaka muyaya.
6Musamatsate milungu ina, kumaitumikira ndi kumaipembedza. Musamapute mkwiyo wanga ndi mafano opanga ndi manja anu. Tsono Ine sindidzakuwonongani.’
7Komabe simudandimvere. Mudaputa mkwiyo wanga ndi mafano amene mudapanga ndi manja anu, motero mudadziwononga nokha,” akuterotu Chauta.
8Motero Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Chifukwa choti simudamvere mau anga,
9ndidzaitana mafuko onse akumpoto, pamodzi ndi mtumiki wanga Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni. Ndidzaŵatuma kuti adzathire nkhondo dzikoli ndi anthu ake, ndiponso anthu a mitundu ina yozungulira dzikoli. Ndidzaŵaononga kwathunthu ndi kuŵasandutsa chinthu chonyansa, chonyozeka ndiponso chochititsa manyazi mpaka muyaya.
10Yer. 7.34; 16.9; Chiv. 18.22, 23 Ndidzathetsa chimwemwe chonse ndi kusangalala konse pakati pao. Ndidzaletseratu mau achikondwerero a mkwati wamwamuna ndi mkwati wamkazi. Sikudzamvekanso phokoso la mphero, ndipo ndidzazima nyale zonse.
112Mbi. 36.21; Yer. 29.10; Dan. 9.2 Dziko lonseli lidzakhala chipululu ndi bwinja. Pa zaka makumi asanu ndi aŵiri mitundu imeneyi idzatumikira mfumu ya ku Babiloni.
12Zaka makumi asanu ndi aŵirizo zitatha, ndidzailanga mfumu ya ku Babiloniyo pamodzi ndi anthu ake chifukwa cha zoipa zao, ndipo dziko lao ndidzalisandutsa bwinja mpaka muyaya.
13Ndidzachita zonse zimene ndidanena zokhudza dziko limenelo, zonse zimene zidalembedwa m'bukumu, ndiponso zonse zimene mneneri Yeremiya adalosa zotsutsa anthu ameneŵa.
14Iwo adzakhala akapolo a anthu a mitundu yochuluka ndi a mafumu otchuka. Motero ndidzaŵabwezera potsata zochita zao ndi ntchito za manja ao.”
Mulungu adzalanga anthu a mitundu ina15Chauta, Mulungu wa Israele, adandiwuza kuti, “Tenga chikho ichi chodzaza ndi mkwiyo wanga, ndipo ukamwetse anthu a mitundu yonse kumene nditi ndikutume.
16Atamwa, adzayamba kudzandira ndipo adzachita misala chifukwa cha nkhondo imene ndikutumiza pakati pao.”
17Tsono ndidalandira chikhocho kumanja kwa Chauta ndipo ndidapatsa anthu a mitundu yonse, kuti amwe monga momwe Chauta adaandilamulira.
18Adandituma ku Yerusalemu, ku mizinda ya ku Yuda, kwa mafumu ake ndi kwa akalonga ake, kuti ndiŵasandutse ngati bwinja, ndi chinthu chonyozeka ndi chomachiseka monga m'mene aliri tsopanomu.
19Adanditumanso kwa Farao, mfumu ya ku Ejipito, kwa nduna zake, kwa akalonga ake, kwa anthu ake onse,
20ndi kwa anthu a mitundu ina yachilendo yokhala pakati pao. Adanditumanso kwa mafumu onse a ku dziko la Uzi, kwa mafumu onse a Afilisti, ndiye kuti ku Asikeloni, ku Gaza, ku Ekeroni ndi ku chigawo chotsala cha ku Asidodi.
21Adanditumanso ku Edomu, ku Mowabu ndiponso kwa Aamoni.
22Adandituma kwa mafumu onse a ku Tiro ndi Sidoni, ndiponso kwa mafumu a maiko a m'mbali mwa nyanja, ndiye kuti
23ku Dedani, ku Tema, ku Buzi ndi kwa onse ometa cham'mbali.
24Adanditumanso kwa mafumu onse a ku Arabiya ndi kwa ena aja okhala m'chipululu.
25Adandituma kwa mafumu onse a ku Zimiri, kwa mafumu onse a ku Elamu, kwa mafumu onse a ku Mediya,
26kwa mafumu onse akumpoto, akufupi ndi akutali omwe, ndi kwa maufumu onse a dziko lonse lapansi. Potsiriza, atamwa onsewo, idzamwe ndi mfumu ya ku Babiloni.
27“Kenaka udzaŵauze kuti, Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, ‘Imwani, muledzere, musanze, mugwe osadzukanso, chifukwa cha nkhondo imene ndikutumiza pakati panu.’ ”
28“Akakana kulandira chikho kumanja kwako kuti amwe, uŵauze kuti, Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, Muyenera kumwa!
29Tsopanotu ndiyamba ndalanga mzinda umene umadziŵika ndi dzina langa. Kodi mukuganiza kuti inuyo simudzalangidwa? Iyai, simungathe kupulumuka. Ndithu, nditumiza nkhondo kwa anthu onse okhala pa dziko lapansi,” akutero Chauta Wamphamvuzonse.
30“Tsono iwe, ulengeze mau oŵatsutsa,
uŵauze kuti,
‘Chauta adzakhuluma kumwamba,
mau ake adzamveka ngati bingu
kuchokera ku malo ake opatulika.
Zoonadi, adzakhuluma, kukalipira anthu ake,
adzafuula kwambiri ngati anthu oponda mphesa,
polimbana ndi anthu onse a pa dziko lapansi.
31Phokoso lalikululo lidzamveka
pa dziko lonse lapansi,
chifukwa Chauta akuŵazenga mlandu
anthu a mitundu yonse.
Akuti aweruza anthu onse,
ndipo oipa adzaphedwa ndi lupanga,
akuterotu Chauta.’ ”
32Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti,
“Onani, tsoka likuti likachoka pa mtundu wina
likukagwa pa mtundu winanso.
Ndipo ku malekezero a dziko lapansi
kukuyambika mphepo yamkuntho.”
33Pa tsiku limenelo, onse ophedwa ndi Chauta adzangoti vuu pa dziko lonse lapansi. Palibe amene adzaŵalire, kapena kukaŵaika m'manda. Adzangosiyidwa ngati ndoŵe ponseponse.
34Inu abusa lirani kwambiri, fuulani kwamphamvu. Inu atsogoleri a anthu anga, dzolani phulusa. Nthaŵi yanu yokaphedwa yafika, ndipo mudzachita kuphedwa ngati nkhosa zamphongo.
35Abusawo adzasoŵa kothaŵira, eniake a nkhosa adzasoŵa njira yopulumukira.
36Mverani, abusa akulira, eniake a nkhosa akulira kwambiri, pakuti Chauta akuwononga busa lao.
37Makola ao a nkhosa, amene adaali pa mtendere, akusanduka mabwinja chifukwa cha ukali woopsa wa Chauta.
38Chauta waŵasiya anthu ake ngati mkango wosiya phanga lake, ndipo dziko lao lasanduka chipululu, chifukwa cha mazunzo a nkhondo ndi mkwiyo woopsa wa Chauta.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.