1 Sam. 23 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Davide apulumutsa mzinda wa Keila.

1Tsiku lina Davide adamva kuti Afilisti akuthira nkhondo mzinda wa Keila, ndipo akufunkha zokolola za m'nkhokwe zao.

2Choncho Davide adafunsa Chauta kuti, “Kodi ndikamenyane nawo nkhondo Afilistiwo?” Chauta adamuuza kuti, “Pita, kamenyane nawo, kuti upulumutse mzinda wa Keila.”

3Koma Davide anthu ake adamuuza kuti, “Ngati tikuchita mantha ku Yuda konkuno, nanga nanji tikapita ku Keila kuti tikamenyane ndi magulu ankhondo a Afilisti? Kodi sitikaopa kwambiri kumeneko?”

4Tsono Davide adapemphanso nzeru kwa Chauta, ndipo adamuyankha kuti, “Nyamuka, upite ku Keila, pakuti ndidzaŵapereka Afilistiwo kwa iwe.”

5Tsono Davide ndi anthu ake aja adapita ku Keila, ndipo adakamenyana nawo Afilistiwo. Adapha ankhondo ambiri nalanda ng'ombe zao. Choncho Davide adapulumutsa anthu amene ankakhala ku Keila.

6Pamene Abiyatara, mwana wa Ahimeleki, adathaŵira kwa Davide ku Keila, adabwera atatenga efodi yaunsembe ija m'manja mwake.

7Saulo atamva kuti Davide wafika ku Keila, adati, “Mulungu wampereka m'manja mwanga. Pamene waloŵa mu mzinda umene uli ndi zipata ndi mipiringidzo yolimba, ndiye kuti wadzimanga yekha.”

8Tsono Saulo adasonkhanitsa ankhondo ake, naŵatuma ku Keila kuti akamzinge Davide pamodzi ndi anthu ake.

9Koma Davide adaadziŵa kuti Saulo akufuna kumchita chiwembu. Choncho adauza wansembe Abiyatara kuti abwere ndi efodi ija.

10Tsono Davide adalankhula ndi Mulungu kuti, “Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, ndithudi, ine mtumiki wanu ndamva kuti Saulo akufunafuna kubwera kuno ku Keila, kuti adzaononge mzindawu chifukwa cha ine.

11Kodi anthu a ku Keila adzandipereka kwa Saulo? Kodi Saulo adzabweradi monga m'mene ine mtumiki wanu ndamvera? Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, ndikukupemphani kuti mundiwuze, ine mtumiki wanu.” Chauta adati, “Saulo abweradi.”

12Tsono Davide adafunsanso kuti, “Kodi anthu a ku Keila adzandipereka ine ndi anthu anga kwa Saulo?” Chauta adati, “Inde adzakupereka.”

13Pamenepo Davide, pamodzi ndi ankhondo ake amene analipo ngati 600, adachokako ku Keila, namayenda chothaŵathaŵa. Saulo atamva kuti Davide wathaŵa ku Keila, adaleka zoŵatuma ankhondo aja.

14Davide ankabisala m'mapanga m'dziko lamapiri ku chipululu cha Zifi. Monsemo Saulo ankamufunafuna, koma Mulungu sadalole kuti agwidwe ai.

Davide achezerana ndi Yonatani ku Horesi.

15Davide adaona kuti Saulo akumfunafuna kuti amuphe. Pa nthaŵiyo Davide anali ku chipululu cha Zifi ku Horesi.

16Tsono Yonatani, mwana wa Saulo, adanyamuka napita kwa Davide ku Horesi, ndipo adamlimbitsa mtima pomuuza kuti Mulungu adzamteteza.

17Yonatani adauza Davide kuti, “Usaope, abambo anga sadzakupha. Udzakhala mfumu ya Aisraele, ndipo ine ndidzakhala wachiŵiri kwa iwe. Abambo angawo akudziŵanso zimenezi.”

181Sam. 18.3Pamenepo aŵiriwo adachita chipangano pamaso pa Chauta. Choncho Davide adakhalabe ku Horesi, ndipo Yonatani adabwerera kwao.

19 Mas. 54 Tsono anthu a ku Zifi adapita kwa Saulo ku Gibea, nakamuuza kuti, “Davide akubisala ku dera lakwathu m'mapanga a ku Horesi pa phiri la Hakila limene lili kumwera kwa Yesimoni.

20Tsono inu amfumu, ife tadziŵa kuti mukumfunafuna kwambiri, choncho bwerani ndithu. Ifeyo tidzampereka kwa inu.”

21Apo Saulo adati, “Chauta akudalitseni, pakuti mwandikomera mtima.

22Pitani mukaonetsetse. Mukafufuze kumene kuli mbuto yake, ndi kupeza munthu amene wamuwona chamaso kumeneko. Ndikumva kuti ngwochenjera mwaukapsala.

23Nchifukwa chake muwone malo onse amene amabisalako, ndipo mubwerenso kuno kuti mudzandiwuze chenicheni. Tsono ndidzapita nanu. Ndipo ngati alidi kumeneko, ndidzamfunafuna pakati pa anthu onse m'dziko lonse la Yuda.”

24Anthuwo adabwerera ku Zifi, Saulo asananyamuke.

Pa nthaŵiyo Davide ndi anthu ake anali ku chipululu cha Maoni ku Araba, kumwera kwa Yesimoni.

25Tsono Saulo ndi anthu ake adapita kukamfunafuna Davide, koma iye anali atazimva. Nchifukwa chake adathaŵa napita ku thanthwe la ku chipululu cha Maoni. Saulo atamva kuti Davide adathaŵira ku Maoni, adamlondola kuchipululu komweko.

26Saulo adadzera mbali ina ya phiri, Davide ndi anthu ake adadzeranso mbali ina ya phirilo. Tsono Davide ndi anthu ake adafulumira kuthaŵa, pamene Saulo ndi anthu ake anali pafupi kuŵagwira.

27Nthaŵi yomweyo padafika wamthenga amene adauza Saulo kuti, “Mufulumire kubwera, pakuti Afilisti akulithira nkhondo dzikoli.”

28Choncho Saulo adalekeza kulondola Davide, napita kukamenyana ndi Afilisti. Nchifukwa chake malo amenewo adaŵatchula Mwala wa malekano.

29Davide adachoka kumeneko, nakhala m'mapanga a ku Engedi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help