1 Sam. 12 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Samuele alaŵirana ndi anthu.

1Pambuyo pake Samuele adauza Aisraele onse kuti, “Ndidamvera zonse zimene mudandiwuza, ndipo ndakupatsani mfumu kuti izikulamulirani.

2Tsopano mfumu ndiyo izikutsogolerani. Ine nkukalamba kuno, kumutuku imvi zati mbuu, ndipo ana anga muli nawo pamodzi. Ndakhala ndikukutsogolerani kuyambira ndili mnyamata mpaka pano.

3Mphu. 46.19Ine ndili pompano, ngati chilipo chimene ndidalakwa, munditsutsiretu tsopano pamaso pa Chauta ndi pamaso pa wodzozedwa wake. Kodi ndani ndidamulandapo ng'ombe? Ndani ndidamulandapo bulu? Ndani ndidamdyererapo? Kodi ndani amene ndidamuzunza? Kodi nkwa yani ndidalandirapo chiphuphu choti nkundidetsa m'maso? Tsimikizeni, ndipo ndikubwezerani zonse.”

4Anthuwo adati, “Simudatidyerere, kapena kutizunza, ngakhale kutenga kanthu kalikonse ka munthu.”

5Apo Samuele adaŵauza kuti, “Chauta ndiye mboni pakati pa ine ndi inu, nayenso wodzozedwa wa Chauta ndiye mboni lero lino kuti simudandipeze chifukwa chilichonse.” Ndipo iwo adati, “Zoonadi, Chauta ndiye mboni.”

6 Eks. 6.26 Samuele adaŵauzanso kuti, “Chauta ndiye amene adasankha Mose ndi Aroni, kuti atulutse makolo anu m'dziko la Ejipito.

7Nchifukwa chake tsono imani pomwepa, kuti tikumbutsane pamaso pa Chauta za ntchito zonse zimene Iye adachita pokupulumutsani inu ndi makolo anu.

8Eks. 2.23 Pamene Yakobe ndi banja lake adapita ku dziko la Ejipito, Aejipito namaŵazunza, pamenepo makolo anuwo adadandaula kwa Chauta. Ndipo Chauta adatuma Mose ndi Aroni kuti aŵatulutse ku Ejipito ndi kudzaŵakhazika ku malo ano.

9Owe. 4.2; Owe. 13.1; Owe. 3.12 Koma makolo anuwo adaiŵala Chauta, Mulungu wao. Ndipo Mulungu adaŵapereka m'manja mwa Sisera, mtsogoleri wa ankhondo a mzinda wa Hazori. Adaŵaperekanso m'manja mwa Afilisti ndi m'manja mwa mfumu ya ku Mowabu. Adani onsewo adachita nkhondo ndi makolo anuwo.

10Owe. 10.10-15 Tsono iwowo adadandaula kwa Chauta nati. ‘Ife tachimwa chifukwa choti tasiya Inu Chauta, ndipo tatumikira mafano aja a Baala ndi Asitaroti. Koma tsopano tipulumutseni kwa adani athu, ndipo tidzakutumikirani.’

11Owe. 7.1; Owe. 4.6; Owe. 11.29; 1Sam. 3.20 Choncho Chauta adatuma Yerubaala, Balaki, Yefita ndi ine Samuele. Tidakupulumutsani kwa adani anu amene ankakuzingani, ndipo mudakhala pa mtendere.

121Sam. 8.19 Tsono pamene mudaona kuti Nahasi, mfumu ya Aamoni, adadza kuti adzamenyane nane, mudandiwuza kuti, ‘Iyai, koma mfumu ndiyo imene idzatilamulire,’ chonsecho mfumu yanu inali Chauta, Mulungu wanu.

13“Tsopano nayi mfumu imene mudaisankha, imene mudachita kuipempha ija. Ndiyo imene Chauta wakupatsani.

14Mukamaopa Chauta ndi kumamtumikira ndi kumamvera mau ake, osakana malamulo ake, ndiponso ngati nonsenu pamodzi ndi mfumu yanu mudzatsata Chauta, Mulungu wanu, zonse zidzakuyenderani bwino.

15Koma mukapanda kumvera mau a Chauta nkumakana malamulo ake, ndiye kuti Iye adzakulangani inu ndi mfumu yanu yomwe.

16Nchifukwa chake tsono imani pomwepa, muwone chinthu chachikulu chimene Chauta akuchitireni mukupenya.

17Kodi ino si nthaŵi yachilimwe yodula tirigu? Komabe nditama Chauta mopemba kuti agwetse mvula yamabingu. Apo mudziŵa ndi kuwona kuti tchimo lanu limene mwachita popempha mfumu kwa Chauta nlalikulu.”

18Choncho Samuele adatama Chauta mopemba, ndipo Chauta adatumizadi mvula yamabingu tsiku limenelo. Motero anthu onse adagwidwa ndi mantha aakulu oopa Chauta ndi Samuele.

19Pamenepo anthu onse adauza Samuele kuti, “Chonde mutipempherere ife atumiki anu kwa Chauta, Mulungu wanu, kuti tingafe, pakuti pa machimo athu onse taonjezapo tchimo limeneli lopempha kuti tikhale ndi mfumu.”

20Samuele adaŵauza kuti, “Musaope. Kuchimwa mwachimwadi, komabe musaleke kutsata Chauta. Muzimtumikira ndi mtima wanu wonse.

21Ndipo musatsate mafano achabe amene alibe phindu, amene sangathe kupulumutsa poti ngopandapake.

22Chauta sadzataya anthu ake, kuti dzina lake lalikulu linganyozeke, poti chidamukondweretsa kuti akusandutseni anthu ake.

23Komanso kunena za ine, sindifuna kuchimwira Chauta, pakuleka kukupemphererani. Ndidzakuphunzitsani zimene zili zabwino ndi zolungama kuti muzizichita.

24Muzingoopa Chauta, ndipo muzimtumikira mokhulupirika ndi mtima wanu wonse. Nthaŵi zonse muziganizira zazikulu zimene wakhala akukuchitirani.

25Koma mukamachitabe zoipa, ndiye kuti inuyo pamodzi ndi mfumu yanu mudzaonongedwa.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help