1Pamene Balamu adaona kuti zinali zokondwetsa Chauta kuti adalitse Aisraele, sadapite monga nthaŵi zina zija kukafunsa kuti adziŵe zimene Mulungu akufuna, koma adangotembenuka nayang'ana ku chipululu.
2Adaona Aisraele ali m'mahema mwao, fuko lililonse pa lokha. Tsono mzimu wa Mulungu udatsika pa iye,
3ndipo adayamba kulankhula mau auneneri, adati,
“Mau a Balamu mwana wa Beori,
mau a munthu amene maso ake ndi otsekuka,
4munthu amene akumva mau a Mulungu,
munthu amene akuwona Mphambe m'masomphenya,
munthu amene akugwa pansi,
koma maso ali chipenyere.
5Mahema ako, iwe Yakobe,
nyumba zako, iwe Israele, si kukoma kwake!
6Anthu ako ali ngati zigwa zofika patali,
ali ngati minda ya m'mbali mwa mtsinje,
ali ngati khonje amene Chauta adabzala,
ali ngati mitengo ya mkungudza yomera m'mbali mwa madzi.
7Madzi adzasefukira m'zotungira zao,
ndipo mbeu zao zidzakhala ndi madzi ambiri,
mfumu yao idzakhala yotchuka kupambana Agagi,
ndipo ufumu wake udzakwezedwa.
8Mulungu adaŵatulutsa m'dziko la Ejipito.
Ali ndi mphamvu zonga za njati,
adzapha mitundu ya adani ao,
adzaswa mafupa ao ndi kuŵaboola ndi mivi yao.
9 Gen. 49.9; Gen. 12.3 Adamyata, nagona pansi ngati mkango
ngati mkango wamphongo kapena waukazi.
Kodi amuutse ndani?
Ndi wodala munthu amene aŵadalitsa,
ndi wotembereredwa munthu amene aŵatemberera.”
10Apo Balaki adapsera mtima Balamu, ndipo adaomba m'manja. Tsono Balakiyo adauza Balamu kuti, “Paja ndidakuitanani kuti mudzatemberere adani anga, ndipo inu mwaŵadalitsa katatu konseka.
11Nchifukwa chake, chokani, kazipitani kwanu. Ndidaakuuzani kuti ndidzakupatsani mphotho, koma Chauta wakana kuti muilandire mphothoyo.”
12Balamu adafunsa Balaki kuti “Kodi amithenga anu amene mudaŵatuma kwa ine aja, sindidaŵauze kuti,
13‘Ngakhale Balaki andipatse nyumba yake yodzaza ndi siliva ndi golide, sindidzatha kuchita zosiyana ndi zimene Chauta wandiwuza. Sindidzachita zabwino kapena zoipa mwa kufuna kwanga. Ndidzalankhula zimene Chauta adzandiwuze?’ ”
Mau otsiriza auneneri a Balamu14Balamu adauza Balaki kuti, “Tsopano ndikupita kwa anthu anga. Bwerani kuno, ndikudziŵitseni zimene Aisraeleŵa adzaŵachite anthu anu masiku akudzaŵa.”
15Ndipo adayambapo kulankhula mau auneneri adati,
“Mau a Balamu mwana wa Beori,
mau a munthu amene maso ake ndi otsekuka,
16munthu amene akumva mau a Mulungu,
ndipo akudziŵa nzeru zake za Wopambanazonse,
munthu amene akuwona Mphambe m'masomphenya,
munthu amene akugwa pansi,
koma maso ake ali chipenyere.
17Ndikupenya mtsogolo,
ndipo ndikuona mtundu wa Israele.
Mfumu yonga nyenyezi idzatuluka mwa Yakobe,
ndodo yaufumu idzadzuka mwa Israele,
idzatswanya atsogoleri a Mowabu,
ndipo idzagonjetseratu mtundu wa Seti.
18Dziko la Edomu lidzalandidwa,
Seiri mdani wake adzagonjetsedwa,
pamene Aisraele adzakhala akupambanabe.
19Mwa Yakobe mudzatuluka mfumu yolamulira,
imene idzaononga otsala mu mzinda.”
20Tsono Balamu adayang'ana Amaleke,
ndipo adayamba kulankhula nati,
“Mtundu wa Amaleke udaali wopambana mitundu ina yonse,
koma potsiriza pake udzaonongeka.”
21Kenaka adayang'ana Akeni,
tsono adayamba kulankhula nati,
“Ngakhale malo amene mukukhalawo ngopanda zovuta,
monga chisa chomangidwa pa thanthwe,
22komabe mudzaonongeka inu ana a Kaini,
mudzakhala mu ukapolo wa Asuri nthaŵi yaitali.”
23Adayamba kulankhulanso nati,
“Kalanga ine, ndani akhale moyo,
Mulungu akachita zimenezi?
24Zombo zidzabwera kuchokera ku Kitimu,
zidzaononga Asuri ndi Eberi.
Kitimu nayenso adzaonongeka.”
25Tsono Balamu adanyamuka nabwerera kwao.
Balaki nayenso adapita kwao.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.