1Nthaŵi ina, Amowabu, Aamoni ndi Ameuni ena adabwera kudzamenyana nkhondo ndi Yehosafati.
2Anthu ena adadzauza Yehosafati kuti “Chinamtindi cha anthu chikudzamenyana nanu nkhondo, kuchokera ku Edomu patsidya pa nyanja. Anthuwo ali ku Hazazoni-Tamara,” (ndiye kuti Engedi).
3Pamenepo Yehosafati adachita mantha, ndipo adaganiza zopempha nzeru kwa Chauta, nalengeza kuti anthu onse a ku dziko la Yuda asale zakudya.
4Ayuda onse adasonkhana kuti adzapemphe chithandizo kwa Chauta. Anthu onse a ku mizinda yonse ya ku Yuda adabwera kudzapempha chithandizo kwa Chauta.
5Tsono Yehosafati adaimirira pakati pa msonkhano wa Ayuda ku Yerusalemu m'Nyumba ya Chauta pa bwalo latsopano.
6Ndipo adati, “Chauta, Mulungu wa makolo athu, kodi Inu sindinu Mulungu Wakumwamba? Kodi suja mumalamulira maufumu onse a mitundu ya anthu? M'manja mwanu muli mphamvu ndi nyonga, kotero kuti palibe ndi mmodzi yemwe woti nkulimbana nanu.
7Yes. 41.8; Yak. 2.23 Kodi Inu, Mulungu wathu, suja mudapirikitsa nzika za dziko lino pamene ankafika Aisraele, anthu anu, ndi kulipereka kwa zidzukulu za Abrahamu, bwenzi lanu mpaka muyaya?
8Mwakuti iwo atakhazikika m'dziko limenelo, adakumangirani Nyumba m'menemo, nkumati,
9‘Choipa chikatigwera mwachilango, monga nkhondo, mlili kapena njala, tidzaima m'Nyumba ino ndiponso pamaso panu, popeza kuti dzina lanu lili m'Nyumba muno. Tsono tidzalira kwa Inu pa mavuto athu, Inuyo mudzamva, ndipo mudzatipulumutsa.’
10Deut. 2.4-19 Pajatu pamene Aisraele ankachoka ku Ejipito, simudalole kuti aŵathire nkhondo Aamoni, Amowabu ndi anthu a ku phiri la Seiri. Onsewo adaŵaleka osaŵaononga.
11Koma tsopano chimene akutibwezera nkudzatipirikitsa m'dziko limene Inu mudatipatsa kuti likhale choloŵa chathu.
12Inu Mulungu wathu, monga simuŵalanga iwoŵa? Ife tilibe mphamvu zoti nkulimbana nacho chinamtindi chikudzatithira nkhondocho. Tikusoŵa chochita, maso athu ali pa Inu.”
13Nthaŵi imeneyo nkuti anthu onse a dziko la Yuda ataimirira pamaso pa Chauta, pamodzi ndi akazi ao ndi ana ao ndi ang'onoang'ono omwe.
14Ndipo mumsonkhanomo mzimu wa Chauta udatsikira Yehaziele, mwana wa Zekariya, mwana wa Benaya, mwana wa Yeiyele, mwana wa Mataniya, mlevi, mmodzi mwa ana a Asafu.
15Deut. 20.1-4 Iyeyo adati, “Mverani Ayuda nonsenu, ndi inu nonse okhala ku Yerusalemu, ndi inunso mfumu Yehosafati. Chauta akukuuzani kuti, ‘Musaope, ndipo musataye nacho mtima chinamtindi cha anthuchi, pakuti nkhondo si yanu, nja Mulungu.
16Maŵa mupite mukamenyane nawo nkhondo. Adzabwera ndipo adzadzera cha ku chikwera cha Zizi. Mudzaŵapeza pafupi ndi chigwa cha kuvuma kwa chipululu cha Yeruwele.
17Eks. 14.13, 14 Sikudzafunika kuti mumenyane nawo pa nkhondo imeneyi. Inu mukhale m'malo mwanu, mungoima, ndipo muwonerere Chauta akukumenyerani nkhondo, inu anthu a ku Yuda ndi inu anthu a mu Yerusalemu.’ Musaope ndipo musataye mtima, mutuluke maŵa mukalimbane nawo, Chauta adzakhala nanu.”
18Apo Yehosafati adazyolikitsa nkhope yake pansi, ndipo anthu onse a ku Yuda ndi anthu onse a ku Yerusalemu adagwa pansi pamaso pa Chauta nampembedza.
19Kenaka Alevi, ana a Kohati ndi ana a Kora, adaimirira kuti atamande Chauta, Mulungu wa Aisraele, mokweza kwambiri.
20Tsono anthuwo adadzuka m'mamaŵa nakaloŵa m'chipululu cha ku Tekowa. Pamene ankatuluka, Yehosafati adaima nati, “Tamverani inu anthu a ku Yuda ndi inu okhala mu Yerusalemu. Khulupirirani Chauta, Mulungu wanu, ndipo mudzalimbika, khulupirirani aneneri ake, ndipo mudzapambana.”
21Tsono ataŵafunsa anthuwo, adasankha ena oti aziimbira Chauta ndi kumtamanda, oimbawo atavala zovala zoyera, akutsogolera gulu lankhondo namanena kuti,
“Thokozani Chauta,
pakuti chikondi chake chosasinthika
chimakhala mpaka muyaya.”
22Iwo aja atayamba kuimba ndi kutamanda, Chauta adaŵatchera msampha Aamoni, Amowabu ndiponso anthu a ku phiri la Seiri, amene adaadzalimbana ndi anthu a ku Yuda, kotero kuti adaŵagonjetsa onse.
23Aamoni ndi Amowabu adaukira anthu okhala ku phiri la Seiri, naŵaononga kotheratu. Ndipo ataononga anthu onse a ku Seiri aja, adayamba kumaphana okhaokha.
24Pambuyo pake anthu a ku Yuda atafika ku nsanja yakuchipululu, adapenya kumene kunali chinamtindi cha anthu chija. Adangoona mitembo yokhayokha ili pansi ngundangunda. Panalibe ndi mmodzi yemwe wopulumuka.
25Tsono Yehosafati ndi anthu ake atadzafunkha za anthuwo, adapeza ng'ombe zambirimbiri, katundu, zovala ndiponso zinthu zamtengowapatali. Adatenga zinthu zochuluka, mpaka kuzilephera. Adafunkha zinthuzo masiku atatu, chifukwa zinali zambirimbiri.
26Pa tsiku lachinai lake, adasonkhana ku chigwa cha Beraka, ndipo kumeneko adatamanda Chauta. Nchifukwa chake malowo amatchedwa chigwa cha Beraka mpaka lero lino.
27Tsono onsewo a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu adabwerera mokondwa ku Yerusalemu, Yehosafati akuŵatsogolera, pakuti Chauta adaŵakondweretsa poŵagonjetsera adani ao.
28Anthuwo adafika ku Yerusalemu, ku Nyumba ya Chauta, akuimba azeze, apangwe ndiponso malipenga.
29Ndipo maufumu onse a m'maiko achilendowo adachita mantha kwambiri, atamva kuti Chauta ndiye adathira nkhondo pa adani a Aisraele.
30Motero mudakhala bata mu ufumu wonse wa Yehosafati, pakuti Mulungu adampatsa mtendere ku maiko onse omzungulira.
Kutha kwa ufumu wa Yehosafati(1 Maf. 22.41-50)31Choncho Yehosafati adayamba kulamulira Yuda. Anali wa zaka 35 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 25 ku Yerusalemu. Mai wake anali Azuba, mwana wa Sili.
32Yehosafati ankayenda motsata chitsanzo chabwino cha Asa atate ake. Sadapatuke pa zimenezo. Ankachita zolungama pamaso pa Chauta.
33Komabe akachisi opembedzerako mafano sadaŵaononge. Anthu anali asanapereke mitima yao kwa Mulungu wa makolo ao.
34Tsono ntchito zonse zimene adachita Yehosafati kuyambira poyamba mpaka potsiriza, zidalembedwa m'buku la mbiri ya Yehu, mwana wa Hanani, limene lili chigawo cha buku lokamba za mafumu a Aisraele.
35Zitapita zimenezi, Yehosafati mfumu ya ku Yuda, adagwirizana ndi Ahaziya mfumu ya ku Israele, amene ankachita zoipa kwambiri.
36Adagwirizana naye pomanga zombo zomapita ku Tarisisi ndipo zombozo ankazimangira ku Eziyoni-Gebere.
37Tsono Eliyezere mwana wa Dodavahu wa ku Maresa, adalosa zoipira Yehosafati adati, “Chifukwa chakuti mwagwirizana ndi Ahaziya, Chauta adzaononga zimene mwapangazo.” Ndipo zombozo zidaonongekadi zosakafika ku Tarisisi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.