Deut. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Aisraele agonjetsa mfumu Ogi(Num. 21.31-35)

1Pambuyo pake tidapitirira ulendo kulunjika ku Basani. Mfumu Ogi pamodzi ndi anthu ake onse, adatuluka kudzatithira nkhondo pafupi ndi mudzi wa Ederei.

2Koma Chauta adandiwuza kuti, “Usamuwope, poti iyeyo, anthu ake, pamodzi ndi dziko lake lomwe, ndakupatsa iwe. Umchite zomwe udachita Sihoni, mfumu ya Aamori, amene ankalamulira ku Hesiboni.”

3Motero Chauta adapereka mfumu Ogi ndi anthu ake m'manja mwathu, ndipo tidaŵapha onsewo osatsalapo ndi mmodzi yemwe.

4Tidalandanso mizinda yake yonse nthaŵi yomweyo, sitidasiyeko ndi umodzi womwe. Mizinda yonse imene tidalanda inali makumi asanu ndi limodzi, dera lonse la Arigobu, kumene mfumu Ogi wa ku Basani ankalamulira.

5Mizinda yonseyi inali yotchinjirizidwa ndi malinga ataliatali, ndiponso ya zipata zokhala ndi mipiringidzo yake. Panalinso midzi yambirimbiri yopanda malinga.

6Tidaononga midziyo ndi mizinda yonse, ndipo tidapha onse amuna ndi akazi ndi ana omwe, monga momwe tidachitira mizinda ya mfumu Sihoni wa ku Hesiboni.

7Kenaka tidafunkha zoŵeta ndi chuma cha m'mizinda yonseyo.

8Tsono pa nthaŵi imeneyo mafumu aŵiri a Aamoriwo tidaŵalanda dziko patsidya pa Yordani, kuchokera ku chigwa cha mtsinje wa Arinoni mpaka ku phiri la Heremoni.

9(Asidoni potchula phiri la Heremoni ankati Sirioni, koma Aamori potchula phiri lomwelo ankati Seniri.)

10Tidalandanso mizinda yakumapiri, dziko lonse la Giliyadi ndi Basani, mpaka ku Saleka ndi Ederei, mizinda ya ufumu wa Ogi ku Basani.

11(Ogi yekha, mfumu ya ku Basani, ndiye amene adatsala mwa Arefaimu. Kama lake linali lachitsulo, m'litali mwake linali la mamita anai, muufupi mwake mamita aŵiri, polinganiza ndi miyeso ya nthaŵi imeneyo. Kamalo angathe kuchiwonabe ku Raba, mzinda wa Aamoni.)

Mafuko amene adakhala kuvuma kwa Yordani(Num. 32.1-42)

12Dzikolo titalanda, ndidagaŵira fuko la Rubeni ndi la Gadi dera lija kuyambira ku Aroere, pafupi ndi mtsinje wa Arinoni, ndiponso theka la dziko lamapiri la Giliyadi, pamodzi ndi mizinda yake.

13Theka la fuko la Manase, ndidalipatsa dera lonse la Giliyadi limene lidatsalira, ndiponso Basani dziko la mfumu Ogi uja, ndiye kuti dera lonse la Arigobu. (Basani linkadziŵika ndi dzina loti dziko la Arefaimu.

14Yairi, wa fuko la Manase, adatenga dera lonse la Arigobu, ndiye kuti Basani, mpaka kukafika ku malire a Gesuri ndi Maaka. Mizindayo adaitchula dzina lake, ndipo mpaka lero lino, imadziŵika kuti ndi ya Yairi.)

15Dziko la Giliyadi ndidalipereka kwa Makiri wa fuko la Manase.

16Dziko lonse kuchokera ku Giliyadi mpaka ku chigwa cha Arinoni, ndidapatsa fuko la Rubeni ndi la Gadi. Pakatimpakati pa chigwa cha Arinoni ndiye panali malire akumwera, ndipo malire ake akumpoto anali mtsinje wa Yaboki, umene mbali yake inali malire a dziko la Aamoni.

17Chakuzambwe dziko lao linkafika mpaka ku mtsinje wa Yordani, kuchokera ku Kinereti kumpoto, mpaka kukafika ku Nyanja ya Araba, ndiye kuti Nyanja yamchere kumwera. Ndipo chakuvuma linkafika pa tsinde la phiri la Pisiga.

18 Yos. 1.12-15 Pa nthaŵi imeneyo ndidaakulamulani kuti, “Chauta, Mulungu wathu, ndiye wakupatsani dzikoli kuti likhale lanu. Amuna onse otha kumenya nkhondo atenge zida ndipo atsogolere abale anu, mafuko a Aisraele.

19Koma akazi anu okha ndi ana anu adzakhalira m'mizinda imene ndidakupatsani, pamodzi ndi ng'ombe zanu zomwe. (Ndikudziŵa kuti muli ndi ng'ombe zambiri.)

20Muŵathandize Aisraele anzanu mpaka akhazikike mwamtendere m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu waŵapatsa kuzambwe kwa Yordani, monga momwe Chauta adakuchitirani inu. Pambuyo pake aliyense mwa inu adzabwere ku dera limene ndidakupatsani.”

21Pamenepo ndidauza Yoswa kuti, “Wapenya zonse zimene Chauta, Mulungu wanu, adaŵachita mafumu aŵiri aja Sihoni ndi Ogi. Tsono ena onse amene muŵathire nkhondo m'maiko ao, adzaŵachita chimodzimodzi.

22Musaŵaope, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene adzaponye nkhondo pamodzi nanu.”

Mose saloledwa kuloŵa m'Kanani

23 Num. 27.12-14; Deut. 32.48-52 Pa nthaŵi imeneyo, ndidapemphera kwa Chauta kuti,

24“Inu Ambuye Chauta, mwangondiwonetsa chiyambi chake chokha cha ntchito za ukulu wanu ndi mphamvu zanu. Kumwambako, ngakhalenso pansi pano, palibe Mulungu wina amene angathe kuchita zinthu zamphamvu zonga zimene inu mumachita.

25Inu Chauta, mundilole kuti ndingooloka mtsinje wa Yordani wokhawu, ndipo kuti ndiwone dziko labwinolo patsidyapo, dziko lokongola lamapiri, ndiponso mapiri a Lebanoni.”

26Koma Chauta anali wondikwiyira ine chifukwa cha inu, ndipo sadandimvere konse. M'malo mwake adangoti, “Pakwana! Usanenenso zimenezi!

27Kwera pa nsonga ya phiri la Pisiga, ndipo uyang'ane kumpoto ndi kumwera, kuvuma ndi kuzambwe. Uyang'anitsitse bwino zimene uziwonezo, chifukwa iwe suwoloka Yordani.

28Koma umlangize bwino Yoswayu ndi kumlimbitsa mtima, chifukwa iyeyu ndiye atsogolere anthuŵa kuwoloka mpaka tsidya linalo, ndi kukakhala m'dziko limene udzaliwonalo.”

29Motero tidatsalira ku chigwa, moyang'anana ndi mzinda wa Betepeori.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help