1Pa mwezi woyamba, mpingo wonse wa Aisraele udafika ku chipululu cha Zini, ndipo anthuwo adakhala ku Kadesi. Miriyamu adafera kumeneko naikidwa komweko.
2 kumene Aisraele adakangana ndi Chauta, ndipo Chauta adadziwonetsa pakati pa anthuwo kuti ndi woyera.
Mfumu ya ku Edomu ikaniza Aisraele kudzera m'dziko mwake14Ali ku Kadesi, Mose adatuma amithenga kwa mfumu ya ku Edomu kuti akanene kuti, “Abale anu Aisraele akuti, ‘Mukudziŵa mavuto onse amene atigwera,
15Pajatu makolo athu adaapita ku Ejipito, ndipo tidakhala kumeneko zaka zambiri. Aejipito adatizunza ife ndi makolo athu.
16Titalira kwa Chauta, adamva kulira kwathu, natuma mngelo amene adatitulutsa m'dziko la Ejipitolo. Tsopano tili kuno ku Kadesi, mzinda umene uli m'malire a dziko lanu.
17Mutilole tsono tidzere m'dziko mwanu. Sitidzera m'minda mwanu kapena m'mipesa mwanu. Ndipo sitidzamwa madzi a m'zitsime zanu. Tidzangodzera mu mseu wanu waukuluwo basi, mpaka titadutsa dziko lanu.’ ”
18Koma Edomu adayankha kuti, “Musadzere kuno, kuti ndingafike kudzakubayani ndi lupanga.”
19Aisraele adamuuza kuti, “Ife tidzangodzera mu mseu waukulu mokhamo. Ngati ife ndi zoŵeta zathu timwako madzi anu, tidzalipira. Mungotilola kuti tidutse chabe.”
20Koma Edomu adaŵayankha kuti, “Simudutsa ai.” Pamenepo Edomu adatuluka ndi gulu lankhondo lalikulu ndi lamphamvu kukalimbana ndi Aisraele.
21Motero Edomu sadavomere kuti Aisraele adutse m'dziko mwake. Ndipo Aisraele adadzera njira ina.
Za imfa ya Aroni22Tsono mpingo wonse wa Aisraele udanyamuka ku Kadesi kuja nukafika ku phiri la Horo.
23Ku phiri limenelo, limene lili m'malire a dziko la Edomu, Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti,
24“Aroni saloŵa nao m'dziko limene ndidapatsa Aisraele. Adzafa, chifukwa choti nonse aŵirinu simudamvere lamulo langa ku madzi a ku Meriba kuja.
25Utenge Aroni pamodzi ndi Eleazara mwana wake, ukwere nawo pamwamba pa phiri la Horo.
26Kumeneko umvule Aroni zovala zaunsembe ndi kuveka mwana wake Eleazara. Ndipo Aroni adzafera komweko.”
27Mose adachitadi zimene Chauta adamlamula. Atatu onsewo adakwera phiri la Horo, mpingo wonse ukupenya.
28Eks. 29.29; Num. 33.38; Deut. 10.6 Apo Mose adamuvula Aroni zovala zake zaunsembe, naveka Eleazara mwana wake. Ndipo Aroni adafera pamwamba pa phiri pomwepo. Tsono Mose ndi Eleazara adatsika phiri.
29Pamene mpingo udamva kuti Aroni wamwalira, mpingo wonse wa Israele udalira maliro a Aroni masiku makumi atatu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.