1Chauta akunena kuti,
“Mverani tsopano, inu am'banja la Yakobe.
Inu Aisraele, ndinu atumiki anga, osankhidwa anga.
2Ine ndine Chauta amene ndidakulengani
ndi kukuumbani m'mimba mwa amai anu,
amenenso ndinkakuthandizani.
Usaope iwe Yakobe, mtumiki wanga.
Inu ndinu anthu anga okondedwa
amene ndidakusankhulani.
3Ndidzathira madzi pa dziko louma,
ndidzayendetsa mitsinje m'chipululu.
Ndidzatumizira ana anu Mzimu wanga,
ndidzatsitsa madalitso anga pa zidzukulu zanu.
4Iwo adzakula bwino ngati udzu wothirira bwino,
ngati misondodzi yomera m'mbali mwa mitsinje.
5Wina adzanena kuti ‘Ine ndine wa Chauta,’
wina adzadzitchula wa m'banja la Yakobe.
Winanso adzalemba padzanja pake kuti, ‘Wa Chauta,’
ndipo adzadzitchula wa m'banja la Israele.”
6 Yes. 48.12; Chiv. 1.17; 2.8; 22.13 Chauta, Mfumu ndi Momboli wa Israele,
Chauta Mphambe, akunena kuti,
“Ine ndine woyamba ndi womaliza.
Palibenso Mulungu wina, koma Ine ndekha.
7Ndani nanga akulingana ndi Ine?
Aimirire, alankhule, andifotokozere.
Kuyambira kalekale ndani adalosa zakutsogolo?
Atidziŵitsetu zimene zikudzachitika.
8Musadedere, musaope.
Suja kuyambira kale lomwe ndakhala
ndikukuuzani ndi kutsimikiza zimenezi?
Inuyo ndinu mboni zanga.
Kodi aliponso Mulungu wina kupatula Ine?
Iyai, palibenso Thanthwe lina,
sindikudziŵa lina lililonse.”
Anyoza opanga mafano9Onse amene amapanga mafano ngachabe, milungu imene amailemekeza kwambiri ndi yopanda phindu. Amene amaipembedza ndi akhungu ndi osadziŵa kanthu, choncho adzaŵachititsa manyazi.
10Phindu lake nchiyani kupanga kamulungu kapena kusungunula fano lachabechabe?
11Onse opembedza fanolo adzaŵachititsa manyazi. Opanga mafano ndi anthu chabe. Onse asonkhane, aonekere ku bwalo la milandu. Onsewo adzaopsedwa, ndipo adzachita manyazi.
12Mmisiri wa zitsulo amatenga chitsulo nachiika pa moto. Ndi dzanja lake lamphamvu amachisula pakuchimenya ndi nyundo. Pambuyo pake amamva njala natha mphamvu, akapanda kumwa madzi, amalefuka.
13Mmisiri wa matabwa amayesa mtengo ndi chingwe. Amalembapo chithunzi ndi cholembera, nachizokota ndi zipangizo zake. Amachipanga ngati munthu, munthu wake wokongola, kuti achiike m'nyumba ya chipembedzo.
14Amagwetsa mitengo ya mkungudza. Mwinanso amasankhula mtengo wa paini kapena wa thundu ku nkhalango. Mwina mwake amabzala mtundu wina wa paini ndipo umakula ndi mvula.
15Lun. 13.11-19Mtengowo munthu amachitako nkhuni. Nthambi zina amasonkhera moto wootha, zina moto wophikapo buledi. Chigawo china cha mtengowo amapangira kamulungu nayamba kukapembedza. Amapanga fano namaligwadira.
16Chigawo china amasonkhera moto wootchapo nyama imene amadya mpaka kukhuta. Amaothanso motowo namanena kuti, “Aha! Ndikumva kufunda! Ati kukoma motowu ati!”
17Ndi chigawo chotsala amapanga kamulungu kake, fano lake limenelo. Amaliŵeramira ndi kumalipembedza. Amapemphera kwa fanolo namanena kuti, “Iwe ndiwe mulungu wanga, undipulumutse.”
18Anthu otere sadziŵa kanthu ndipo samvetsa konse. Maso ao ndi omatirira, sangathe kupenya. Nzeru zaonso nzogontha, sangathe kumvetsa.
19Palibe wolingalira, palibe wanzeru kapena womvetsa woti anganene kuti, “Chigawo china cha mtengo ndidatentha pa moto, pa makala ake ndidaphikapo buledi, ndidaotchapo nyama ndipo ndidadya. Tsopano chigawo chotsalachi ndipangira chinthu chonyansa! Monga ine ndizipembedza mtengo?”
20Munthuyo akuchita ngati kudya phulusa, maganizo ake opusa amsokeretsa kotero kuti sangapulumutsenso moyo wake. Sangathenso kudzifunsa kuti, “Kodi chinthu chili m'manja mwangachi si chabodza?”
Chauta ndiye Mlengi ndi Mpulumutsi21Chauta akunena kuti,
“Ukumbukire zimenezi, iwe Yakobe,
popeza kuti ndiwe mtumiki wanga, iwe Israele.
Ndidakulenga, ndiwe mtumiki wanga.
Iwe Israele sindidzakuiwala.
22Ndachotsa zolakwa zako ngati mtambo
ndiponso machimo ako ngati nkhungu.
Bwerera kwa Ine poti ndakuwombola.”
23Imbani mokondwa,
inu zolengedwa zamumlengalenga,
pakuti Chauta wagwiradi ntchito.
Fuula iwe dziko lapansi.
Yambani nyimbo, inu mapiri,
ndiponso inu nkhalango ndi mitengo yanu yonse,
chifukwa Chauta waombola Yakobe,
waonetsa ulemerero wake mwa Israele.
24Chauta, Mpulumutsi wako,
amene adakupanga m'mimba mwa mai wako,
akunena kuti,
“Ndine Chauta, amene ndidapanga zinthu zonse.
Pamene ndinkayalika zakuthambo,
ndinali ndekha.
Pamene ndinkalenga dziko lapansi,
kodi analipo amene adandithandiza?
25 1Ako. 1.20 Ndine amene ndimalepheretsa
mipingu ya anthu onama,
ndi kupusitsa anthu oombeza ula.
Ndine amene ndimatsutsa mau a anthu anzeru,
ndi kuŵaonetsa kuti nzeru zao nzopusa.
26Ndine amene ndimatsimikiza mau a mtumiki wanga,
ndi kupherezetsa zimene amithenga anga adaneneratu.
Ndine amene ndimanena za Yerusalemu
kuti anthu adzakhalanso kumeneko,
ndi kunenanso za mizinda ya ku Yuda
kuti idzamangidwanso.
Ine ndidzautsanso malo ao amene adagwetsedwa.
27Ndine amene ndimauza nyanja yaikulu kuti,
‘Uma, ndipo mitsinje yakonso ndiiwumitsa.’
28 2Mbi. 36.23; Eza. 1.2 Ndine amene ndimanena za Kirusi kuti
‘Iye uja ndi mbusa wanga,
adzachita zonse zimene ndikulinga!
Adzalamula kuti Yerusalemu amangidwenso,
ndipo kuti maziko a Nyumba ya Mulungu aikidwe.’ ”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.