1Afilisti adamenyananso nkhondo ndi Aisraele, ndipo Aisraele adathaŵa Afilisti; ambiri adakaphedwa ku phiri la Gilibowa.
2Afilistiwo adapanikiza Saulo ndi ana ake, ndipo adapha Yonatani, Abinadabu ndi Malikisuwa ana a Saulo.
3Nkhondo idampanikiza kwambiri Sauloyo, ndipo anthu amauta adampeza namlasa koopsa.
4Pamenepo Saulo adauza wonyamula zida zake kuti, “Solola lupanga lako, undibaye, kuwopa kuti anthu osaumbalidwaŵa akabwera angadzandiseke.” Koma wonyamula zida uja sadathe kuchita zimenezo, chifukwa ankachita mantha kwambiri. Ndiye Saulo adangotenga lupanga lake nagwerapo.
5Wonyamula zida uja ataona kuti Sauloyo wafa, nayenso adadzigwetsa pa lupanga lake, nkufa.
6Umu ndimo m'mene adafera Saulo, iyeyo ndi ana ake atatu, pamodzi ndi banja lake lonse.
7Aisraele onse amene anali ku chigwa, ataona kuti gulu lankhondo lathaŵa, ndipo kuti Saulo ndi ana ake aphedwa, nawonso adathaŵa nasiya mizinda yao. Tsono Afilisti aja adabwera nkudzakhala m'menemo.
8M'maŵa mwake, Afilisti atabwera kudzafunkha za anthu ophedwawo, adapeza Saulo ataphedwa pamodzi ndi ana ake pa phiri la Gilibowa.
9Adamdula mutu Sauloyo, namuvula zida zake zankhondo. Kenaka adatuma amithenga ku dziko lao lonse, kuti akafalitse uthenga wabwinowu kwa milungu yao ndi kwa anthu omwe.
10Tsono adaika zida za Sauloyo m'nyumba ya milungu yao, ndipo adakhomerera mutu wakewo ku nyumba ya Dagoni, mulungu wao.
11Koma anthu a ku Yabesi-Giliyadi atamva zonse zimene Afilisti adaamchita Saulo,
12amuna onse olimba mtima adanyamuka kukatenga mtembo wa Saulo ndi mitembo ya ana ake kubwera nayo ku Yabesi. Adakwirira mafupa aowo patsinde pa mtengo wa thundu ku Yabesi, ndipo adasala zakudya masiku asanu ndi aŵiri.
13 1Sam. 13.8-14; 15.1-24; Lev. 19.31; 20.6; 1Sam. 28.7, 8 Choncho Saulo adafa chifukwa cha kusakhulupirika kwake. Iyeyo anali wosakhulupirika kwa Chauta, poti sankamvera mau a Chauta ndiponso ankapempha nzeru kwa anthu olankhula ndi mizimu,
14ndipo sankafuna kuti Chauta amutsogolere. Nchifukwa chake Chautayo adamupha napereka ufumu kwa Davide mwana wa Yese.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.