1Tsono Elifazi wa ku Temani adati,
2“Iwe Yobe, kodi wina atakuyankha,
ndiye kuti wakulakwira?
Ah, koma ine ndekha sindingathe kukhala chete.
3Taona, iwe waphunzitsa anthu ambiri,
walimbitsa mtima anthu ofooka.
4Mau ako adathandiza munthu wofuna kugwa,
adachirikiza munthu wotha mphamvu.
5Koma tsopano mavuto akufikira iweyo,
ndipo wataya mtima.
Zakukhudza lero, ndipo ukuchita mantha.
6Unkalemekeza Mulungu, tsono uyenera kumdalira Iyeyo,
Unkayenda m'njira yosalakwa,
tsono uyenera kukhulupirira Mulungu.
7“Ganiza bwino tsopano: Kodi alipo munthu wosachimwa
amene adaonongekapo nkale lonse?
Nanga nkuti kumene udaona anthu olungama ataphedwa?
8Monga ndaonera ine,
anthu amene amabzala tchimo namafesa mavuto,
amakolola zomwezo.
9Monga momwe mphepo ya mkuntho imasakazira zinthu,
Mulungu amaŵaononga ndi mkwiyo wake.
10Anthu oipa amakhuluma ngati mkango,
koma Mulungu amaŵathyola mano.
11Iwowo amafa ngati mikango yosoŵa nyama,
ndipo misona yao imamwazikana.
12“Tsono mau adandifika monong'ona,
khutu langa lidamva kunong'onako.
13 Yob. 33.15 Zidandibwerera usiku m'masomphenya,
nthaŵi imene anthu amagona tulo tofa nato.
14Ndidagwidwa ndi mantha,
nkuyamba kunjenjemera,
thupi langa lonse lidaweyeseka.
15Pamenepo mpweya wayaziyazi udandidutsa kumaso,
ndipo ubweya wa pathupi panga udangoti njoo, kuimirira,
chifukwa cha mantha.
16Chinthucho chidangoti chilili,
koma ine osaŵazindikira maonekedwe ake.
Patsogolo panga panali chinthu ndithu,
kudangoti zii, kenaka ndidamva mau akuti:
17‘Kodi munthu angathe kukhala wolungama
pamaso pa Mulungu?
Kodi munthu angathe kukhala wangwiro
pamaso pa Mlengi wake?
18Mulungu sakhulupirira ndi atumiki ake omwe,
angelo ake omwe amaŵapeza cholakwa.
19Nanji munthu amene adachokera ku dothi,
amene ali fumbi chabe,
amene amathudzuka ngati kadziwotche.
20M'maŵa ali moyo, madzulo nkufa munthuyo.
Amapita ku manda, naiŵalika kotheratu.
21Zonse zimene ali nazo zimatha,
ndipo amafa osadziŵa nkanthu komwe.’ ”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.