Mk. 12 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Fanizo la antchito olima m'munda wamphesa(Mt. 21.33-46; Lk. 20.9-19)

1 Yes. 5.1, 2 Yesu adayamba kulankhula nawo m'mafanizo. Adati, “Munthu wina adaabzala mipesa m'munda mwake, namanga mpanda kuzinga mundawo. Adakumba nkhuti yoponderamo mphesa, namanga nsanja yolondera mundawo. Pambuyo pake munda uja adaubwereka alimi, iye nkunyamuka ulendo wa ku dziko lina.

2Nyengo yothyola zipatso itafika, munthu uja adatuma wantchito wake kwa alimi aja, kuti alimiwo akampatsireko zipatso za m'munda muja.

3Koma alimiwo adamugwira wantchitoyo nammenya, nkumubweza osampatsa kanthu.

4Munthu uja adatumanso wantchito wina, koma alimi aja adamtema m'mutu nkumunyazitsa.

5Munthuyo adatumanso wantchito wina, uyu ndiye adangomupheratu. Adachita chimodzimodzi ndi antchito ena ambiri, ena adaŵamenya, ena kuŵapheratu.

6“Munthu uja adangotsala ndi mmodzi basi, mwana wake weniweni wapamtima. Ndiye pambuyo pa onse adadzatuma iyeyu. Adati, ‘Mwana wanga yekhayu akamchitira ulemu.’

7Koma alimi aja adayamba kuuzana kuti, ‘Ameneyu ndiye amene ati adzamsiyire chumachi. Tiyeni timuphe kuti chidzakhale chathu.’

8Tsono adamugwiradi, namupha nkumuponya kunja kwa mundawo.

9“Kodi mwini munda wamphesa uja adzachita chiyani? Ndithu, adzabwera naŵapha alimiwo, munda uja nkuubwereka alimi ena.

10Mas. 118.22, 23 Nanga monga simudaŵerenge Malembo aja akuti,

“ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba adaaukana,

womwewo wasanduka mwala wapangondya,

wofunika koposa.

11Ambuye Mulungu ndiwo adachita zimenezi,

ndipo nzotidabwitsa kwambiri.’ ”

12Pamene akulu a Ayuda aja adazindikira kuti fanizolo Yesu ankaphera iwowo, adafunitsitsa kumugwira, koma ankaopa khamu la anthu. Tsono adangomusiya nachokapo.

Afunsa Yesu za kukhoma msonkho(Mt. 22.15-22; Lk. 20.20-26)

13Anthu ena a m'gulu la Afarisi, ndi enanso a m'chipani cha Herode, adaatumidwa kuti akatape Yesu m'kamwa.

14Atafika, adati, “Aphunzitsi, tikudziŵa kuti Inu mumanena zoona, ndipo simuwopa munthu aliyense. Simuyang'anira kuti uyu ndani, koma mumaphunzitsa malamulo a Mulungu moona. Nanga tsono, kodi Malamulo a Mulungu amalola kuti tizikhoma msonkho kwa Mfumu ya ku Roma, kapena ai?

15Kodi tizikhomadi kapena tisamakhoma?” Koma Yesu podziŵa maganizo ao onyenga, adati, “Bwanji kodi mukundiyesa dala? Tandipatsirani ndalama, ntaiwona.”

16Iwo adampatsadi ndalamayo. Tsono Iye adaŵafunsa kuti, “Kodi nkhopeyi ndi ya yani, ndipo dzinali ndi la yani?” Iwo aja adati, “Zonse ndi za Mfumu ya ku Roma.”

17Apo Yesu adaŵauza kuti, “Tsono perekani kwa Mfumu zake za Mfumuyo, ndiponso kwa Mulungu zake za Mulunguyo.” Atamva zimenezi anthuwo adathedwa nzeru.

Za kuuka kwa akufa(Mt. 22.23-33; Lk. 20.27-40)

18 Ntc. 23.8 Pambuyo pake Asaduki ena adadza kwa Yesu. Iwo amati akufa sadzauka. Adamufunsa kuti,

19Deut. 25.5 “Aphunzitsi, Mose adatilembera lamulo lakuti, ‘Ngati munthu amwalira, nasiya mkazi, koma opanda ana, mbale wake wa womwalirayo aloŵe chokolo, kuti amuberekere ana mbale wake uja.’

20Tsono padaali anthu asanu ndi aŵiri pachibale pao. Woyamba adaakwatira mkazi, namwalira opanda mwana.

21Wachiŵiri adamtenga mai uja, nayenso nkumwalira osasiya mwana. Wachitatunso chimodzimodzi.

22Mpaka asanu ndi aŵiri onse aja adamwalira osasiya mwana. Potsiriza pake mai uja nayenso adamwalira.

23Nanga tsono pa tsiku lodzauka akufa, mwini mkaziyo adzakhala utiwuti, popeza kuti abale asanu ndi aŵiri onse aja adaamkwatirapo?”

24Yesu adaŵayankha kuti, “Si pamenepa nanga pomwe mumalakwira, chifukwa chosadziŵa Malembo ndiponso mphamvu za Mulungu?

25Pajatu pouka akufa, palibenso za kukwatira kapena kukwatiwa ai. Onse ali ngati angelo Kumwamba.

26Eks. 3.6Tsono zakuti anthu adzauka kwa akufa, kodi simudaŵerenge m'buku la Mose, paja akunena za chitsamba choyakapa? Suja akuti Mulungu adamuuza Mose kuti, ‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, ndine Mulungu wa Isaki, ndine Mulungu wa Yakobe?’

27Ndiye kutitu sali Mulungu wa anthu akufa ai, koma wa anthu amoyo. Inu ndinu olakwa kwabasi.”

Za lamulo lalikulu(Mt. 22.34-40; Lk. 10.25-28)

28Mphunzitsi wina wa Malamulo adaŵamva akutsutsana. Ataona kuti Yesu waŵayankha bwino Asaduki aja, adadza pafupi, namufunsa kuti, “Kodi mwa malamulo onse, lalikulu ndi liti?”

29Deut. 6.4, 5Yesu adamuyankha kuti, “Lamulo lalikulu ndi ili, ‘Tamverani, inu Aisraele, Chauta, Mulungu wathu, Iye yekha ndiye Mulungu.

30Motero, uzikonda Chauta, Mulungu wakoyo, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu zako zonse.’

31Lev. 19.18 Lamulo lachiŵiri lake ndi ili, ‘Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.’ Palibe lamulo lina loposa malamulo ameneŵa.”

32 Deut. 4.35 Mphunzitsi wa Malamulo uja adati, “Ai, mwayankha bwino, Aphunzitsi. Monga mwaneneramo, nzoonadi kuti Mulungu ndi mmodzi yekhayo, ndipo palibe winanso koma Iye yekha.

33Hos. 6.6 Mwalondolanso ponena kuti chinthu chopambana ndicho kumkonda Mulungu ndi mtima wonse, ndi nzeru zonse, ndi mphamvu zonse, ndiponso kukonda mnzako monga umadzikondera iwe wemwe. Kuteroko nkoposa kupereka nsembe zopsereza ndiponso nsembe zina zonse.”

34Lk. 10.25-28Yesu adaona kuti munthuyo wayankha mwanzeru. Tsono adamuuza kuti, “Iwe suli kutali ndi Ufumu wa Mulungu.” Ndipo kuyambira apo panalibenso wina woti ayesere kumfunsa kanthu.

Za Mpulumutsi Wolonjezedwa uja(Mt. 22.41-46; Lk. 20.41-44)

35Pamene Yesu ankaphunzitsa anthu m'Nyumba ya Mulungu, adafunsa kuti, “Kodi bwanji aphunzitsi a Malamulo amati Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndi mwana wa Davide?

36Mas. 110.1 Paja Davide, ndi nzeru zochokera kwa Mzimu Woyera, adati,

“ ‘Chauta adauza Mbuye wanga kuti,

Khala ku dzanja langa lamanja,

mpaka nditasandutsa adani ako

kuti akhale ngati chopondapo mapazi ako.’

37Davide weniweniyo akutchula Mpulumutsi wolonjezedwa uja kuti Mbuye wake. Tsono angakhale mwana wakenso bwanji?”

Yesu achenjeza anthu za aphunzitsi a Malamulo(Mt. 23.1-36; Lk. 20.45-47)

Anthu ambirimbiri aja ankakondwa kwambiri pomva mau ake.

38Pamene Yesu ankaŵaphunzitsa, adati, “Chenjera nawoni aphunzitsi a Malamulo. Amakonda kuyenda atavala mikanjo yaitali, ndi kuti anthu aziŵalonjera mwaulemu pa misika.

39Amakonda mipando yaulemu kwambiri m'nyumba zamapemphero, ndiponso malo olemekezeka pa maphwando.

40Koma amaŵadyera chuma chao azimai amasiye, nkumapemphera mapemphero ataliatali monyengezera. Anthu ameneŵa adzalangidwa koposa.”

Za chopereka cha mai wina wamasiye(Lk. 21.1-4)

41Tsiku lina Yesu adaakhala pansi kuyang'anana ndi bokosi loponyamo ndalama zopereka ku Nyumba ya Mulungu. Ankayang'anitsitsa m'mene anthu ankaponyera ndalama zao. Anthu ambiri achuma ankaponyamo ndalama zambiri.

42Koma padafika mai wina wamasiye, wosauka. Iyeyu adangoponyamo tindalama tiŵiri.

43Tsono Yesu adaitana ophunzira ake naŵauza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti mai wamasiye wosaukayu waponyamo koposa anthu ena onseŵa, amene akuponya ndalama m'bokosimu.

44Chifukwa ena onseŵa angoponyamo zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo. Koma maiyu, mwa umphaŵi wake, waponyamo zonse zimene anali nazo, ngakhale zimene akadagulira chakudya.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help