Tob. 10 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tobiyasi atsazika apongozi ake

1Tsiku ndi tsiku Tobiti ankaŵerenga masiku ofunikira ulendo wopita ku Mediya ndi kubwerako. Poona kuti atha masiku amene adaaŵerengera, koma mwana wake kukali zii, adaganiza kuti, “Kusakhale kuti kwachitika zina zomchedwetsa kumeneko!

2Kapenatu Gabaele adafa, ndiye palibe wompatsa ndalama zija.”

3Tsono adayamba kuvutika.

4Hana, mkazi wake, ankanena kuti, “Mwana wanga watayika basi, sali moyonso.” Pomwepo adayamba kudza misozi, ndi kumalira mwana wake.

5Ankati, “Kalanga ine! Mwana wanga, ndidakulolezeranji kupita, iwe chimwemwe cha moyo wanga.”

6Apo Tobiti adati, “Iwe mlongo wanga, tonthola! Usachulukitse mau, ali moyobe. Ndithu, kanthu kena kachitika kuti achedwe. Munthu amene adapita naye uja ndi wokhulupirika, ndipo ndi mmodzi mwa abale athu. Usataye mtima, mlongo wanga. Afika ndithu posachedwa.”

7Koma iye adayankha kuti, “Musandiwuzenso kanthu, musandinyenge ndi mau anu. Mwana wanga adamwalira basi.” Choncho ankadzuka nkukayang'ana kunjira kumene mwana wake adaadzera. Ankatero masiku onse, ndipo sankakhulupirira maso a munthu wina aliyense, koma ake okha basi. Dzuŵa litaloŵa, ankabwerera ku nyumba akulira misozi, ndipo ankalira usiku wonse, osaona tulo.

Atatha masiku khumi ndi anai a phwando laukwati, amene Raguele adaalumbira kuti amchitira mwana wake, Tobiyasi adadza kwa iye, nati, “Mundilole ndizipita, chifukwa ndikudziŵa kuti atate anga ndi amai anga akuganiza kuti sadzandiwonanso. Tsopano, ndikukupemphani bambo, mundilole kuti ndizipita, ndibwerere kwa atate anga. Ndakuuzani m'mene analiri pamene ndinkaŵasiya.”

8Apo Raguele adauza Tobiyasi kuti “Bakhala konkuno, mwana wanga, bakhala nane. Ndituma amithenga kwa Tobiti bambo wako, kuti akamudziŵitse za iwe.”

9Koma iye adati, “Iyai, pepani, mundilole kuti ndizipita tsopano lino, ndibwerere kwa bambo wanga.”

10Tsono Raguele adadzuka, napatsa Tobiyasi Sara mkazi wake ndi hafu la chuma chake, anthu antchito, adzakazi, ng'ombe, nkhosa, abulu, ngamira, zovala, ndalama ndi ziŵiya zam'nyumba.

11Ndipo adaŵaloleza kupita ndi chimwemwe. Potsazikana nawo adati, “Tobiyasi, mwana wanga, ukhale ndi moyo wamphamvu ndipo uyende bwino. Ambuye akumwamba atsagane nanu, iwe ndi Sara mkazi wako, ndipo Mulungu alole kuti ndidzaone ana anu ndisanafe.”

12Kenaka adauza Sara mwana wake kuti, “Tsopano pita ku nyumba kwa apongozi ako, chifukwa tsopano iwowo ndi atate ako ndi amai ako, monga momwe tiliri anakubala akofe. Pita ndi mtendere mwana wanga, Mulungu akuthandize kuti ndizimva zabwino zokhazokha za iwe pa moyo wanga wonse.” Tsono atatsazikana nawo, adaŵalola kupita.

Edina adauza Tobiyasi kuti, “Mwana wanga ndi mlongo wanga wokondedwa, Ambuye akutsogolere bwino kwanu. Ndidzaone ana anu ine ndisanafe. Pamaso pa Ambuye, undisungire bwino mwana wangayu, usamuvutitse ndi tsiku limodzi lomwe pa moyo wake. Mwana wanga, pita ndi mtendere! Tsopano ine ndine mai wako, Sara ndi mkazi wako. Mulungu atithandize tonse kuti tikhale osangalala masiku onse a moyo wathu.” Atatero adaŵampsompsona aŵiriwo, naŵalola kupita ali okondwa.

13Tsono Tobiyasi adachoka kunyumba kwa Raguele mtima uli m'malo. Adayamika Ambuye akumwamba, Mfumu ya zinthu zonse amene adatsagana naye pa ulendo wake wonse. Ndipo adalonjeza Raguele ndi mkazi wake Edina kuti, “Ndidzakulemekezani inu, atate ndi amai, pa moyo wanga wonse.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help