1 Mt. 11.5; Lk. 7.22 Lk. 4.18, 19 Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine,
chifukwa Chauta wandidzoza.
Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino
kwa anthu osauka,
ndi kukasangalatsa a mtima wosweka,
kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu,
ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.
2 Mt. 5.4 Wandituma kukalengeza za nthaŵi
imene Chauta adzapulumutsa anthu ake
ndi kulipsira adani ake.
Wanditumanso kukatonthoza olira.
3Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika
olira a ku Ziyoni,
ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo
m'malo mwa phulusa lachisoni,
ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa
m'malo mwa kulira,
ndiŵapatse chovala cha chikondwerero
m'malo mwa kutaya mtima.
Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo,
yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.
4Adzamanganso mabwinja akale a mzinda,
adzautsa nyumba zimene zidaaonongeka.
Adzakonzanso mizinda imene idaapasuka,
ndiponso malo osiyidwa chiyambire cha kalekale.
5“Anthu achilendo adzakutumikirani,
ndipo adzaŵeta ziŵeto zanu,
iwo omwewo adzalima minda yanu,
makamaka minda yanu yamphesa.
6Koma inu mudzatchedwa ansembe a Chauta,
ponena za inu anthu adzati ndinu atumiki a Mulungu.
Mudzadyerera chuma cha anthu a mitundu ina,
ndipo mudzanyadira ulemu umene mwaŵalanda.
7Popeza kuti mudalandira manyazi,
manyozo ndi zotukwana moŵirikiza,
tsopano mudzalandira chigawo cha dziko lanu
moŵirikizanso.
Chimwemwe chanu chidzakhala chamuyaya.”
8“Ine Chauta ndimakonda chilungamo,
ndimadana ndi zakuba ndi zoipa.
Anthu anga ndidzaŵapatsa mphotho mokhulupirika,
ndidzapangana nawo chipangano chosatha.
9Ana ao adzakhala odziŵika
pakati pa anthu a mitundu ina,
zidzukulu zaonso zidzakhala zotchuka
pakati pa anthu onse.
Aliyense woŵaona adzazindikira
kuti ndi anthu amene Ine Chauta ndidaŵadalitsa.”
10 Chiv. 21.2 Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta,
mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga.
Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso.
Wandiveka mkanjo wa chilungamo.
Zinali ngati mkwati wamwamuna
wavala nkhata ya maluŵa m'khosi,
ndiponso ngati mkwati wamkazi
wavala mikanda ya mtengo wapatali.
11Monga momwe nthaka imameretsera mbeu,
ndiponso monga momwe munda
umakulitsira zimene adabzalamo,
momwemonso Chauta adzaonetsa chilungamo
ndi ulemerero wake pamaso pa anthu onse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.