Mas. 64 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero lopempha chitetezoKwa Woimbitsa Nyimbo. Salmo la Davide.

1Imvani mau anga, Inu Mulungu,

pamene ndikukudandaulirani.

Tetezani moyo wanga kwa mdani woopsa.

2Tchinjirizeni ku upo wachiwembu wa anthu oipa,

tetezeni ku chiwawa cha anthu ochita zoipa.

3Iwo amanola lilime lao ngati lupanga,

amaponya mau obaya ngati mivi.

4Amabisalira anthu osalakwa

namaŵalasa modzidzimutsa ndi mopanda mantha.

5Amalimbikira za chiwembu chao,

amakambirana zoti atche misampha yobisika,

amanena kuti, “Angatiwone ndani?”

6Amaganizira zoipa nkumati,

“Takonza mochenjera ndithu chiwembu chathu.”

Malingaliro ndi zofuna za mtima wa munthu nzobisika.

7Koma Mulungu adzaŵaponya mivi.

Motero mwadzidzidzi iwo adzalasidwa.

8Adzaŵaononga chifukwa cha zokamba zao,

onse oŵapenya adzapukusa mitu.

9Pompo anthu onse adzachita mantha,

adzasimba zimene Mulungu wachita,

adzalingalira zomwe Mulungu wachitazo.

10Chauta adalitse anthu ake

mtendere ndi chimwemwe zikhale nao,

anthu akondwere chifukwa cha Chauta

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help