1Chauta adauza Mose kuti,
2“Uza Aisraele kuti mkazi akakhala ndi pakati, nabala mwana wamwamuna, adzakhala woipitsidwa masiku asanu ndi aŵiri, monga pa nthaŵi yake yakusamba.
3Gen. 17.12; Lk. 2.21 Ndipo pa tsiku lachisanu ndi chitatu mwanayo aumbalidwe.
4Mkaziyo adikirebe masiku ena 33, kuti ayeretsedwe ku matenda ake. Asakhudze kanthu kopatulika kalikonse, ndipo asaloŵe m'malo oyera, mpaka masiku akudziyeretsa atatha.
5Koma akabala mwana wamkazi, adzakhala woipitsidwa masabata aŵiri monga pa nthaŵi yake yakusamba. Ndipo mkaziyo adikirebe masiku ena 66, kuti ayeretsedwe ku matenda ake.
6“Tsono masiku akudziyeretsa kwake aja atatha, kapena ndi a mwana wamwamuna kapena a mwana wamkazi, abwere kwa wansembe ndi mwanawankhosa wa chaka chimodzi pa khomo la chihema chamsonkhano, kuti nkhosayo ikhale nsembe yopsereza. Abwerenso ndi bunda la nkhunda kapena njiŵa, kuti aperekere nsembe yopepesera machimo.
7Wansembeyo apereke zimenezo pamaso pa Chauta potsata mwambo wopepesera mkaziyo. Apo mkaziyo adzakhala woyeretsedwa ku matenda ake. Limeneli ndi lamulo la mkazi amene abala mwana wamwamuna kapena wamkazi.
8Lk. 2.24 Koma ngati alibe mwanawankhosa, atenge njiŵa ziŵiri kapena maundaankhunda aŵiri, imodzi ikhale ya nsembe yopsereza, ndipo inayo ikhale ya nsembe yopepesera machimo. Tsono wansembe achite mwambo wopepesera, ndipo mkaziyo adzakhala woyeretsedwa.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.