Mphu. 27 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Ambiri adachimwa chifukwa chofuna kupeza phindu,

munthu wofunitsitsa kulemera amauma mtima.

2Monga chikhomo chimakhomedwa pakati pa miyala iŵiri,

momwemonso tchimo limakhazikika pakati pa kugulitsa

ndi kugula malonda.

3Munthu akapanda kulimbikira kuwopa Ambuye,

nyumba yake idzagamuka msanga.

Zokamba za munthu zimaonetsa maganizo ake.

4Munthu akagwedeza sefa, zinyatsi zimatsalira momwemo.

Chimodzimodzinso zolakwa za munthu zimaoneka

iye akamalankhula.

5Monga mbiya amaiyesa pa moto,

momwemonso munthu amayesedwa pa zokamba zake.

6 Mt. 7.17; 12.33; Lk. 6.44 Monga chipatso cha mtengo chimatidziŵitsa luso la mlimi,

momwemonso zokamba za munthu zimaonetsa zimene

zili mumtima mwake.

7Usatamande munthu usanamve zolankhula zake,

poti mayeso enieni a anthu ali pamenepa.

Za chilungamo

8Ngati ufunafuna chilungamo, udzachipeza,

ndipo udzachivala ngati mkanjo wokongola.

9Mbalame za mtundu umodzi zimayendera pamodzi.

Chonchonso chilungamo chimakhala nawo amene amachitsata.

10Mkango umalalira nyama,

chimodzimodzinso tchimo limalalira anthu osatsata chilungamo.

Za kulankhula kopusa

11Zolankhula za munthu wokonda Mulungu nzanzeru

nthaŵi zonse,

koma munthu wopusa amasinthasintha ngati mwezi.

12Ukamacheza ndi anthu opusa,

yesa kupeza mpata wochokerapo msanga,

koma ukamacheza ndi anthu okamba zanzeru,

ungathe kukhalitsa ndithu.

13Mau a anthu opusa amanyansa,

ndipo iwo amangosekerera machimo.

14Mau a anthu okonda kulumbiralumbira

amaimiritsa tsitsi pa mutu,

akayambana, anzao amangotseka makutu.

15Anthu onyada akayambana,

amakhetsana magazi,

mau ao otukwana amamvetsa chisoni.

16 Miy. 20.19; 25.9 Munthu wokonda kuulula zinsinsi salinso wokhulupirika,

ndipo sangapeze konse bwenzi lapamtima.

17Ukonde bwenzi wako

ndi kukhala wokhulupirika kwa iye.

Koma ngati udawanditsa zinsinsi zake,

usakacheze nayenso.

18Chifukwa monga momwe munthu

amaonongera mnzake pakumupha,

momwemonso iweyo udapheratu

chibwenzi cha mnzako.

19Monga momwe mbalame imakupulumukira m'manja,

ndi m'menenso wakupulumukira bwenzi wako,

ndipo sungamugwirenso.

20Usamulondolenso chifukwa wapita kutali,

ali ngati mphoyo imene yaonjoka ku msampha.

21Chilonda ukhoza kuchimanga,

munthu wachipongwe ukhoza kumkhululukira,

koma munthu woulula chinsinsi cha mnzake

sungamkhulupirirenso.

Za makhalidwe onyenga

22Munthu akakutuzulira maso,

ndiye kuti akuganiza kukuchita zoipa,

palibe amene angamletse

kuchita zimenezo.

23Pokamba nawe, amalankhula mau amyaa,

ndipo amayamika zimene ukunena.

Koma pambuyo pake amasintha mau ake,

napotoza mau ako kuti akutsutse.

24Pali zambiri zimene ndimadana nazo,

koma munthu wotere ndimadana naye

kupambana zonse.

Ambuye nawonso amadana naye.

25Munthu woponya mwala kumwamba

umamugwera pamutu pake pomwe.

Nkhonya yobisalira imadzetsa zilonda pa mwiniwake.

26Ukakumba mbuna, udzagwamo ndiwe wemwe.

Ukatcha msampha udzakodwamo ndiwe wemwe.

27Munthu wochita anzake zoipa,

zoipa zake zomwezo zimambwerera,

osadziŵa kumene zachokera.

28Munthu wodzikuza amanyodola anzake ndi

kuŵachita chipongwe,

koma kulipsira kumamlalira iye yemwe ngati mkango.

29Anthu amene amakondwera akaona munthu

wabwino alikugwa,

adzakodwa mu msampha,

ndipo adzazunzika asanafe.

Za mkwiyo

30Mkwiyo ndi ukali, nazonso nzoipa zazikulu,

munthu wochimwa amakhala nazo ziŵiri zonsezo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help