1Tsoka kwa ufumu wonyada wa zidakwa za ku Efuremu!
Tsoka kwa ulemerero wake
umene wayamba kufota ngati duŵa,
mzinda uja uli kumtunda kwa chigwa chachonde,
umene amanyadira anthu oledzera vinyo.
2Ambuye ali naye wina wamphamvu ndi wanyonga.
Iyeyo adzabwera ngati mkuntho wamatalala
ndi namondwe woononga,
ngati chigumula chamadzi chokokolola zonse,
ndipo adzaŵagwetsa pansi mwankhanza.
3Kunyada kwa atsogoleri oledzera a ku Efuremu
adzakuthetseratu kwenikweni.
4Ndipo ulemerero wa mzinda uja
umene uli ngati duŵa lokhala kumtunda
kwa chigwa chachonde wayamba kufota.
Udzakhala ngati nkhuyu yoyambirira kupsa.
Munthu akangoiwona, amaithyola
ndi kuidya nthaŵi yomweyo.
5Tsiku limenelo Chauta Wamphamvuzonse
adzakhala ngati chisoti chachifumu chaulemerero
ndi nsangamutu yokongola kwa anthu ake otsala.
6Oweruza adzaŵapatsa mtima wachilungamo.
Adzaŵalimbitsa mtima onse amene amalimbana ndi
adani pa zipata za mzinda.
Yesaya atsutsa aneneri oledzera a ku Yuda7Nawonso aŵa ali punzipunzi chifukwa cha vinyo,
akudzandira ndi zakumwa zaukali.
Ansembe ndi aneneri ali punzipunzi ndi zakumwa zaukali.
Onsewo ndi osokonezeka chifukwa cha vinyo,
ali dzandidzandi chifukwa cha zakumwa zaukali.
Amamvetsa molakwa zimene amaziwona m'masomphenya,
amalephera kuweruza milandu imene amadzaŵatulira.
8Pa matebulo onse pali masanzi okhaokha,
palibenso malo opanda uve.
9Iwo akuti,
“Kodi munthu ameneyu akuti aphunzitse yani?
Kodi uthengawo akuti afotokozere yani?
Kodi ndife ana ongoleka kumene kuyamwa,
kapena makanda ongoŵachotsa kumene kubere?
10Akuyesa kumatiphunzitsa pang'onopang'ono
lemba ndi lemba, mzere ndi mzere,
phunziro ndi phunziro.
Zonsezo akungoti apa pang'ono, apa pang'ono.”
11 1Ako. 14.21 Ndithudi, Mulungu adzakuphunzitsani
kudzera mwa anthu a chilankhulo chachilendo,
anthu a chilankhulo chamtundu.
12Adaakuuzani kuti, “Malo opumulira ndi ano,
otopa apumule, malo ousira ndi ano,”
koma inu simudamvere.
13Nchifukwa chake Chauta adzakuphunzitsani
pang'onopang'ono, lemba ndi lemba,
mzere ndi mzere, phunziro ndi phunziro,
kuti mudzakhumudwe poyenda.
Mudzapweteka, mudzakodwa mu msampha,
ndipo adzakutengani ku ukapolo.
Mwala wapangodya ku Ziyoni14Tsopano mverani zimene Chauta akukuuzani,
inu anthu achipongwe,
amene mumalamulira anthu ake kuno ku Yerusalemu.
15 Lun. 1.16; Mphu. 14.12 Inu mumanena kuti
“Ife tidachita chipangano ndi imfa,
ndipo manda satiwopsa ai.
Chiwonongeko chikamadzafika, sichidzatikhudza konse.
Inu mumakhulupirira mabodza ngati kothaŵira,
ndipo mumadalira kunama kuti kukhale kopulumukira.”
16 Mas. 118.22, 23; Aro. 9.33; 10.11; 1Pet. 2.6 Tsopano zimene akunena Ambuye Chauta nzakuti,
“Ku Ziyoni ndikuika maziko a mwala wotsimikizika,
mwala wapangodya wamtengowapatali
wopanga maziko amphamvu.
Pamwalapo palembedwa kuti,
‘Wokhulupirira sadzagwedezeka.’
17Chilungamo ndicho chidzakhala ngati chingwe
choyesera maziko ake,
ndipo ungwiro udzakhala ngati choongolera chake.
Koma matalala adzaononga mabodza
amene mumaŵakhulupirira,
ndipo chigumula chidzamiza malo anu opulumukirapo.”
18Chipangano chimene mudachita ndi imfa chidzatha,
kotero kuti manda adzayamba kukuwopsani.
Chiwonongeko chikamadzafika, chidzakugonjetsani.
19Nthaŵi iliyonse imene chizidzaoneka,
chizidzakukanthani.
Chizidzafika m'maŵa mulimonse,
usana ndi usiku.
Tsono anthu akadzamvetsa uthenga umenewu,
adzaopsedwa kwambiri.
20Mudzakhala ngati munthu wogona
pa bedi lalifupi kwambiri,
kotero kuti sangatambalitsepo miyendo,
ndiponso ngati munthu wofunda kabulangete kopereŵera.
21 2Sam. 5.20; 1Mbi. 14.11; Yos. 10.10-12 Chauta adzamenya nkhondo
monga adachitira ku phiri la Perazimu.
Adzakalipa monga adachitira ku chigwa cha Gibiyoni.
Adzachita zimene afuna,
ngakhale kuti zidzaoneke ngati zachilendo.
Adzatsiriza ntchito yake,
ntchito yake yozizwitsayo.
22Tsono inu musanyozere mau ameneŵa.
Mukatero, maunyolo anu adzakuthinani koposa.
Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, andiwuza kuti,
“Ndagamula kuti ndidzaononga dziko lonse.”
Nzeru za Mulungu23Tcherani khutu, ndipo mumve mau anga.
Mvetserani ndipo mumve zimene ndikukuuzani.
24Kodi mlimi wofuna kubzala
amangokhalira kutipula kokhakokha?
Kodi amangokhalira kugaula ndi kugalauza?
25Akasalaza mundawo,
suja amafesa maŵere ndi chitoŵe?
Suja amafesa tirigu ndi barele m'mizere,
nabzala mcheŵere m'mphepete mwa mundawo?
26Mulungu ndiye amamulangiza
ndi kumphunzitsa njira yokhoza.
27Maŵere sapuntha poponderezapo
ndi gareta lopanda mikombero,
ndipo chitoŵe sapuntha popondetsapo
mikombero ya gareta.
Maŵere amapuntha ndi kamtengo,
chitoŵe amaomba ndi ndodo.
28Tirigu sangamupunthe kosalekeza,
kuwopa kuti angatekedzeke.
Amampuntha poyendetsapo galeta,
koma osatekedza njere zake.
29Nzeru zimenezi zimachokera kwa Chauta Wamphamvuzonse.
Uphungu wake ndi wodabwitsa, nzeru zake nzopambana.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.