Zek. 10 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chauta adzapulumutsa anthu ake

1Pemphani Chauta kuti akupatseni mvula

pa nyengo yobzala.

Ndiye amene amapanga mitambo yamvula.

Ndiye amene amagwetsera anthu mvula yamvumbi,

ndiye amene amameretsera aliyense mbeu m'munda.

2 Mt. 9.36; Mk. 6.34 Paja mafano am'nyumba amalankhula zonama,

ndipo oombeza maula amaona zabodza.

Olota maloto amalota zabodza,

ndipo mau ao othuzitsa mtima ndi nkhambakamwa chabe.

Motero anthu amangoyenda uku ndi uku ngati nkhosa,

amazunzika chifukwa chosoŵa mbusa.

3Chauta akuti,

“Ndaŵakwiyira kwambiri abusa,

ndipo atsogoleri a m'dzikomo ndidzaŵalanga.

Koma Ine Chauta Wamphamvuzonse

ndidzasamala nkhosa zanga,

ndiye kuti banja la Yuda,

ndipo ndidzazisandutsa ngati akavalo ankhondo amphamvu.

4Mwa iwo mudzatuluka mtsogoleri

amene adzakhala ngati mwala wapangodya,

ngati uta wankhondo.

Ndipo atsogoleri onse olamulira adzachokeranso mwa iyeyo.

5Ayuda onse pamodzi adzakhala ngati ngwazi zankhondo,

zopondereza adani m'matope am'miseu nthaŵi yankhondo.

Adzamenya nkhondo chifukwa choti Chauta ali nawo,

ndipo adzagonjetsa adani okwera pa akavalo.

6“Banja la Yuda ndidzalilimbitsa,

banja la Yosefe ndidzalipambanitsa.

Anthuwo ndidzaŵabwezanso kwao

chifukwa choti ndaŵamvera chifundo.

Tsono adzakhala ngati kuti sindidaŵataye,

pakuti Ine ndine Chauta, Mulungu wao,

ndipo ndidzayankha zopempha zao.

7Pamenepo Aefuremu adzakhala ngati ankhondo amphamvu,

adzasangalala ngati anthu okhuta vinyo.

Ana ao adzaziwona zimenezi, nawonso nkusangalala,

mumtima mwao mudzadzaza chimwemwe,

chifukwa cha zimene Chauta wachita.

8“Ndidzaliza mluzu kuti anthu anga asonkhane pamodzi.

Ndidaŵapulumutsa, ndipo adzachuluka

monga momwe adaaliri masiku amakedzana.

9 Bar. 2.20-32 Ngakhale ndidaŵabalalitsira

pakati pa mitundu ya anthu,

komabe ku maiko akutaliwo adzandikumbukira.

Iwowo pamodzi ndi ana ao adzakhala moyo nadzabwerera.

10Ndidzaŵatulutsa ku Ejipito ndi kupita nawo kwao,

ndipo ndidzaŵasonkhanitsa kuchokera ku Asiriya.

Ndidzaŵafikitsa ku dziko la Giliyadi ndi la Lebanoni

mpaka kudzaza dziko lonse.

11Pamene azidzaoloka nyanja ya ku Ejipito,

ndidzathetsa mafunde a pa nyanjayo,

madzi onse a mtsinje wa Nailo adzaphweratu.

Kudzikuza kwa Asiriya kudzatha,

ndipo ndodo yaufumu ya Ejipito idzathyoka.

12Ineyo ndidzalimbitsa anthu anga,

ndipo adzakhala onyadira dzina la Chauta.”

Ndikutero Ine Chauta.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help