1 Yer. 3.6 Yosiya anali wa zaka zisanu ndi zitatu pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 31 ku Yerusalemu.
2Iyeyo adachita zolungama pamaso pa Chauta, namatsata chitsanzo cha Davide kholo lake pa zonse, osapatukira kumanja kapena kumanzere.
Yosiya achotsa chipembedzo chachikunja3Pa chaka chachisanu ndi chitatu cha ufumu wake, adakali mnyamata, adayambapo kumapembedza Mulungu wa Davide kholo lake. Ndipo pa chaka cha 12 adayamba kuchotsa akachisi opembedzerako mafano ku Yuda ndi mu Yerusalemu. Adachotsanso mafano, osema ndi osungunula.
42Maf. 21.3; 2Mbi. 33.3 Anthu adagumula maguwa a Abaala, iyeyo ali pomwepo. Adagwetsa maguwa ofukizirapo lubani, ndiponso mafano a dzuŵa amene ankakhala pamwamba pake, adaŵagwetsa pansi. Adaphwanya mafano, osema ndi osungunula. Tsono adaŵaperapera mpaka kuŵasandutsa fumbi, ndipo adawaza fumbilo pa manda a anthu amene ankapereka nsembe kwa mafano.
51Maf. 13.2 Iyeyo adatenthanso mafupa a ansembe ao pa maguwa ao ndipo adayeretsa dziko la Yuda ndi mzinda wa Yerusalemu.
6Adayeretsanso mizinda ya Manase, Efuremu, Simeoni, mpaka ku Nafutali, kudzanso mabwinja ao oŵazungulira.
7Adagwetsamo maguwa, naphwanyaphwanya mafano ndi zithunzi, mpaka kuzidyukula ngati fumbi. Ndipo adagwetsa maguwa ofukizirapo lubani m'dziko lonse la Israele. Pambuyo pake adabwerera ku Yerusalemu.
Akonza Nyumba ya Chauta(2 Maf. 22.3-20)8Pa chaka cha 18 cha ufumu wake, atayeretsa dzikolo pamodzi ndi Nyumba ya Chauta yomwe, Yosiya adatuma Safani, mwana wa Azaliya, ndi Maaseiya, kazembe wa mzinda, kudzanso Yowa, mwana wa Yowahazi, mlembi wolemba mbiri, kuti akonze Nyumba ya Chauta Mulungu wake.
9Iwoŵa adadza kwa Hilikiya mkulu wa ansembe, napereka ndalama zimene adaabwera nazo ku Nyumba ya Chauta. Ndalamazo nzimene Alevi ndi alonda apakhomo adaasonkha ku dziko la Manase ndi la Efuremu ndi kwa anthu onse otsala a ku Israele, kwa onse a ku Yuda ndi a ku Benjamini ndiponso kwa nzika zonse za mu Yerusalemu.
10Iwowo adapereka ndalamazo kwa akapitao oyang'anira Nyumba ya Chauta. Adaperekako ndalama zina kwa anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Chauta, kuti aikonze ndi kuilimbitsa.
11Adaperekanso ndalama zina kwa amisiri amatabwa ndi kwa amisiri omanga nyumba, kuti agule miyala yosema ndi mitengo ya mitanda ndi phaso la nyumba, zimene mafumu a ku Yuda adaalola kuti ziwonongeke.
12Anthuwo adagwira ntchitoyo mokhulupirika. Amene ankaŵayang'anira anali Yahati ndi Obadiya, a m'banja la Alevi, ana a Merari. Zekariya ndi Mesulamu, ana aamuna a m'banja la Akohati, adaŵaikamo kuti aziyang'anira. Alevi onse amene anali ndi luso la kumaimba ndi zipangizo zoimbira,
13ankayang'anira anthu onyamula katundu, namatsogolera anthu onse amene ankagwira ntchito iliyonse yotumikira. Alevi ena anali alembi, akapitao ndiponso alonda apamakomo.
Hilikiya apeza Buku la Malamulo14Pa nthaŵi imene ankatulutsa ndalama zimene adaabwera nazo ku Nyumba ya Chauta, wansembe Hilikiya adapeza buku la Malamulo a Chauta, Malamulo aja amene Mulungu adaaŵapereka kudzera mwa Mose.
15Pomwepo Hilikiyayo adauza Safani mlembi kuti, “Ndalipeza buku la Malamulo lija m'Nyumba ya Chauta.” Ndipo adapereka bukulo kwa Safani.
16Safani adadza nalo kwa mfumu, ndiponso adauza mfumu kuti, “Zonse zimene mudauza atumiki anu kuti achite, akuchita.
17Akhuthula ndalama zimene zinali m'Nyumba ya Chauta, azipereka kwa akapitao ndi kwa antchito.”
18Tsono Safaniyo adauza mfumu kuti, “Wansembe Hilikiya wandipatsira buku.” Ndipo adaliŵerenga bukulo pamaso pa mfumu.
19Mfumu itamva mau a Malamulo, idang'amba zovala zake mwachisoni.
20Pomwepo idalamula Hilikiya, Ahikamu mwana wa Safani, Abidoni mwana wa Mika, Safani mlembi uja ndi Asaya mtumiki wa mfumu kuti,
21“Pitani, mukafunse kwa Chauta m'malo mwanga ndi m'malo mwa anthu otsala ku Israele ndi ku Yuda, za mau a m'buku limene lapezekali. Ndithu mkwiyo wa Chauta umene watiyakirawu ngwaukulu, chifukwa choti makolo athu sadamvere mau a Chauta, sadatsate zonse zimene zalembedwa m'bukuli.”
22Choncho Hilikiya, pamodzi ndi anthu amene mfumu idaŵatuma aja, adapita kwa mneneri wamkazi dzina lake Hulida, mkazi wa Salumu. Salumuyo, wosunga zovala zachifumu, anali mwana wa Tokati, mwana wa Hasira. Mkaziyo ankakhala ku Yerusalemu m'dera lachiŵiri la mzindawo. Tsono anthu aja atalankhula naye adamuuza za nkhaniyo,
23Iyeyo adaŵauza kuti, “Chauta, Mulungu wa Israele, akunena kuti, Muuzeni munthu amene wakutumani kwa Ineyo kuti,
24Ine Chauta ndikuti, Ndidzabweretsa choipa ku mzinda uno ndi pa anthu onse am'menemo, potsata matemberero onse olembedwa m'buku limene adaliŵerenga pamaso pa mfumu ya ku Yuda.
25Chifukwa chakuti anthuwo adandisiya Ine namapembedza milungu ina, nkumandichimwira ndi mafano ao, adaputa mkwiyo wanga ndi ntchito zonse za manja ao, Ine pano mkwiyo wanga wayakira mzinda uno, ndipo sudzazima ai.
26Koma mfumu ya ku Yuda imene idakutumani kuti mukafunse Chauta, mukaiwuze kuti Ine Chauta, Mulungu wa Aisraele, ndikuti, Kumva wamva ndithu,
27pakuti mtima wako walapa ndipo wadzichepetsa pamaso pa Mulungu, utamva mau ake otsutsa mzinda uno ndi anthu onse am'menemo. Popeza kuti wadzichepetsa pamaso panga, nkung'amba zovala zako numalira pamaso panga, Inenso ndamva pemphero lako, ndatero Ine Chauta.
28Tsono Ine ndidzakutenga, ukalondole makolo ako, ndipo udzaikidwa m'manda mwamtendere. Motero maso ako sadzaona zoipa zija zimene ndidzabweretsa pa mzinda uno ndi pa anthu ake.” Tsono anthu aja adabwerera nakanena mau amenewo kwa mfumu.
Yosiya achitanso chipangano ndi Mulungu(2 Maf. 23.1-20)29Pamenepo mfumu idatumiza mau kukaitana akuluakulu onse a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti adzasonkhane.
30Ndipo mfumuyo idapita ku Nyumba ya Chauta, pamodzi ndi anthu onse a ku Yuda, nzika za mu Yerusalemu, ansembe ndi Alevi, ndiponso anthu onse aakulu ndi aang'ono omwe. Tsono iye adaŵerenga, pamaso pao, momveka ndithu, mau onse a m'buku lija lachipangano limene lidaapezeka m'Nyumba ya Chauta.
31Kenaka mfumu idaimirira pamalo pake, ndipo idachita chipangano pamaso pa Chauta kuti idzatsata njira za Chauta, ndipo kuti idzasunga mau, malamulo ndi malangizo ake ndi mtima wake wonse ndi moyo wake wonse, ndipo kuti idzagwiritsa ntchito mau a chipangano olembedwa m'bukulo.
32Tsono Yosiya adauza anthu onse amene anali mu Yerusalemu ndi ku Benjamini kuti azisunga chipanganocho. Ndipo nzika za mu Yerusalemu zidatsatadi chipangano cha Mulungu, Mulungu wa makolo ao.
33Kenaka Yosiya adachotsa zinthu zonyansa zonse ku maiko onse a Aisraele, nakakamiza anthu onse okhala ku Israele kuti azitumikira Chauta, Mulungu wao. Motero anthuwo sadaleke kutsata Chauta, Mulungu wa makolo ao, pa masiku onse a Yosiya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.