Yob. 24 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1“Chifukwa chiyani Mphambe

saikiratu nthaŵi yoti aweruze?

Chifukwa chiyani amene ali olungama

saŵaona masiku otero?

2Anthu ena amasendeza malire, kuti akuze dziko lao,

amalanda ziŵeto namakazidyetsa ku mabusa ao.

3Amalanda abulu a ana amasiye,

amalandanso ng'ombe za akazi amasiye,

kuti zikhale chikole.

4Amapatutsa anthu osauka m'miseu,

ndipo amapirikitsa amphaŵi onse.

5Amphaŵiwo amakafunafuna chakudya

ku chipululu ngati mbidzi.

Kulibe kwina koti apezere ana ao chakudya.

6Amakolola za m'minda ya eniake,

amakunkha mphesa m'minda ya anthu oipa.

7Amagona maliseche usiku wonse,

pa nthaŵi yozizira amasoŵa chofunda.

8Amavumbwa ndi mvula yakumapiri,

amakangamira ku thanthwe chifukwa chosoŵa pousa.

9Palinso ena amene amatsomphola ana a masiye ku bele,

ndipo amagwira ana a mmphaŵi kuti akhale chikole.

10Amphaŵi amangoyenda maliseche kusoŵa chovala,

amasenza mitolo ya tirigu ali ndi njala.

11Amayenga mafuta a olivi m'minda ya anthu oipa,

namapsinya mphesa, koma nkumamvabe ludzu.

12Anthu amene alikufa akubuula mumzindamo,

anthu ovulala akulirira chithandizo.

Komabe Mulungu sakusamalako mapemphero ao.

13“Pali ena amene amakana kuŵala,

safuna kuyenda m'kuŵalako,

ndipo sadziŵa njira zake.

14Wopha anzake amadzuka usiku

kuti aphe osauka ndi amphaŵi.

Nthaŵi ya usiku ena amasanduka mbala.

15Munthu wachigololo amadikira chisisira,

namanena kuti, ‘Palibe woti angandiwone,’

ndipo amadzizimbaitsa nkhope.

16Mbala zimathyola nyumba usiku,

masana zimadzitsekera,

ndiye kuti zimapewa kuŵala.

17Onsewo kukada kwambiri, ndiye kuti kwaŵachera.

Zoopsa za mdima woti goo ndiye bwenzi lao.

18“Munthu woipa amatengedwa ndi madzi a chigumula.

Minda yake njotembereredwa m'dziko lonse.

Sapitako kukagwira ntchito ku minda yake yamphesa.

19Monga momwe amasungunukira matalala nkuloŵa pansi

chifukwa cha fundira, ndimo m'mene munthu wochimwa

adzatsikire ku dziko la akufa.

20Ngakhale mai wake adzamuiŵala,

koma mphutsi zidzasangalala pomudya.

Momwemonso woipayo adzathyoka ngati mtengo.

21“Zidzatero chifukwa choti adaŵachita nkhanza

akazi amasiye, akazi opanda ana sadaŵachite zabwino.

22Koma Mulungu amaononga anthu amphamvu.

Anthuwo ngakhale atakhazikika,

moyo wao ndi wosatsimikizika.

23Mulungu angathe kumtchinjiriza

munthu woipa ndi kumpatsa mtendere,

koma amakhala akupenyetsetsa njira zake.

24Woipayo amamkweza pa kanthaŵi kochepa,

koma posachedwa saonekanso.

Monga ena onse nayenso amafota ngati udzu,

amagwa ngati ngala za tirigu akazidula.

25Ndani angathe kukana kuti si momwemo?

Kodi wina anganditsutse kuti mau angaŵa si oona?”

Bilidadi

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help