Num. 27 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ana aakazi a Zelofehadi

1Nthaŵi imeneyo kudabwera ana aakazi a Zelofehadi. Iyeyo anali mwana wa Hefere, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, a m'mabanja a Manase mwana wa Yosefe. Ana ake aakaziwo anali aŵa: Mala, Nowa, Hogola, Milika ndi Tiriza.

2Iwoŵa adakaima pamaso pa Mose, pa wansembe Eleazara, pa atsogoleri, ndiponso pamaso pa mpingo wonse, pakhomo pa chihema chamsonkhano, nati,

3“Bambo wathu adafera m'chipululu. Iyeyo sanali nao m'gulu la anthu aja amene adasonkhana pamodzi ndi Kora naukira Chauta, iye adafera tchimo lake, koma analibe ana aamuna.

4Kodi dzina la bambo wathu life chifukwa choti analibe mwana wamwamuna? Mutipatse choloŵa chathu pakati pa abale a bambo wathu.”

5Mose adapita ndi mlandu umenewu pamaso pa Chauta.

6Tsono Chauta adauza Mose kuti,

7Num. 36.2“Ana aakazi a Zelofehadiwo akunena zoona. Uŵapatse choloŵa chao pakati pa abale a bambo wao. Uŵapatse choloŵa cha bambo waocho kuti chikhale chao.

8Ndipo uŵauze Aisraele kuti, ‘Munthu akafa opanda mwana wamwamuna, choloŵa chake chikhale cha mwana wake wamkazi.

9Akakhala kuti alibe mwana wamkazi, choloŵa chakecho chikhale cha abale ake.

10Akakhala kuti alibe abale, choloŵa chakecho chikhale cha abale a bambo wake.

11Bambo wakeyo akakhala wopanda abale, choloŵa chakecho upatse wachibale wake pabanja pakepo, ndipo chidzakhala chake. Ameneŵa akhale malamulo ndi malangizo kwa Aisraele, monga momwe Chauta adaalamulira Mose.’ ”

Mulungu asankha Yoswa kuti aloŵe m'malo mwa Mose(Deut. 31.1-8)

12 Deut. 3.23-27; 32.48-52 Chauta adauza Mose kuti, “Ukwere phiri ili la Abarimu, kuti uwone dziko limene ndapatsa Aisraele.

13Ndipo utaliwona, udzamwalira monga momwe adachitira Aroni mbale wako,

14chifukwa simudamvere mau anga m'chipululu cha Zini pa nthaŵi imene mpingo udandiwukira ku madzi a Meriba, pamene simudaonetse kuyera kwanga pamaso pao.” (Ameneŵa ndiwo madzi a kasupe wa ku Meriba ku Kadesi, m'chipululu cha Zini.)

15Mose adapempha Chauta kuti,

16“Inu Chauta, mwini mpweya wopatsa moyo anthu onse, musankhe munthu kuti aziyang'anira mpingowu.

171Maf. 22.17; Ezek. 34.5; Mt. 9.36; Mk. 6.34 Munthuyo aziŵatsogolera pa nkhondo ndi kuŵalamula, kuti mpingo wanu usamakhale ngati nkhosa zopanda mbusa.”

18Eks. 24.13 Apo Chauta adauza Mose kuti, “Tenga Yoswa mwana wa Nuni, munthu amene mzimu wa Mulungu uli mwa iye, ndipo umsanjike manja.

19Umuimiritse pamaso pa wansembe Eleazara ndi pamaso pa mpingo wonse, tsono umlonge m'malo mwako, iwo akupenya.

20Umpatseko udindo wako, kuti mpingo wonse wa Aisraele uzimumvera.

21Eks. 28.30; 1Sam. 14.41; 28.6 Tsono adzapite kwa wansembe Eleazara amene adzamdziŵitse zimene Chauta akufuna, pofunsa kwa Urimu ndi Tumimu. Umotu ndi m'mene Iyeyu adzatsogolere ndi kulamula Yoswa ndi mpingo wonse wa Aisraele.”

22Mose adachitadi monga momwe Chauta adamlamulira. Adamtengadi Yoswa namuimiritsa pamaso pa wansembe Eleazara ndi pamaso pa mpingo wonse.

23Deut. 31.23 Ndipo adamsanjika manja, nampatsa udindo monga momwe Chauta adamlangizira kudzera mwa Mose.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help