Yes. 20 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chizindikiro cha mneneri wamaliseche

1Chaka china mtsogoleri wankhondo wotumidwa ndi Sarigoni, mfumu ya ku Asiriya, adaadzalimbana ndi mzinda wa Asidodi, naulanda.

2Nthaŵi imeneyo nkuti Chauta atalankhula kale kudzera mwa Yesaya mwana wa Amozi. Adaanena kuti, “Pita ukavule chiguduli m'chiwuno mwako ndi nsapato kuphazi kwako.” Ndipo iyeyo adaachitadi zimenezo. Ankangoyenda maliseche ndiponso opanda nsapato.

3Tsono mzinda wa Asidodi uja utalandidwa, Chauta adati, “Yesaya mtumiki wanga wakhala akuyenda maliseche ndiponso opanda nsapato zaka zitatu zapitazi. Chimenechi chakhala chizindikiro kwa Aejipito ndi Aetiopiya cholosera zimene zilikudza.

4Ndimo m'mene mfumu ya ku Asiriya idzachitire: idzatenga akapolo a ku Ejipito ndi opirikitsidwa ku Etiopiya, anyamata ndi okalamba, nidzaŵayendetsa ali maliseche ndi opanda nsapato, matako ao ali pamtunda. Zimenezi zidzachititsa manyazi Aejipitowo.

5Tsono onse amene ankadalira dziko la Etiopiya ndiponso amene ankakhulupirira Ejipito, adzamva chisoni ndi kuchita manyazi.

6Tsiku limenelo anthu okhala m'mphepete mwa nyanja adzati, ‘Onanitu zimene zachitikira anthu aja tinkaŵakhulupiriraŵa, amene tinkathaŵirako kuti atithandize ndi kutipulumutsa kwa mfumu ya ku Asiriya! Ha! Tsopano tonsefe tidzapulumuka bwanji?’ ”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help