1Ine ndidati,
“Imvani inu akuluakulu a Yakobe,
olamulira a banja la Israele!
Kodi oyenera kudziŵa chilungamo sindinu?
2Mumadana ndi zabwino, mumakonda zoipa.
Anthu anga mumaŵasenda amoyo,
ndi kukangadzula mnofu wao.
3Mumandidyera anthu anga,
mumachita ngati kumaŵasenda,
kuphwanya mafupa ao,
ndi kumaŵachekera mumphika ngati nyama.
4“Nthaŵi ikubwera pamene mudzalira kwa Chauta,
koma sadzakuyankhani.
Nthaŵi imeneyo adzakufulatirani
chifukwa ntchito zanu nzoipa.”
5Zimene akunena Chauta ndi izi:
“Pali aneneri amene amasokeza anthu anga:
amamlosera za mtendere amene amaŵadyetsa,
koma amamlosera nkhondo amene alibe choŵapatsa.”
6Ndiye Chauta akuti,
“Nchifukwa chake simudzaonanso zinthu m'masomphenya,
simudzalosanso konse.
Inu aneneri, kwakuderani, mdima wakugwerani.”
7Alauli adzaŵanyazitsa,
oombeza maula adzaŵachititsa manyazi.
Onse adzangoti pakamwa gwirire,
chifukwa Mulungu sakuŵayankha.
8Koma ine Chauta wandidzaza ndi mphamvu,
wandidzaza ndi mzimu wake.
Wandidzaza ndi kulungama ndi kulimba mtima,
kuti ndidzudzule a banja la Yakobe
chifukwa cha zolakwa zao,
kuti ndiwonetse Aisraele zoipa zao.
9Imvani izi inu atsogoleri a banja la Yakobe,
inu olamulira a banja la Israele.
Inu mumadana ndi chilungamo,
mumakhotetsa zinthu zokhoza.
10Mumamanga Ziyoni ndi chuma chochipata
pakupha anthu,
Yerusalemu mumammanga ndi kuipa kwanu.
11Atsogoleri ake saweruza popanda chiphuphu,
ansembe ake saphunzitsa popanda malipiro,
aneneri ake salosa popanda ndalama.
Komabe amagonera pa Chauta ndi kunena kuti,
“Kodi suja Chauta ali pakati pathu?
Tsoka silingatigwere ai.”
12 Yer. 26.18 Tsono chifukwa cha inu
Ziyoni adzatipulidwa ngati munda,
Yerusalemu adzasanduka bwinja,
ndipo phiri la Nyumba ya Mulungu
lidzasanduka nkhalango.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.