1 Chiv. 21.2, 27 Dzuka, dzuka,
vala dzilimbe iwe Ziyoni.
Vala zovala zako zabwino,
iwe Yerusalemu, mzinda woyera.
Anthu osaumbalidwa ndi onyansa pa chipembedzo
sadzaloŵanso pa zipata zako.
2Udzisanse fumbi ndipo udzuke,
iwe Yerusalemu wogwidwa.
Inu omangidwa a ku Ziyoni,
aduleni maunyolo ali m'khosi mwanuwo.
3Chauta akunena kuti, “Sadalandirepo kanthu pokugulitsani, choncho mudzaomboledwa osaperekapo ndalama.
4Kale inu anthu anga mudaapita ku Ejipito kukakhala nao kumeneko, ndipo Aasiriya adaakuzunzani popanda chifukwa.
5Aro. 2.24 Tsono Ine Chauta ndikunena kuti, ‘Tsopano nditani poona kuti anthu anganu adakutengani ukapolo osaperekapo kanthu? Okulamulani akufuula monyodola, ndipo angokhalira kundinyoza kosalekeza.
6Pamenepo inu anthu anga mudzandidziŵa, nthaŵi imeneyo mudzadziŵa kuti ndine amene ndikulankhula. Ndithu ndinedi!’ ”
7 Nah. 1.15; Aro. 10.15; Aef. 6.15 Si kukondwetsa kwake
pamene mukuwona wamthenga akuyenda m'mapiri,
akubwera ndi uthenga wabwino,
akulengeza za mtendere,
akudzetsa chisangalalo,
akulengeza za chipulumutso,
akuuza anthu a ku Ziyoni kuti,
“Mulungu wanu ndi mfumu.”
8Mverani, alonda anu akukweza mau,
akuimba pamodzi mokondwa,
popeza kuti akuwona chamaso
Chauta akubweranso ku Ziyoni.
9Fuulani mokondwera inu mabwinja a Yerusalemu,
pakuti Chauta waŵatonthoza mtima anthu ake,
wapulumutsa Yerusalemu.
10Chauta wagwiritsa ntchito mphamvu
zake zoyera pamaso pa anthu a mitundu yonse,
dziko lonse lapansi mpaka ku mathero
lidzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.
11 2Ako. 6.17 Nyamukani, nyamukani,
chokaniko msanga ku Babiloniko,
musakhudze kanthu konyansa pa chipembedzo.
Tulukanimo ndipo mudziyeretse,
inu amene mukunyamula ziŵiya zopatulikira Chauta.
12Koma ulendo uno simudzachoka mofulumira,
simudzachita chothaŵa.
Chauta azidzayenda patsogolo panu,
Mulungu wa Aisraele azidzakutetezani kumbuyo kwanu.
Za mtumiki wozunzika wa Chauta13Chauta akuti,
“Mtumiki wanga adzapambana pa ntchito yake.
Adzakwezedwa ndi kulemekezedwa,
ndipo adzalandira ulemu waukulu kwambiri.
14Anthu ambiri atamuwona adadzidzimuka,
chifukwa nkhope yake inali itasakazika,
kotero kuti siinkachitanso ngati ya munthu.
Maonekedwe ake sanalinso ngati a munthu.
15 Aro. 15.21 Chimodzimodzinso anthu a mitundu yonse
adzadodoma naye,
Mafumu omwe adzasoŵa naye chonena,
popeza kuti zinthu zosaŵauzapo chiyambire adzaziwona,
ndipo zinthu zosamvapo nkale lonse, adzazimvetsa.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.