Eks. 31 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Antchito opanga chihema cha Chauta(Eks. 35.30—36.1)

1Pambuyo pake Chauta adapitirira kuuza Mose kuti,

2“Ndasankha Bezalele mwana wa Uri, mdzukulu wa Huri, wa fuko la Yuda.

3Iyeyu ndampatsa mzimu wanga, kotero kuti ali ndi luso ndi nzeru, ndipo akudziŵa bwino ntchito zonse zaluso monga izi:

4kulemba mapulani a ntchito zaluso ndi kugwira ntchito ndi golide, siliva ndi mkuŵa.

5Akudziŵanso kuzokota miyala yogwira nayo ntchito, kujoba mitengo, ndi kuchita zaluso zonse.

6Ndasankhanso Aholiyabu mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani. Ndipo anthu ena onse aluso ndaŵapatsa nzeru zambiri zoti athe kupanga chinthu chilichonse chimene ndingakulamule kuti iwoŵa apange.

7Apange chihema chamsonkhano Ine ndi anthu anga, bokosi lachipangano, chivundikiro cha bokosi, pamodzi ndi zipangizo za chihema,

8tebulo ndi zipangizo zake, choikaponyale cha golide wabwino kwambiri, pamodzi ndi zipangizo zake, guwa lofukizirapo lubani,

9guwa la zopereka zopsereza, pamodzi ndi zipangizo zake, beseni losambira ndi phaka lake,

10zovala zopatulika za wansembe Aroni ndi za ana ake, zomavala pa nthaŵi imene akutumikira,

11mafuta odzozera ndiponso lubani wa fungo lokoma, zonsezo zokhalira malo oyera. Adzapange zinthu zonsezi monga ndakulamulira iwe.”

Za tsiku lopumula

12Chauta adauzanso Mose kuti,

13“Uza Aisraele kuti, ‘Muzisunga Sabata, tsiku langa lopumula, chifukwa ndilo chizindikiro chamuyaya pakati pa Ine ndi inu ndi zidzukulu zanu, choonetsa kuti Ine ndine Chauta, amene ndimakuyeretsani.

14Motero muzisunga tsiku la Sabata, chifukwa ndi loyera kwa inu. Munthu aliyense wosalisunga, aphedwe. Aliyense wogwira ntchito pa tsiku limenelo adzachotsedwe pakati pa anthu anzake.

15Eks. 20.8-11; 23.12; 34.21; 35.2; Lev. 23.3; Deut. 5.12-14Munthu agwire ntchito zake zonse pa masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi tsiku la Sabata lopumula, tsiku loyera la Chauta. Aliyense wogwira ntchito pa tsiku limeneli aphedwe.

16Aisraele azisunga tsiku la Sabatalo, ndipo mibadwo yonse yakutsogoloko izidzalisunga ngati pangano losatha.

17Eks. 20.11 Chimenechi ndi chizindikiro chosatha pakati pa Ine ndi Aisraele, chakuti Ine Chauta ndidalenga kumwamba ndi dziko lapansi pa masiku asanu ndi limodzi, ndipo ndidapumula pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri.’ ”

18Chauta atatsiriza kulankhula ndi Mose pa phiri la Sinai lija, adampatsa Moseyo miyala iŵiri yaumboni, imene Mulungu mwini anali atalembapo kale.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help