Yos. 13 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Maiko otsala oyenera kulandidwa.

1Nthaŵi imeneyo Yoswa anali atakalamba kwambiri. Tsono Chauta adamuuza kuti, “Tsopanotu iwe wakalamba kwambiri, koma dziko losalandidwa likalipo lalikulu.

2Maiko amene atsalako ndi aŵa: dziko lonse la Afilisti, ndi dziko lonse la Gesuri,

3(dziko limene layambira ku mtsinje wa Sihori kuvuma kwa Ejipito mpaka ku malire a Ekeroni, lonselo lili m'manja mwa Akanani. Olamulira dziko la Afilisti akukhala ku Gaza, ku Asidodi, ku Asikeloni, ku Gati ndi ku Ekeroni), ndiponso dziko la Avimu chakumwera.

4Palinso dziko la Akanani ndi la Meala, lomwe lili m'manja mwa Asidoni mpaka ku Afeki, malo amene ali pafupi ndi malire a Aamori.

5Palinso dziko lonse la Gebala ndi la Lebanoni chakuvuma, kuchokera ku Balagadi patsinde pa phiri la Heremoni mpaka ku Hamatipasi.

6Num. 33.54 Palinso dziko la Asidoni, amene akukhala m'dera lamapiri, pakati pa phiri la Lebanoni ndi la Misirefoti-Maimu. Anthu onsewo Ine Mulungu ndidzaŵapirikitsa m'mene Aisraele azikafika. Uŵagaŵire Aisraele maiko ameneŵa kuti akhale choloŵa chao, potsata zomwe ndakulamula.

7Tsono ugaŵe maiko ameneŵa pakati pa mafuko asanu ndi anai ndi theka lina lija la fuko la Manase, kuti akhale choloŵa chao.”

Maiko opatsidwa kwa Manase, Rubeni ndi Gadi.

8 Num. 32.33; Deut. 3.12 Anthu a fuko la Rubeni ndi la Gadi ndiponso theka lina lija la fuko la Manase adalandira dziko lao cha kuvuma kwa Yordani. Dziko limeneli ndilo lija adaŵapatsa Mose mtumiki wa Chauta.

9Dziko laolo lidayambira ku Aroere, mzinda umene uli pafupi ndi chigwa cha Arinoni, ndiponso ku mzinda wokhala pakati pa chigwacho. Dzikolo linkaphatikiza dera lonse lokwera kuyambira ku Medeba kukafika ku Diboni.

10Linkaphatikizaponso mizinda yonse yomwe inkalamulidwa ndi Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankalamula ku Hesiboni, mpaka ku malire a Aamoni.

11Lidaphatikizaponso Giliyadi ndi dziko limene Agesuri ndi Amakati ankakhalamo, kudzanso phiri lonse la Heremoni, pamodzi ndi Basani, mpaka ku Saleka.

12Ndipo ku Basani lidaphatikizapo dziko la Ogi amene ankalamula ku Asitaroti ndi ku Ederei. (Ogi anali yekhayo mfumu ya Arefaimu amene adatsalako). Mose anali atagonjetseratu anthu ameneŵa ndi kuŵapirikitsira kutali.

13Koma Aisraele sadapirikitse Agesuri ndi Amakati. Anthu ameneŵa akadalipo pakati pa Aisraele.

14 Deut. 18.1 Komabe Mose sadapereke dziko kwa fuko la Levi. Zimene ankalandira iwowo ngati choloŵa chao ndi gawo la zopereka zopsereza zimene anthu ankapereka kwa Chauta, monga momwe Chauta adaauzira Mose.

Dziko la fuko la Rubeni.

15Mose adapereka gawo lina la dziko kwa mabanja a fuko la Rubeni kuti likhale choloŵa chao.

16Dziko laolo lidayambira ku Aroere, mzinda umene uli pafupi ndi chigwa cha Arinoni, ndiponso mzinda wokhala pakati pa chigwacho, ndiponso dera lonse lokwera kuyambira ku Medeba,

17kuphatikizapo Hesiboni, pamodzi ndi mizinda yonse ya ku chigwa monga: Diboni, Bamoti-Baala, Bete-Baala-Meyani,

18Yahazi, Kedemoti, Mefaati,

19Keriyataimu, Sibima, Zeretisahara pa phiri la m'chigwa,

20Betepeori, matsitso onse a phiri la Pisiga ndi Beteyesimoti.

21Imeneyi ndiyo mizinda yonse yakuchigwa, mizinda yonse ya Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankalamulira ku Hesiboni. Mose anali atagonjetsa Sihoni pamodzi ndi onse olamulira ku Midiyani monga: Evi, Rekemu, Zeri, Huri ndi Reba. Onseŵa ankalamulira dzikolo ngati anyakwaŵa a Sihoni.

22Pakati pa ophedwa ndi Aisraele panali Balamu, mwana wa Beori, wolosa zakutsogolo uja.

23Mtsinje wa Yordani ndiwo unali malire a fuko la Rubeni. Mizinda imeneyo pamodzi ndi midzi yake ndi imene idapatsidwa kwa mabanja a fuko la Rubeni, kuti ikhale choloŵa chao.

Dziko la fuko la Gadi.

24Gawo lina la dzikolo, Mose adalipatsa mabanja a fuko la Gadi, kuti likhale choloŵa chao.

25Dziko laolo lidaphatikiza Yazere pamodzi ndi mizinda ya Giliyadi, hafu lonse la dziko la Aamoni mpaka ku Aroere, kuvuma kwa Raba.

26Lidayambira ku Hesiboni mpaka ku Ramati-Mizipe ndi Betonimu, kuchokeranso ku Mahanaimu mpaka ku malire a Lodebara.

27M'chigwa cha Yordani adalandiramo Beteharamu, Betenimura, Sukoti ndi Safoni, kudzanso theka la dziko la Sihoni, mfumu ya ku Hesiboni. Malire ake akuzambwe anali mtsinje wa Yordani kufikira ku nyanja ya Galilea chakumpoto.

28Mizinda imeneyi, pamodzi ndi midzi yake, ndiyo imene idapatsidwa kwa mabanja a fuko la Gadi, kuti ikhale choloŵa chao.

Dziko la fuko la Manase kuvuma.

29Mose anali atapereka kale gawo lina la dziko kwa mabanja a theka la fuko la Manase lija, kuti likhale choloŵa chao.

30Dzikolo lidayambira ku Mahanaimu kuphatikizapo dziko lonse la mfumu Ogi, mfumu ya ku Basani, pamodzi ndi midzi 60 ya ku Yairo, ku Basaniko.

31Lidaphatikizaponso theka la Giliyadi, pamodzi ndi Asitaroti ndi Ederei, mizinda yaikulu ya mfumu Ogi wa ku Basani. Mizinda imeneyi idapatsidwa kwa mabanja a Makiri mwana wa Manase, kuti ikhale choloŵa cha hafu la Amakiri malinga ndi mabanja ao.

32Umu ndimo m'mene Mose adagaŵira dziko la m'zigwa za Mowabu, kuvuma kwa Yeriko, kutsidya kwa Yordani.

33Num. 18.20; Deut. 18.2 Komatu Mose sadaŵapatse dziko a fuko la Levi. Mose adaŵauza Aleviwo kuti choloŵa chao ndi gawo la zopereka zimene anthu ankapereka ngati nsembe zopsereza kwa Chauta, monga momwe Chautayo adaauzira Mose.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help