1Khoma la mzinda lija litamangidwa, ndidaikira zitseko, ndipo alonda a ku Nyumba ya Mulungu, anthu oimba nyimbo ndiponso Alevi adasankhidwa.
2Pamenepo ndidasankha mbale wanga Hanani ndi Hananiya, mkulu woyang'anira linga lankhondo, kuti aŵiriwo azilamulira Yerusalemu. Hananiyayo anali munthu wokhulupirika ndi womvera Mulungu kupambana anthu ambiri.
3Tsono ndidaŵauza kuti, “Musalole kuti atsekule zipata za Yerusalemu mpaka dzuŵa litatentha. Ndipo atseke zitseko ndi kuzipiringidza, alonda asanaŵeruke. Musankhe olonda pakati pa anthu okhala m'Yerusalemu, aliyense akhale pamalo pake, ndiponso akhale poyang'anana ndi nyumba yake.”
Mndandanda wa anthu obwerako ku ukapolo(Eza. 2.1-20)4Mzinda wa Yerusalemu unali wotambasuka ndiponso waukulu, koma anthu okhala mumzindamo anali oŵerengeka, ndipo munalibe nyumba zambiri.
5Tsono Mulungu adaika mumtima mwanga maganizo oti ndisonkhanitse atsogoleri, akuluakulu ndiponso anthu onse, kuti alembedwe potsata mibadwo ya mabanja ao. Ndidapeza buku m'mene mudalembedwa maina a mabanja a anthu amene anali oyamba kubwerako ku ukapolo. Zolembedwa m'menemo zinali izi:
6Naŵa anthu a m'chigawo cha Yuda amene adabwerako ku ukapolo, omwe Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adaaŵagwira kupita nawo ku Babiloni. Anthuwo adabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wa makolo ake.
7Adabwera pamodzi ndi atsogoleri aŵa: Zerubabele, Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu ndi Baana.
Nachi chiŵerengero cha anthu aamuna a Aisraele.
8A banja la Parosi 2,172.
9A banja la Sefatiya 372.
10A banja la Ara 652.
11A banja la Pahatimowabu, ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa ndi Yowabu 2,818.
12A banja la Elamu 1,254.
13A banja la Zatu 845.
14A banja la Zakai 760.
15A banja la Binuyi 648.
16A banja la Bebai 628.
17A banja la Azigadi 2,322.
18A banja la Adonikamu 667.
19A banja la Bigivai 2,067.
20A banja la Adini 655.
21A banja la Atere, ndiye kuti la Hezekiya, 98.
22A banja la Hasumu 328.
23A banja la Bezai 324.
24A banja la Harifi 112.
25A banja la Gibiyoni 95.
26Amuna a ku Betelehemu ndi a ku Netofa 188.
27Amuna a ku Anatoti 128.
28Amuna a ku Betazimaveti 42.
29Amuna a ku Kiriyati-Yearimu, Kefira, ndi Beeroti 743.
30Amuna a ku Rama ndi Geba, 621.
31Amuna a ku Mikimasi 122.
32Amuna a ku Betele ndi Ai 123.
33Amuna a ku Nebo wina 52.
34A banja la Elamu wina 1,254.
35A banja la Harimu 320.
36A ku Yeriko 345.
37A ku Lodi, Hadidi ndi Ono 721.
38A ku Senaya 3,930.
39Ansembe anali aŵa: a banja la Yedaya, ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa, 973.
40A banja la Imara 1,052.
41A banja la Pasuri 1,247.
42A banja la Harimu 1,017.
43Alevi anali aŵa: a banja la Yesuwa ndi la Kadimiyele, ndiye kuti zidzukulu za Hodaviya, 74.
44Oimba nyimbo anali aŵa: a banja la Asafu 148.
45Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali aŵa: a banja la Salumu, a banja la Atere, a banja la Talimoni, a banja la Akubu, a banja la Hatita, a banja la Sobai, onse pamodzi 138.
46Antchito a ku Nyumba ya Mulungu anali aŵa: a banja la Ziha, a banja la Hasufa, a banja la Tabaoti,
47a banja la Kerosi, a banja la Siya, a banja la Padoni,
48a banja la Lebana, a banja la Hagaba, a banja la Salimai,
49a banja la Hanani, a banja la Gidele, a banja la Gahara,
50a banja la Reaya, a banja la Rezini, a banja la Nekoda,
51a banja la Gazamu, a banja la Uza, a banja la Paseya,
52a banja la Besai, a banja la Meunimu, a banja la Nefusesimu,
53a banja la Bakibuki, a banja la Hakufa, a banja la Harihuri,
54a banja la Baziliti, a banja la Mehida, a banja la Harisa,
55a banja la Barikosi, a banja la Sisera, a banja la Tema,
56a banja la Neziya, a banja la Hatifa.
57Mabanja a antchito ake a Solomoni anali aŵa: a banja la Sotai, a banja la Sofereti, a banja la Perida,
58a banja la Yaala, a banja la Darikoni, a banja la Gidele,
59a banja la Sefatiya, a banja la Hatili, a banja la Pokereti-Hazebaimu ndi a banja la Amoni.
60Antchito onse a ku Nyumba ya Mulungu, kuphatikizapo zidzukulu za antchito a Solomoni, onse pamodzi analipo 392.
61Anthu ali m'munsiŵa ndiwo amene adabwera kuchokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adoni ndi ku Imeri, ngakhale sankatha kutsimikiza kuti makolo ao kapena mafuko ao analidi Aisraele enieni kapena ai.
62A banja la Delaya, a banja la Tobiya, a banja la Nekoda 642.
63Ndiponso ena mwa ansembe anali aŵa: a banja la Hobaya, a banja la Hakozi, a banja la Barizilai (kunena amene adaakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Barizilai wa ku Giliyadi, nkutenga dzina la bambo waoyo).
64Iwoŵa adaafunafuna maina ao m'buku lolongosola kaundula wa mafuko ao, koma maina ao sadapezekemo. Choncho adaŵachotsa pa unsembe naŵaŵerenga kuti ngodetsedwa pa chipembedzo.
65Eks. 28.30; Deut. 33.8Bwanamkubwa adaŵauza anthuwo kuti asamadye nawo chakudya choperekedwa kwa Mulungu, mpaka wansembe wodziŵa kuwombeza ndi Urimu ndi Tumimu atapezeka.
66Chiŵerengero cha anthu onse obwerako ku ukapolo aja chinali 42,360.
67Kuwonjezera pamenepa, panalinso antchito ao aamuna ndi aakazi okwanira 7,337. Anali nawonso anthu oimba nyimbo, amuna ndi akazi omwe, okwanira 245.
68Akavalo ao analipo 736, nyulu zao zinalipo 245,
69ngamira zao zinalipo 435, ndipo abulu ao analipo 6,720.
70Atsogoleri ena a mabanja adapereka mphatso zothandizira ntchito. Bwanamkubwa adapereka ku thumba la chuma ndalama zagolide za makilogaramu asanu ndi atatu, mbale makumi asanu, ndiponso mikanjo ya ansembe yokwanira 530.
71Atsogoleri ena a mabanja adapereka mosungira chumamo ndalama zagolide za makilogaramu 168, ndiponso ndalama zasiliva za makilogaramu 1,250.
72Ndipo anthu onse otsala adapereka ndalama zagolide za makilogaramu 168, ndalama zasiliva zamakilogaramu 140, ndiponso mikanjo ya ansembe yokwanira 67.
73 1Mbi. 9.2; Neh. 11.3 Motero ansembe, Alevi, alonda a ku Nyumba ya Mulungu, anthu oimba nyimbo, ambiri mwa anthu wamba, atumiki a m'Nyumba ya Mulungu ndi Aisraele ena onse, ankakhala m'mizinda mwao.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.